NYIMBO 106

Khalani Achikondi

Khalani Achikondi

(1 Akorinto 13:1-8)

  1. 1. M’lungu tikupempha m’tipatse,

    Makhalidwe anu onsewo.

    Koma lofunika koposa

    N’chikondi, mzimu ’matipatsa

    Tingakhaletu ndi maluso,

    Popanda chikondi n’ngachabe.

    Tisonyezanedi chikondi,

    M’zochita ndi muzolankhula.

  2. 2. Chikondi chimatithandiza

    Kuti tikhaledi opatsa.

    Sichimasunganso zifukwa,

    Chimakhululukira ena.

    Chikondi chimapiriranso,

    Mavuto angakule bwanji.

    Chikondi sichimagonjanso;

    Chidzakhala mpaka muyaya.