NYIMBO 97
Moyo Umadalila Mau a Mulungu
-
1. Moyo wathu ‘madalila
Mau a Yehova.
Zonse iye ananena
Zitipindulitsa.
Timakhala na mtendele,
Timadalitsidwa.
(KOLASI)
Moyo umadaliladi;
Mau a Mulungu.
Ngati ‘se tiwatsatila;
Tidzadalitsidwa.
-
2. M’Mau a Mulungu wathu
Tipeza zitsanzo,
Za amuna ndi akazi,
Okhulupilika.
Tikaŵelenga za iwo
Tilimbikitsidwa.
(KOLASI)
Moyo umadaliladi;
Mau a Mulungu.
Ngati ‘se tiwatsatila;
Tidzadalitsidwa.
-
3. Mwa Mau ake Yehova
Amatithandiza.
Kukhala anthu olimba
Olo tivutike.
Mayeselo akabwela
Amatitonthoza.
(KOLASI)
Moyo umadaliladi;
Mau a Mulungu.
Ngati ‘se tiwatsatila;
Tidzadalitsidwa.
(Onaninso Yos. 1:8; Aroma 15:4.)