Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 106

Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi

Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi

(1 Akorinto 13:1-8)

  1. 1. Tithandizeni kuonetsa

    Makhalidwe anu abwino.

    Koposa zonse tionetse

    Cikondi kwa abale athu.

    Ngati cikondi cazilala,

    Inu Yehova simukondwa.

    Tionjezeleni cikondi,

    Nthawi zonse ticionetse.

  2. 2. Cikondi cimatipangitsa

    Kuti tiganizile ena.

    Tikhululukila anzathu,

    Monga Yesu anakambila.

    Cikondi cimatithandiza

    Kupilila pamayeselo.

    Cikondi cipilila zonse

    Cikondi sicidzalephela.

(Onaninso Yoh. 21:17; 1 Akor. 13:13; Agal. 6:2.)