Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 108

Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu

Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu

(Yesaya 55:1-3)

  1. 1. M’lungu ndi chikondi.

    Amatikonda kwambiri.

    Anaperekatu Yesu

    Kuwombola anthu onse,

    Ndipo tikudikirira

    Moyo wosangalatsadi.

    (KOLASI)

    Inu nonse a ludzu

    Dzamweni kwaulere

    Madzi opatsa moyo.

    M’lungu ndi chikondi.

  2. 2. M’lungu ndi chikondi.

    Ntchito zake ndi umboni.

    Anasonyeza chikondi

    Popatsa Yesu Ufumu.

    Ufumu wake tsopano

    Wayamba kulamulira.

    (KOLASI)

    Inu nonse a ludzu

    Dzamweni kwaulere

    Madzi opatsa moyo.

    M’lungu ndi chikondi.

  3. 3. M’lungu ndi chikondi.

    Nafenso tichisonyeze.

    Tiphunzitse anthu onse

    Malamulo a Mulungu.

    Timamvera M’lungu wathu

    Polalikira konseko.

    (KOLASI)

    Inu nonse a ludzu

    Dzamweni kwaulere

    Madzi opatsa moyo.

    M’lungu ndi chikondi.