Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 116

Mphamvu ya Kukoma Mtima

Mphamvu ya Kukoma Mtima

(Aefeso 4:32)

  1. 1. Tiyamikila imwe Yehova,

    M’lungu wacikondi.

    Ngakhale kuti muli na mphamvu

    Ndimwedi wokoma mtima.

  2. 2. Mwana wanu Yesu aitana

    Onse ovutika,

    Kuti iwo abwele kwa iye,

    Ndipo adzatonthozedwa.

  3. 3. Tikhale ngati M’lungu na Yesu,

    Mu zocita zathu.

    Ngati tikhala okoma mtima,

    Tidzakhaladi amphamvu.

(Onaninso Mika 6:8; Mat. 11:28-30; Akol. 3:12; 1 Pet. 2:3.)