NYIMBO 143

Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso Komanso ndi Kudikira

Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso Komanso ndi Kudikira

(Aroma 8:20-25)

  1. 1. Nthawi ya Mulungu wathu,

    Yayandikira kwambiri​​—

    Kutitu alamulire

    Umboni waoneka.

    (KOLASI)

    Pitirizani kukhala maso,

    Kuti mudzapeze moyo,

    Womwe M’lungu wakonza.

  2. 2. M’lungu anaika nthawi;

    Yoti Yesu agonjetse,

    Adani ake onsewa.

    Iye adzapambana.

    (KOLASI)

    Pitirizani kukhala maso,

    Kuti mudzapeze moyo,

    Womwe M’lungu wakonza.

  3. 3. Mavuto m’chilengedwechi,

    Akuchuluka kwambiri.

    Tiyembekeze Yehova,

    Adzatipulumutsa.

    (KOLASI)

    Pitirizani kukhala maso,

    Kuti mudzapeze moyo,

    Womwe M’lungu wakonza.