Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 148

Yehova Amapulumutsa

Yehova Amapulumutsa

(2 Samueli 22:1-8)

  1. 1. Yehova, ndimwedi Mulungu wamoyo;

    Ndimwe munalenga

    kumwamba na dziko.

    Ndani angalimbane namwe M’lungu?

    Kulibe.

    Adani adziŵe.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu wathu mpothaŵila.

    Iye ni Thanthwe kwa atumiki ake.

    Tisayope, tilimbe mtima.

    Dzina lake tilengeze pa dziko lonse,

    tim’tamande.

  2. 2. Ngakhale kuti nizingidwe na imfa,

    Atate Yehova,

    nipatseni mphamvu.

    Nilimbitseni mtima,

    n’tetezeni,

    Nipempha, conde M’lungu wanga.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu wathu mpothaŵila.

    Iye ni Thanthwe kwa atumiki ake.

    Tisayope, tilimbe mtima.

    Dzina lake tilengeze pa dziko lonse,

    tim’tamande.

  3. 3. Kucokela kumwamba mudzabangula.

    Olimbana namwe

    adzati nje nje nje.

    Koma okukondani

    adzakondwa

    Cifukwa adzapulumuka.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu wathu mpothaŵila.

    Iye ni Thanthwe kwa atumiki ake.

    Tisayope, tilimbe mtima.

    Dzina lake tilengeze pa dziko lonse,

    tim’tamande.

(Onaninso Sal. 18:1, 2; 144:1, 2.)