Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 99

Abale Ambirimbiri

Abale Ambirimbiri

(Chivumbulutso 7:​9, 10)

  1. 1. Abale ambirimbiri.

    Inde ochuluka.

    Aliyense ndi mboni

    Yokhulupirika.

    Tilipodi ambiri.

    Tikuchulukabe.

    Tachokera m’mayiko onse

    Ndi mitundu yonse.

  2. 2. Abale ambirimbiri.

    Timalalikira

    Uthenga wabwinowu

    Kwa ofuna kumva.

    Pamene tafooka

    Yesu atipatsa

    Mpumulo ndi mphamvu zambiri.

    Sitimada nkhawa.

  3. 3. Abale ambirimbiri.

    Timatetezedwa

    Potumikira M’lungu

    Padziko lapansi.

    Tilipodi ambiri.

    Timalalikira.

    Timagwira ntchito ndi M’lungu

    Pomutumikira.