NYIMBO 147
Lonjezo la Moyo Wamuyaya
(Salimo 37:29)
-
1. Mulungu watilonjeza,
Moyo wokondweletsa.
Ngati ticita zabwino,
Tidzaulandila.
(KOLASI)
Moyo wamuyaya,
M’lungu walonjeza,
Iye sanganame,
Zidzacitika.
-
2. Ana onse a Yehova,
Adzakhala angwilo.
Mu Ufumu wa Mulungu,
Tidzasangalala.
(KOLASI)
Moyo wamuyaya,
M’lungu walonjeza,
Iye sanganame,
Zidzacitika.
-
3. Posacedwa’pa Mulungu,
Adzaukitsa anthu.
Mitundu yonse ya anthu,
Idzadalitsika.
(KOLASI)
Moyo wamuyaya,
M’lungu walonjeza,
Iye sanganame,
Zidzacitika.
(Onaninso Yes. 25:8; Luka 23:43; Yoh. 11:25; Chiv. 21:4.)