NYIMBO 148

Yehova Amapereka Populumukira

Yehova Amapereka Populumukira

(2 Samueli 22:1-8)

  1. 1. Yehova ndinudi Mulungu wamoyo;

    M’chilengedwe chonse

    Mphamvu zaoneka.

    Palibe M’lungu wina angachite

    ​​—zimene

    Inu mumachita.

    (KOLASI)

    Yehova ndiye pothawira pathu.

    Tidzaonadi kuti iye ndi Thanthwe.

    Tilengeze molimba mtima

    mphamvu zake.

    Yehova m’pothawira pathu,

    tim’tamande.

  2. 2. Zingwe za imfa zingandizungulire,

    ndidalira inu,

    “Mundipatse mphamvu,

    mundilimbitse mtima.”

    Mumve kulira kwanga

    “Ndibiseni M’lungu.”

    (KOLASI)

    Yehova ndiye pothawira pathu.

    Tidzaonadi kuti iye ndi Thanthwe.

    Tilengeze molimba mtima

    mphamvu zake.

    Yehova m’pothawira pathu,

    tim’tamande.

  3. 3. Mudzagunda ngati

    mabingu kumwamba.

    Adzanjenjemera;

    Adani anuwo.

    Mudzakhala chimene mukufuna

    kukhala

    Onse adzaona.

    (KOLASI)

    Yehova ndiye pothawira pathu.

    Tidzaonadi kuti iye ndi Thanthwe.

    Tilengeze molimba mtima

    mphamvu zake.

    Yehova m’pothawira pathu,

    tim’tamande.