Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 139

Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

(Chivumbulutso 21:​1-5)

  1. 1. Yerekeza ukuona

    Tonse tili m’dziko latsopano.

    Ona mmene udzamvere

    Kukhala m’dziko lamtendere.

    Oipa onse adzatha.

    M’lungu wathu sadzalephera,

    Adzasinthadi zinthu padzikoli.

    Tidzamuimbira

    nyimbo tikumati:

    (KOLASI)

    “Tikuthokoza mwachita bwino.

    Zonse zakhaladi zatsopano.

    Tikuimba nyimbo mwachisangalalo

    Ndinudi woyenera ulemerero.”

  2. 2. Taganizira m’tsogolo

    Tonse tili m’dziko latsopano.

    Sitidzamva ndi kuona

    Zinthu zotichititsa mantha.

    Zomwe M’lungu walonjeza

    Zonse zidzakwaniritsidwa.

    Adzaukitsanso anthu akufa,

    Iwo ndi ife

    tidzamuyamikira.

    (KOLASI)

    “Tikuthokoza mwachita bwino.

    Zonse zakhaladi zatsopano.

    Tikuimba nyimbo mwachisangalalo

    Ndinudi woyenera ulemerero.”