Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 106

Tikulitse Khalidwe la Chikondi

Tikulitse Khalidwe la Chikondi

(1 Akorinto 13:​1-8)

  1. 1. Chonde Mulungu mutipatse

    Makhalidwe anu onsewo.

    Koma lofunika kwambiri

    N’chikondi chomwe muli nacho.

    Ngati tilibe chikondichi

    Maluso athu ndi achabe.

    Tizisonyezana chikondi

    M’zochita ndi muzolankhula.

  2. 2. Chikondi ndi chokoma mtima

    Sichimafuna zake zokha.

    Sichimasunganso zifukwa,

    Chimakhululukira ena.

    Mavuto angakule bwanji

    Chikondi chimapirirabe.

    Chikondi sichimagonjanso.

    Chidzakhalapo mpaka kale.