NYIMBO 149
Nyimbo ya Cipambano
(Ekisodo 15:1)
-
1. Muimbileni Yehova M’lungu wokwezeka.
Aŵaponya m’nyanja Aigupto onyada.
Mutamandeni palibe
Wolingana naye.
Dzina ni Yehova wapambana
Pa nkhondo.
(KOLASI)
Yehova M’lungu wokwezeka
Ndimwe mwekha ‘mene simusintha.
Mudzayeletsadi dzina lanu
Na kuwononga oipa.
-
2. Mitundu yonse, ikutsutsana na Yehova.
Adzaiwononga ngakhale
Ni yamphamvu.
Posacedwapa otsutsa
Adzawonongedwa.
Onse adzadziŵa Yehova
Ni wamphamvu.
(KOLASI)
Yehova M’lungu wokwezeka
Ndimwe mwekha ‘mene simusintha.
Mudzayeletsadi dzina lanu
Na kuwononga oipa.
(Onaninso Sal. 2:2, 9; 92:8; Malaki 3:6; Chiv. 16:16.)