Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 100

Alandileni na Manja Aŵili

Alandileni na Manja Aŵili

(Machitidwe 17:7)

  1. 1. Yehova amatilandila bwino.

    Amasamalila mosakondela.

    Mvula imagwabe,

    dzuŵa imawala;

    Amatipatsanso cakudya.

    Pamene tithandiza ovutika,

    Timatengela citsanzo ca M’lungu.

    Ngati tionetsa

    cifundo kwa ena,

    Yehova adzatidalitsa.

  2. 2. Pothandiza ena sitingadziŵe

    Zabwino zimene tingalandile.

    Ngakhale amene

    sitimaŵadziŵa

    Tifunika kuŵathandiza.

    Monga Lidiya tiziŵalandila,

    Akabwela tiziŵatsitsimula.

    Atate Yehova

    amaona onse

    Ocitila ena cifundo.

(Onaninso Mac. 16:14, 15; Aroma 12:13; 1 Tim. 3:2; Aheb. 13:2; 1 Pet. 4:9.)