Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 111

Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

(Mateyu 5:12)

  1. 1. Tili ndi zifukwa zambiri

    Zakuti tisangalale.

    Anthu okondedwa ndi M’lungu

    Akusangalala nafe.

    Timasangalala chifukwa

    Timadziwa Mawu ake.

    Timawaphunzira mwakhama

    Ndipo amatilimbitsa.

    Zotisangalatsa n’zambiri,

    Zikuyaka mumtimamu.

    Tikakumana ndi mavuto

    M’lungu amatithandiza.

    (KOLASI)

    Yehova Mulungu wathu

    Amatipatsa chimwemwe.

    Ndi wabwinodi, ntchito zakenso,

    N’zazikulu ndi zamphamvu.

  2. 2. Timasangalala kuona

    Kumwamba, nyanja ndi dziko.

    Yehova analenga zonse

    Ife timamuthokoza.

    Timachitiradi umboni

    Ndi kulengeza uthenga.

    Timalalikira kwa onse

    Madalitso a Ufumu.

    Kusangalala sikudzatha

    Mu dziko latsopanolo.

    Zimene anatilonjeza

    Tidzasangalala nazo.

    (KOLASI)

    Yehova Mulungu wathu

    Amatipatsa chimwemwe.

    Ndi wabwinodi, ntchito zakenso,

    N’zazikulu ndi zamphamvu.