Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 136

Yehova “Akufupe Mokwanila”

Yehova “Akufupe Mokwanila”

(Rute 2:12)

  1. 1. Yehova ni wokhulupilikadi;

    Saiŵala anthu ake.

    Iye adziŵa kuti nthawi zina

    Iwo amavutikadi.

    Ngati mwasiya nyumba na mabwenzi

    Kuti mumutumikile.

    Adziŵa kutaikilidwa kwanu,

    Adzakudalitsanidi.

    (KOLASI)

    O Yehova akudalitseni

    Akupatseni mphoto yabwino.

    Iye ni wokhulupilika,

    Sadzakusiyani; mudalileni.

  2. 2. Nthawi zina nkhawa za moyo wathu

    Zimaticulukiladi.

    Koma Yehova amasamalila

    Zonse ise timasoŵa.

    Iye amamvela ukapemphela

    Cifukwa amakukonda.

    Mwa mau ake na abale onse,

    Iye adzakutonthoza.

    (KOLASI)

    O Yehova akudalitseni

    Akupatseni mphoto yabwino.

    Iye ni wokhulupilika,

    Sadzakusiyani; mudalileni.

(Onaninso Ower. 11:38-40; Yes. 41:10.)