NYIMBO 144
Mukhulupirikebe
-
1. Pomwe osaona aona,
Ovutika kumva akumva,
Ana akuimbatu nyimbo,
Mtendere padziko lonse.
Pomwe akufa akuuka,
Uchimo ndi mavuto zatha.
(KOLASI)
Mudzaona zinthu zonsezi,
Mukakhulupirikabe.
-
2. Mimbulu ikudya ndi nkhosa,
Mikango ikudya ndi ng’ombe,
Mwana akuzitsogolera,
Zikumvera mawu ake.
Pomwe misozi yonse yatha,
Mantha ndi zopweteka zatha.
(KOLASI)
Mudzaona zinthu zonsezi,
Mukakhulupirikabe.
(Onaninso Yes. 11:6-9; 35:5-7; Yoh. 11:24.)