Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 143

Musaleke Kugwila Nchito, Kuyang’anila, na Kuyembekezela

Musaleke Kugwila Nchito, Kuyang’anila, na Kuyembekezela

(Aroma 8: 20-25)

  1. 1. M’lungu wa nyengo na nthawi,

    Dzina lake ni Yehova.

    Posacedwa ‘dzayeletsa

    Dzina lake loyela.

    (KOLASI)

    Moyo udzakhala wacimwemwe,

    Pano padziko lapansi.

    M’lungu watilonjeza.

  2. 2. Iye anakonza nthawi;

    Yakuti Yesu abwele

    Kudzacotsa ‘nthu oipa

    Ndipo adzapambana.

    (KOLASI)

    Moyo udzakhala wacimwemwe,

    Pano padziko lapansi.

    M’lungu watilonjeza.

  3. 3. Olo tivutike bwanji,

    Tidziŵa kuti Yehova,

    Adzatipulumutsadi,

    Na kuthetsa mavuto.

    (KOLASI)

    Moyo udzakhala wacimwemwe,

    Pano padziko lapansi.

    M’lungu watilonjeza.

(Onaninso Mat. 25:13; Luka 12:36.)