Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 125

“Acifundo ni Acimwemwe!”

“Acifundo ni Acimwemwe!”

(Mateyu 5:7)

  1. 1. Yehova ni wacifundo,

    Ndipo ni wokoma mtima.

    Iye amasamalila

    Zonse zimene tifuna.

    Ocimwa ngati alapa,

    Amaŵakhululukila.

    Cifukwa iye adziŵa

    Kuti ‘se ndise ofooka.

  2. 2. Tikakhala na cifundo,

    M’lungu adzatidalitsa.

    Adzatikhululukila

    Ise pamene tilakwa.

    Yesu anatiphunzitsa

    Kufunika kwa cifundo.

    Tidzakhala na mtendele,

    Ngati timakhululuka.

  3. 3. Pamene tipatsa ena

    Mphatso zathu za cifundo.

    Ise tisadzitamande,

    Tikhale odzicepetsa.

    Anthu onse acifundo,

    Amakhala acimwemwe.

    Yehova amaŵakonda,

    Iye amaŵadalitsa.

(Onaninso Mat. 6:2-4, 12-14.)