Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 95

Kuwala Kukuwonjezerekabe

Kuwala Kukuwonjezerekabe

(Miyambo 4:18)

  1. 1. Aneneri akale ankafuna

    Kudziwa za Yesu Mesiya.

    Mzimu wa M’lungu unaneneratu

    Kuti adzatipulumutsa.

    Nthawi yakwana akulamulira.

    Umboni wake ulipo.

    Kudziwa zimenezi ndi mwayi

    Waukulu womwe tili nawo.

    (KOLASI)

    Kuwala kwa panjira yathu

    Kukuwonjezerekabe.

    Zomwe M’lungu akuulula

    Zimatitsogoleradi.

  2. 2. Ambuye wathu wasankha kapolo

    Amene akumatidyetsa.

    Kuwala kwa choonadi panopa

    Kukungowonjezerekabe.

    Pano tikuyenda molimba mtima,

    Tikumayenda mowala.

    Tikuthokoza Yehova chifukwa

    Watipatsa choonadichi.

    (KOLASI)

    Kuwala kwa panjira yathu

    Kukuwonjezerekabe.

    Zomwe M’lungu akuulula

    Zimatitsogoleradi.