Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 141

Moyo Ndi Wodabwitsa

Moyo Ndi Wodabwitsa

(Salimo 36:9)

  1. 1. Mphatso ya moyo ndiponso mvula,

    Mbewu komanso kuwala kwa dzuwa,

    Mulungu ndiye amatipatsa

    Mphatsozi ndipo zimatithandizadi.

    (KOLASI)

    Tingachite chani ndi mphatso iyi?

    Tizikonda M’lungu yemwe anatipatsa.

    Sitingaipeze mphatsoyi patokha,

    Mphatso yaketu ndi moyo wodabwitsa.

  2. 2. Ena potopa ndi mavutowa

    Angamanene kuti bola kufa.

    Koma ifeyo sitili choncho.

    Timathokoza kuti tili ndi moyo.

    (KOLASI)

    Tingachite chani ndi mphatso iyi?

    Tizikonda anzathu omwe tili nawo.

    Sitingaipeze mphatsoyi patokha,

    Mphatso yaketu ndi moyo wodabwitsa.