NYIMBO 131

“Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”

“Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”

(Mateyu 19:5, 6)

  1. 1. Mulungu ndi anthu,

    Amva malonjezo.

    Chingwe cholimba bwino,

    Chamangidwa lero.

    (KOLASI 1)

    Mwamuna walonjeza

    Kukonda mkaziyu.

    “Chomwe M’lungu wamanga,

    Musalekanitse.”

  2. 2. Onse afufuza

    M’Mawu a Mulungu,

    Kuti akwaniritse,

    Zomwe alonjeza.

    (KOLASI 2)

    Mkaziyu walonjeza

    Kukonda mwamuna.

    “Chomwe M’lungu wamanga,

    Musalekanitse.”