NYIMBO 142

Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

(Aheberi 6:18, 19)

  1. 1. Anthu akhala akuyenda mumdima.

    Ndipo sanapindule kalikonse.

    Zadziwika kuti anthu ochimwa;

    Kuvutika sangakuthetse.

    (KOLASI)

    Tiyeni tiimbe mokondwera!

    Poti Ufumu wa M’lungu wabwera.

    Yesu adzachotsadi zoipa;

    Chiyembekezochi n’chodalirika.

  2. 2. Uthenga womwe ukumveka ndi woti;

    “Tsiku la Mulungu layandikira.”

    Anthu sadzakhalanso ndi chisoni.

    M’lungu wathu timuimbira.

    (KOLASI)

    Tiyeni tiimbe mokondwera!

    Poti Ufumu wa M’lungu wabwera.

    Yesu adzachotsadi zoipa;

    Chiyembekezochi n’chodalirika.