Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 146

‘Apanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano’

‘Apanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano’

(Chivumbulutso 21: 1-5)

  1. 1. “Zizindikilo” zikutionetsa,

    Kuti Yesu akulamulila.

    Yehova ndiye anamusankha,

    Kuti acotse zoipa m’dziko.

    (KOLASI)

    Tiyeni tisangalale,

    M’lungu adzatidalitsa.

    Iye adzacotsaponso nkhawa,

    kudwala, imfa na kuvutika.

    “Zonse zidzakhala zatsopano,”

    Mawuwa ni oona.

  2. 2. Yerusalemu aoneka bwino,

    Monga mkazi wa mwanawankhosa.

    Yehova ndiye anamukonza,

    Ukwati wake uli pafupi.

    (KOLASI)

    Tiyeni tisangalale,

    M’lungu adzatidalitsa.

    Iye adzacotsaponso nkhawa,

    kudwala, imfa na kuvutika.

    “Zonse zidzakhala zatsopano,”

    Mawuwa ni oona.

  3. 3. Mitundu yonse idzasangalala,

    Na mzinda watsopano woyela.

    Anthu adzayenda mu kuwala.

    Tiyeni tionetse kuwala.

    (KOLASI)

    Tiyeni tisangalale,

    M’lungu adzatidalitsa.

    Iye adzacotsaponso nkhawa,

    kudwala, imfa na kuvutika.

    “Zonse zidzakhala zatsopano,”

    Mawuwa ni oona.

(Onaninso Mat. 16:3; Chiv. 12:7-9; 21:23-25)