Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 138

Imvi Ndi Chisoti cha Ulemerero

Imvi Ndi Chisoti cha Ulemerero

(Miyambo 16:31)

  1. 1. Pano tili ndi anthu

    Achikulire.

    Akukondabe M’lungu

    Sanamusiye.

    Ena akuvutika

    Ndi umasiye.

    M’lungu atonthozeni,

    Alimbitseni.

    (KOLASI)

    Mumakumbukira

    Zochita zawo.

    M’lungu auzeni:

    “Mwachita bwino.”

  2. 2. Imvi za olungama

    Ndi zokongola.

    Yehova M’lungu wathu

    Amawakonda.

    Tikumbukire kuti

    Kale kalelo,

    Pa unyamata wawo

    Ankayesetsa.

    (KOLASI)

    Mumakumbukira

    Zochita zawo.

    M’lungu auzeni:

    “Mwachita bwino.”