Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 111

Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

(Mateyu 5:12)

  1. 1. Zimene zitisangalatsa

    Lelo zilipo zambili.

    Mitundu ya anthu ibwela

    Kudzalambila Yehova.

    Tsiku na tsiku tiphunzila

    Mau a Mulungu wathu.

    Ndipo timakhulupilila

    Zimene timaphunzila.

    Monga moto mitima yathu

    Imayaka na cimwemwe.

    Olo ise timavutika

    Yehova ‘matithandiza.

    (KOLASI)

    Yehova Mulungu wathu

    Ndiyedi cimwemwe cathu.

    Ubwino wake na mphamvu zake

    Zimatisangalatsadi!

  2. 2. Timakondwela tikaona

    Kumwamba, nyanja na mtunda.

    Zonse Yehova analenga

    Zimamutamanda iye.

    Mokondwa ise tilengeza

    Za Ufumu wa Mulungu.

    Tilalikila konse-konse

    Kuti Khristu’a lamulila.

    Dziko latsopano lafika

    Tiyeni tisangalale.

    Tidzalandila madalitso

    Na cimwemwe camuyaya.

    (KOLASI)

    Yehova Mulungu wathu

    Ndiyedi cimwemwe cathu.

    Ubwino wake na mphamvu zake

    Zimatisangalatsadi!

(Onaninso Deut. 16:15; Yes. 12:6; Yoh. 15:11.)