Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 102

“Muzithandiza Ofooka”

“Muzithandiza Ofooka”

(Machitidwe 20:35)

  1. 1. Tonse timavutika,

    Timafooka,

    Koma Mulungu wathu

    Amatikonda.

    Ali ndi chifundo

    Komanso chikondi.

    Nafe tikonde anthu,

    Tiwathandize.

  2. 2. Atumiki a M’lungu

    Angafooke.

    Tiziwalimbikitsa

    Ndi mawu athu.

    Mzimu wa Mulungu

    Umawalimbitsa.

    Tiziwadera nkhawa

    Tiwatonthoze.

  3. 3. M’malo mowaweruza

    Tikumbukire

    Kuti kukoma mtima

    N’kolimbikitsa.

    Tizichita khama

    Powalimbikitsa.

    Tikamawathandiza

    Amamva bwino.