NYIMBO 111

Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

(Mateyu 5:12)

  1. 1. Tili ndi zifukwa zambiri,

    Zakuti tisangalale.

    Anthu a mumitundu yonse

    Akusangalala nafe.

    Chisangalalo n’chachikulu,

    Mawu a M’lungu tidziwa.

    Timawaphunzira mwakhama;

    Amatilimbikitsadi.

    Zotisangalatsa n’zambiri,

    Mumtimamu zikuyaka.

    Tikakumana ndi mavuto,

    Yehova amathandiza.

    (KOLASI)

    Amatisangalatsadi,

    Yehova Mulungu wathu.

    Ndi wabwinodi ndi ntchito zake,

    N’zazikulu ndi zamphamvu.

  2. 2. Timasangalala kuona,

    Kumwamba, nyanja ndi dziko.

    Yehova analenga zonse,

    Ife timayamikira.

    Timachitiratu umboni,

    Ndi kulengeza Ufumu.

    Madalitso a Ufumuwo,

    Tilengeza kulikonse.

    Kusangalala kwamuyaya,

    Kwayandikira tsopano.

    Zimene anatilonjeza

    Tidzasangalala nazo.

    (KOLASI)

    Amatisangalatsadi,

    Yehova Mulungu wathu.

    Ndi wabwinodi ndi ntchito zake,

    N’zazikulu ndi zamphamvu.