NYIMBO 137
Azimayi Okhulupilika, Alongo Athu
(Aroma 16:2)
-
1. Sara, Estere, Mariya na Rute—
Iwo anali akazi abwino.
Anali odzipeleka kwa M’lungu,
Timaŵadziŵa na maina awo.
Panali ena osachulidwa,
Naonso anali okhulupilika.
-
2. Onsewa ni zitsanzo za bwinodi.
Anali akazi olimba mtima.
Anali acikondi na ubwino.
Zocita zawo ise titengele.
Tiyamikile alongo athu,
Amatumikila mokhulupilika.
-
3. Atsikana, akazi amasiye,
Mumagwila nchito yanu mwakhama;
Mumadzipeleka mofunitsitsa.
Musaope Yehova ali namwe,
Limbikilani mpaka mapeto;
Mudzasangalala, mudzadalitsidwa.
(Onaninso Afil. 4:3; 1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:4, 5.)