Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 148

Yehova Amapereka Populumukira

Yehova Amapereka Populumukira

(2 Samueli 22:​1-8)

  1. 1. Yehova ndinudi Mulungu wamoyo.

    Mphamvu zaoneka

    M’chilengedwe chonse.

    Palibe M’lungu wina

    angachite zimene

    Inu mumachita.

    (KOLASI)

    Yehova ndiye pothawira pathu.

    Timaonadi kuti iye ndi Thanthwe.

    Tilengeze molimba mtima

    mphamvu zake.

    Tithawire kwa Yehovayo,

    tim’tamande.

  2. 2. Zingwe za imfa zikandizungulira

    Ndidalira inu.

    Mundipatse mphamvu,

    Mundilimbitse mtima,

    mumve kulira kwanga.

    M’lungu ndibiseni.

    (KOLASI)

    Yehova ndiye pothawira pathu.

    Timaonadi kuti iye ndi Thanthwe.

    Tilengeze molimba mtima

    mphamvu zake.

    Tithawire kwa Yehovayo,

    tim’tamande.

  3. 3. Mudzamveka ngati mabingu

    kumwamba.

    Adani anuwo

    Adzanjenjemera.

    Mudzakhala chimene

    mukufuna kukhala.

    Onse adzaona.

    (KOLASI)

    Yehova ndiye pothawira pathu.

    Timaonadi kuti iye ndi Thanthwe.

    Tilengeze molimba mtima

    mphamvu zake.

    Tithawire kwa Yehovayo,

    tim’tamande.