Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 117

Ubwino

Ubwino

(2 Mbiri 6:41)

  1. 1. O Yehova M’lungu wathu,

    Ise mwatidalitsa.

    Ndinu wokhulupilika

    Wabwino m’zinthu zonse.

    Mwationetsa cifundo

    Cifukwa mutikonda.

    Tidzakutumikilani

    Nakukulambilani.

  2. 2. Tiona ubwino wanu

    Mwa anthu munasankha.

    Amalengeza uthenga

    Na kucita zabwino.

    Mwa akulu a mumpingo,

    Tipita patsogolo.

    Tipatseni mzimu wanu

    Tionetse ubwino.

  3. 3. Kwa abale athu onse,

    Tionetse ubwino.

    Tipempha mutithandize

    Kukonda athu onse.

    Ku mipingo na mabanja,

    Ndi kwa anansi athu,

    Tipempha thandizo lanu,

    Tionetse ubwino.

(Onaninso Sal. 103:10; Maliko 10:18; Agal. 5:22; Aef. 5:9.)