Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 138

Kukongola kwa Imvi

Kukongola kwa Imvi

(Miyambo 16:31)

  1. 1. Pakati pathu pali

    Acikulile.

    Ngakhale avutike,

    Iwo safo’ka.

    Ena anafeledwa.

    Ena adwala.

    Yehova tipemphela,

    Atonthozeni.

    (KOLASI)

    Atate Yehova,

    Adalitseni.

    Auzeni kuti:

    “Mwagwila nchito.”

  2. 2. A imvi olungama

    Ni okongola.

    Yehova aŵakonda

    Sadzaŵasiya.

    Tiziŵayamikila

    Pa nchito zawo.

    Anadzipelekadi

    Na mphamvu zonse.

    (KOLASI)

    Atate Yehova,

    Adalitseni.

    Auzeni kuti:

    “Mwagwila nchito.”

(Onaninso Sal. 71:9, 18; Miy. 20:29; Mat. 25:21, 23; Luka 22:28; 1 Tim. 5:1.)