Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 125

“Osangalala Ndi Anthu Achifundo”

“Osangalala Ndi Anthu Achifundo”

(Mateyu 5:7)

  1. 1. Yehova ndi wachifundo,

    Amasonyeza chifundo.

    Iye ndi wokoma mtima.

    Amatisamaliradi.

    Amamvanso mapemphero

    Ochokera kwa olapa.

    Amadziwa ndife fumbi,

    Amatikomera mtima.

  2. 2. Tikachimwa n’kupemphera,

    M’lungu amakhululuka.

    Yesu anatiphunzitsa

    Mmene tingapempherere,

    Muzitikhululukira,

    Takhululukira ena.

    Tisasungenso zifukwa.

    Tidzapezadi mtendere.

  3. 3. Tikapatsa ena mphatso

    Tizisonyeza chifundo.

    Tisamafune kutchuka

    Koma kungowathandiza.

    M’lungu yemwe amaona

    Adzatibwezera ndithu.

    Anthu onse achifundo

    Mulungu amawakonda.

(Onaninso Mat. 6:​2-4, 12-14.)