NYIMBO 124

Tizikhulupirika Nthawi Zonse

Tizikhulupirika Nthawi Zonse

(Salimo 18:25)

  1. 1. Tikhulupirike zedi,

    Kwa M’lungu ndi kum’konda.

    Malamulo ake onse,

    Tifuna kuwadziwa.

    Timapindula kwambiri,

    Tikamamvera iye.

    Ndi wokhulupirikadi,

    Ndipo sitingam’siye.

  2. 2. Tikhulupirike zedi,

    Kwa abale mumpingo.

    Nthawi zonse pamavuto,

    Amatisamalira.

    Tiziwalemekezatu

    Kuchokera mumtima.

    Tiwamvere nthawi zonse,

    Ndipo tisawasiye.

  3. 3. Tikhulupirike zedi

    Tikamalangizidwa.

    Ndi abale amumpingo,

    Tifunika kumvera.

    Ndipo Yehova Mulungu

    Adzatidalitsatu,

    Tikakhulupirikadi,

    Iye adzatikonda.