NYIMBO 117

Khalidwe la Ubwino

Khalidwe la Ubwino

(2 Mbiri 6:41)

  1. 1. Yehova M’lungu wabwino

    Mumatidalitsadi.

    Ndinu wokhulupirika,

    Mumachita zabwino.

    Mumasonyeza chifundo

    Kwa anthu ochimwafe.

    Tilambire inu nokha.

    Tikutumikireni.

  2. 2. Taona ubwino wanu

    Mwa atumiki anu.

    Khalidwe lawo labwino

    Limatilimbikitsa.

    Mwatipatsa Mawu anu

    Ndi abusa abwino.

    Mutipatse mzimu wanu

    Tizichita zabwino.

  3. 3. Chonde muzitidalitsa

    Tikachita zabwino.

    Tikhale okoma mtima

    Kwa munthu aliyense.

    M’mabanja ndi mumipingo

    Ndiponso kulikonse,

    Muzitithandiza kuti

    Tizichita zabwino.