Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

‘Mulungu Analandira’ Mphatso Zawo

‘Mulungu Analandira’ Mphatso Zawo

AHEBERI 11:4

MFUNDO YAIKULU: Mbiri ya zimene Yehova wachita zokhudza kulambira koyera

1-3. (a) Kodi tikambirana mafunso ati? (b) Kodi tikambirana zinthu 4 ziti zofunika pa kulambira koyera? (Onani chithunzi choyambirira.)

 ABELE akuyendera nkhosa zake kuti adziwe mmene zilili. Iye wakhala akuweta nkhosa zimenezi kuyambira zitangobadwa kumene. Tsopano akusankha zina mwa nkhosazi n’kuzipha kenako akuzipereka kwa Mulungu monga mphatso. Kodi Yehova angalandire mphatso imeneyi, yomwe yaperekedwa ndi munthu amene si wangwiro?

2 Mtumwi Paulo anauziridwa kuti alembe zokhudza Abele kuti: “Mulungu . . . analandira mphatso zakezo.” Koma Yehova sanalandire nsembe ya Kaini. (Werengani Aheberi 11:4.) Zimenezi zikubweretsa mafunso ofunika kuwaganizira. N’chifukwa chiyani Mulungu anavomereza kulambira kwa Abele osati kwa Kaini? Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo za Kaini ndi Abele komanso anthu ena amene atchulidwa m’chaputala 11 cha buku la Aheberi? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kumvetsa zimene zimafunika pa kulambira koyera.

3 Tikamakambirana mwachidule zinthu zimene zinachitika kuyambira m’nthawi ya Abele kudzafika m’nthawi ya Ezekieli, tiona zinthu 4 zimene ndi zofunika kwambiri kuti Mulungu azivomereza kulambira kwathu. Zinthu zake ndi izi: Kulambira kwathu kuyenera kupita kwa Yehova, kulambirako kuyenera kukhala kwabwino kwambiri, njira yolambirira iyenera kukhala yovomerezeka ndi Mulungu, komanso munthu afunika kukhala ndi zolinga zabwino akamalambira Mulungu.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sanavomereze Kulambira kwa Kaini?

4, 5. N’chiyani chinathandiza Kaini kudziwa kuti mphatso yake akuyenera kuipereka kwa Yehova?

4 Werengani Genesis 4:2-5. Kaini ankadziwa kuti mphatso yake iyenera kupita kwa Yehova. Kaini anali ndi mwayi komanso nthawi yambiri yoti aphunzire za Yehova. N’kutheka kuti Kaini ndi Abele anali ndi zaka pafupifupi 100 pamene ankapereka mphatso zawo. a Anyamata awiri onsewa anakula akudziwa za munda wa Edeni, n’kuthekanso kuti ankaona munda wachondewo chapatali. N’zodziwikiratu kuti iwo ankaonanso akerubi amene ankatchinga njira yopita kumundawo. (Gen. 3:24) N’zosakayikitsa kuti makolo a anyamatawa anawauza kuti Yehova analenga zamoyo zonse komanso kuti moyo umene ankakhala unali wosiyana kwambiri ndi cholinga cha Mulungu chokhudza anthu. Iwo ankavutika, kukalamba komanso ankayembekezera kuti adzafa. (Gen. 1:24-28) Kudziwa zinthu zimenezi kunathandiza Kaini kuti azindikire kuti mphatso yake iyenera kuperekedwa kwa Mulungu.

5 Chinanso n’chiyani chimene chinachititsa Kaini kuti apereke nsembe? Yehova anali ataneneratu kuti padzakhala “mbadwa” kapena kuti winawake amene adzaphwanye mutu wa “njoka” imene inapusitsa Hava n’kumupangitsa kusankha zinthu zolakwika. (Gen. 3:4-6, 14, 15) Popeza Kaini anali woyamba kubadwa, n’kutheka kuti ankaganiza kuti “mbadwa” yolonjezedwayo ndi iyeyo. (Gen. 4:1) Kuwonjezera pamenepo Yehova sanasiyiretu kulankhula ndi anthu ngakhale kuti anali ochimwa. Mwachitsanzo Adamu atachimwa, Mulungu analankhula naye ndipo zikuoneka kuti anachita zimenezi kudzera mwa mngelo. (Gen. 3:8-10) Komanso Yehova analankhula ndi Kaini atapereka nsembe yake. (Gen. 4:6) Mosakaikira Kaini ankadziwa kuti Yehova ndi woyenera kumulambira.

6, 7. Kodi panali cholakwika chilichonse ndi mtundu wa nsembe imene Kaini anapereka komanso njira imene anaperekera? Fotokozani.

6 Nanga n’chifukwa chiyani Yehova sanasangalale ndi nsembe ya Kaini? Kodi chinali chifukwa chakuti mphatsoyo sinali yabwino kwambiri? Baibulo silinena chilichonse. Limangonena kuti Kaini anabweretsa “zokolola zake zakumunda.” Patapita nthawi, Yehova anasonyeza m’Chilamulo chimene anapereka kwa Mose kuti nsembe zamtundu umenewu ndi zovomerezeka. (Num. 15:8, 9) Komanso taganizirani mmene zinthu zinalili. Pa nthawi imeneyo anthu ankadya zomera basi. (Gen. 1:29) Komanso chifukwa chakuti Mulungu anali atatemberera nthaka imene inali kunja kwa munda wa Edeni, Kaini anavutika kwambiri kuti apeze nsembe yake. (Gen. 3:17-19) Iye anapereka nsembe imene inali chakudya chimene anthu ankadalira kuti akhale ndi moyo. Ngakhale zinali choncho Yehova sanalandire nsembe ya Kaini.

7 Ndiye kodi panali china chake cholakwika ndi njira imene Kaini anaperekera mphatsoyi? Kodi Kaini sanapereke nsembeyi m’njira yovomerezeka? N’kutheka kuti chifukwa chake sichinali chimenecho. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti pamene Yehova ankakana nsembe ya Kaini, sanamudzudzule chifukwa cha njira imene anasankha popereka nsembeyo. Komanso Baibulo silifotokoza chilichonse chokhudza mmene Kaini kapena Abele anaperekera nsembe zawo. Ndiye kodi chinavuta n’chiyani?

Zolinga za Kaini sizinali zabwino (Onani Ndime 8, 9)

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani Yehova sanasangalale ndi Kaini komanso nsembe yake? (b) Kodi n’chiyani chimene chakuchititsani chidwi ndi zimene Baibulo limanena zokhudza Kaini ndi Abele?

8 Mawu ouziridwa amene Paulo analembera Aheberi amasonyeza kuti cholinga chimene Kaini anaperekera nsembeyo sichinali chabwino. Kaini analibe chikhulupiriro. (Aheb. 11:4; 1 Yoh. 3:11, 12) N’chifukwa chake Yehova sanasangalale ndi Kaini mwiniwakeyo, osati nsembe yake yokhayo. (Gen. 4:5-8) Yehova ndi Bambo wachikondi choncho anayesetsa kuthandiza Kaini mokoma mtima. Koma Kaini anakana kuthandizidwa ndi Yehova. Mumtima mwa Kaini munali mutadzaza “chidani, ndewu, nsanje,” zomwe ndi ntchito za thupi lochimwali. (Agal. 5:19, 20) Mtima woipa wa Kaini unachititsa kuti zinthu zina zimene anachita polambira Yehova zikhale zopanda ntchito. Zimene zinachitikira Kaini zikutiphunzitsa kuti kulambira koyera kumafuna zambiri osati chabe kungodzionetsera kuti ndife odzipereka kwa Yehova.

9 Baibulo limatiuza zambiri zokhudza Kaini. Mwachitsanzo timawerenga zimene Yehova anauza Kaini, zimene iye anayankha, mayina a ana ake komanso zina mwa zinthu zimene ana akewo anachita. (Gen. 4:17-24) Koma Baibulo silinena ngati Abele anali ndi ana komanso silinena chilichonse chimene analankhula. Ngakhale zili choncho, zinthu zimene anachita zikulankhulabe mpaka pano. Kodi zimenezi zikutheka bwanji?

Abele Anatipatsa Chitsanzo pa Nkhani ya Kulambira Koyera

10. Kodi Abele anapereka chitsanzo chotani pa kulambira koyera?

10 Abele anapereka nsembe yake kwa Yehova chifukwa ankadziwa kuti ndi Yehova yekha amene ali woyenera kulandira nsembeyo. Mphatso yake inali yabwino kwambiri. Iye anasankha “ana oyamba a ziweto zake.” Ngakhale kuti Baibulo silinena ngati ziwetozi anazipereka paguwa lansembe kapena ayi, koma n’zosakayikitsa kuti njira imene anaperekera nsembeyo inali yovomerezeka. Abele anapereka mphatso yakeyi zaka 6,000 zapitazo. Koma zimene zimatichititsa chidwi ndi cholinga chimene anali nacho popereka mphatsoyi ndipo zimenezi zimatipatsa phunziro lofunika kwambiri. Iye anapereka mphatsoyi chifukwa ankakhulupirira Mulungu komanso chifukwa chakuti ankakonda kwambiri mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Tikudziwa bwanji zimenezi?

Abele anatsatira zinthu 4 zofunika pa kulambira koyera (Onani Ndime 10)

11. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti Abele anali wolungama?

11 Choyamba, taganizirani zimene Yesu ananena zokhudza Abele, munthu yemwe ankamudziwa bwino kwambiri. Yesu anali ali kumwamba pa nthawi imene Abele anali ndi moyo. Yesu ankachita chidwi kwambiri ndi mwana wa Adamu ameneyu. (Miy. 8:22, 30, 31; Yoh. 8:58; Akol. 1:15, 16) Choncho pamene Yesu ananena kuti Abele anali munthu wolungama, ankanena zinthu zimene anaona ndi maso ake. (Mat. 23:35) Munthu wolungama ndi munthu amene amazindikira kuti Yehova ndi amene ali woyenera kukhazikitsa mfundo zokhudza chabwino ndi choipa. Koma amachitanso zambiri. Zolankhula komanso zochita zake zimasonyeza kuti amagwirizana ndi mfundo zokhudza chabwino ndi choipa zimene Mulungu anakhazikitsazo. (Yerekezerani ndi Luka 1:5, 6) Zimatenga nthawi kuti munthu azidziwika kuti ndi munthu wolungama. Choncho ngakhale asanapereke mphatso yake kwa Mulungu, Abele ankadziwika kuti ndi munthu amene ankatsatira mfundo za Yehova. Komatu kuchita zimenezi sikunali kophweka kwa iye. N’zosakayikitsa kuti mchimwene wake Kaini sankamupatsa chitsanzo chabwino chifukwa anali ndi mtima woipa. (1 Yoh. 3:12) Mayi ake a Abele sanamvere lamulo lomveka bwino limene Mulungu anapereka komanso bambo ake anapandukira Yehova, chifukwa ankafuna kuti azisankha okha chabwino ndi choipa. (Gen. 2:16, 17; 3:6) Apatu Abele anasonyeza kulimba mtima kwambiri chifukwa anasankha zinthu zosiyana ndi zimene anthu am’banja lake anasankha.

12. Kodi Kaini ndi Abele ankasiyana bwanji?

12 Chachiwiri, taonani mmene mtumwi Paulo anasonyezera kugwirizana pakati pa kukhala ndi chikhulupiriro ndi kukhala wolungama. Iye analemba kuti: “Chifukwa cha chikhulupiriro, Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yamtengo wapatali kuposa ya Kaini. Ndipo chifukwa cha chikhulupirirocho, Mulungu anamupatsa umboni wakuti anali wolungama.” (Aheb. 11:4) Zimene Paulo analembazi zikusonyeza kuti mosiyana ndi Kaini, Abele anapereka nsembe chifukwa chakuti kwa moyo wake wonse ankakhulupirira Yehova kuchokera pansi pa mtima komanso ankakhulupirira njira imene Yehova amachitira zinthu.

13. Kodi chitsanzo cha Abele chikutiphunzitsa chiyani?

13 Zimene Abele anachitazi zikutiphunzitsa kuti kulambira koyera kumachokera mumtima umene uli ndi zolinga zabwino. Izi zikutanthauza kuti munthu ayenera kumakhulupirira Yehova kuchokera pansi pa mtima komanso kumachita zinthu zogwirizana ndi mfundo zake zolungama. Kuwonjezera pamenepa, tikuphunzira kuti kulambira koyera kumafuna zambiri osati kungochita zinthu zosonyeza kudzipereka kamodzi kokha. Kumakhudza moyo wathu wonse komanso zochita zathu zonse.

Makolo Akale Anatsatira Chitsanzo cha Abele

14. N’chifukwa chiyani Yehova analandira mphatso zimene Nowa, Abulahamu ndi Yakobo anapereka?

14 Pa anthu omwe si angwiro, Abele anali munthu woyamba kulambira Yehova m’njira yoyenera koma sanali womaliza. Mtumwi Paulo anatchula anthu enanso amene ankalambira Yehova m’njira yoyenera. Ena mwa anthu amenewa anali Nowa, Abulahamu ndi Yakobo. (Werengani Aheberi 11:7, 8, 17-21.) Nthawi ina pa moyo wawo anthu amenewa anapereka nsembe kwa Yehova ndipo Yehovayo analandira mphatso zawozo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anthu amenewa anachita zinthu zambiri osati kungochita mwamwambo zinthu zokhudza kulambira. Aliyense wa iwo anakwaniritsa zinthu zimene zimafunika pa kulambira koyera. Tiyeni tione zimene anachita.

Nsembe za Nowa zinapereka uthenga wamphamvu (Onani Ndime 15, 16)

15, 16. Kodi Nowa anakwaniritsa bwanji zinthu 4 zofunika pa kulambira koyera?

15 Nowa anabadwa patangopita zaka 126 zokha kuchokera pamene Adamu anamwalira koma anakulira m’dziko limene anthu ambiri ankalambira mafano. b (Gen. 6:11) Pa mabanja onse amene anali padziko lapansi Chigumula chisanachitike, Nowa yekha ndi banja lake ndi amene ankalambira Yehova m’njira yovomerezeka. (2 Pet. 2:5) Atapulumuka Chigumula, Nowa anaona kuti akuyenera kumanga guwa lansembe n’kupereka nsembe kwa Yehova. Guwa lansembe limeneli ndi loyamba kutchulidwa m’Baibulo. Zimene Nowa anachitazi, zinathandiza anthu am’banja lake komanso mbadwa zake zonse kudziwa kuti kulambira kwathu kuyenera kupita kwa Yehova yekha basi. Pa nyama zonse zomwe zinalipo zomwe akanatha kupereka nsembe, Nowa anasankha “zina mwa nyama zonse zosadetsedwa, ndi zina mwa zouluka zonse zosadetsedwa.” (Gen. 8:20) Nyama zimenezi zinali nsembe zabwino kwambiri chifukwa Yehova ndi amene ananena kuti zinali zoyera.—Gen. 7:2.

16 Nowa anapereka nsembe zopsereza zimenezi paguwa lansembe limene anamanga lija. Kodi njira yolambirira imeneyi inali yovomerezeka? Inde. Baibulo limanena kuti Yehova anasangalala ndi kafungo kokoma kamene kankachokera ku nsembe zimenezi ndipo anadalitsa Nowa ndi ana ake. (Gen. 8:21; 9:1) Koma Yehova analandira nsembeyi makamaka chifukwa cha cholinga chimene Nowa anali nacho popereka nsembeyi. Nsembezi zinali njira imodzi imene Nowa anasonyezera kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova komanso mmene amachitira zinthu. Popeza kuti Nowa ankamvera Yehova nthawi zonse komanso kutsatira mfundo zake, Baibulo limanena kuti iye “anayenda ndi Mulungu woona.” Chifukwa cha zimenezi Nowa amadziwika kuti anali munthu wolungama.—Gen. 6:9; Ezek. 14:14; Aheb. 11:7.

17, 18. Kodi Abulahamu anakwaniritsa bwanji zinthu 4 zofunika pa kulambira koyera?

17 Anthu ambiri m’nthawi ya Abulahamu ankalambira mafano. Mzinda wa Uri, komwe kunali kwawo kwa Abulahamu, unali wotchuka chifukwa cha kachisi amene anamangidwa polemekeza mulungu wa dzuwa dzina lake Nana. c Ngakhalenso bambo ake a Abulahamu pa nthawi ina ankalambira milungu yabodza. (Yos. 24:2) Koma Abulahamu anasankha kulambira Yehova. N’kutheka kuti anadziwa za Mulungu woona kuchokera kwa agogo ake a Semu, omwe anali mwana wa Nowa. Iwo anakhala limodzi ndi moyo kwa zaka 150.

18 Pa nthawi yonse imene anakhala ndi moyo Abulahamu anapereka nsembe zambiri. Koma nthawi zonse nsembe zimene ankapereka pa kulambira kwake ankazipereka kwa Yehova yekha, yemwe ndi woyenera kuzilandira. (Gen. 12:8; 13:18; 15:8-10) Kodi Abulahamu anali wokonzeka kupereka kwa Yehova nsembe zabwino kwambiri? Funso limeneli linayankhidwa pamene Abulahamu anasonyeza kuti anali wokonzeka kupereka mwana wake wokondedwa Isaki, monga nsembe. Pa nthawi imeneyo Yehova anamuuza njira imene akuyenera kutsatira popereka nsembe. (Gen. 22:1, 2) Abulahamu ankafunitsitsa kutsatira malangizo amenewo mosamala kwambiri. Yehova ndi amene anamuletsa Abulahamu kuti asaphe mwana wake. (Gen. 22:9-12) Yehova anasangalala ndi zimene Abulahamu anachitazi chifukwa choti ankachita zimenezi ndi zolinga zabwino. Paulo analemba kuti: “Abulahamu anakhulupirira zimene Yehova anamuuza, ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama.”—Aroma 4:3.

Yakobo anapereka chitsanzo chabwino kwa banja lake (Onani Ndime 19, 20)

19, 20. Kodi Yakobo anakwaniritsa bwanji zinthu 4 zofunika pa kulambira koyera?

19 Ku Kanani n’kumene Yakobo anakhalako kwa nthawi yayitali pa moyo wake. Limeneli linali dziko limene Yehova analonjeza Abulahamu ndi mbadwa zake. (Gen. 17:1, 8) M’dziko limeneli anthu ankachita zinthu zoipa kwambiri zokhudzana ndi kulambira moti Yehova ananena kuti dzikolo “lidzalavula anthu ake kunja.” (Lev. 18:24, 25) Yakobo ali ndi zaka 77 anachoka ku Kanani n’kupita kukakwatira ndipo kenako anabwereranso ku Kanani ali ndi banja lalikulu. (Gen. 28:1, 2; 33:18) Komano anthu ena a m’banja lake anayamba kulambira mafano. Ngakhale zinali choncho, Yehova atauza Yakobo kuti apite ku Beteli n’kukamanga guwa lansembe, iye anachitapo kanthu nthawi yomweyo. Choyamba iye anauza anthu a m’banja lake kuti: ‘Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu ndipo mudziyeretse.’ Kenako anatsatira mokhulupirika malangizo amene anapatsidwa.—Gen. 35:1-7.

20 Yakobo anamanga maguwa ansembe angapo m’Dziko Lolonjezedwa, koma nthawi zonse nsembe zake ankazipereka kwa Yehova. (Gen. 35:14; 46:1) Nsembe zake zinali zabwino kwambiri. Njira imene ankalambirira Mulungu komanso zolinga zake zinali zabwino moti Baibulo limati Yakobo anali “munthu wosalakwa.” Mawu amenewa amanena za munthu amene Mulungu akusangalala naye. (Gen. 25:27) Zonse zimene Yakobo ankachita pa moyo wake anapereka chitsanzo chabwino kwa mtundu wonse wa Isiraeli, umene unachokera mwa iye.—Gen. 35:9-12.

21. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza kulambira koyera pa zitsanzo za makolo akale?

21 Kodi zitsanzo zimene makolo akalewa anasonyeza zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kulambira koyera? Mofanana ndi makolowa ifenso tazunguliridwa ndi anthu, mwinanso achibale athu amene angatilepheretse kulambira Yehova mokhulupirika. Kuti tisagonje tikuyenera kukhulupirira kwambiri Yehova komanso kukhala otsimikiza kuti mfundo zake zolungama ndi zabwino kwambiri. Timasonyeza chikhulupiriro chimenecho pomvera Yehova komanso pogwiritsa ntchito mphamvu zathu, nthawi yathu ndi chuma chathu pomutumikira. (Mat. 22:37-40; 1 Akor. 10:31) N’zosangalatsatu kwambiri kudziwa kuti tikamadzipereka polambira Yehova m’njira imene iye amafuna komanso tili ndi zolinga zabwino, iye amationa kuti ndife olungama.—Werengani Yakobo 2:18-24.

Mtundu Wodzipereka pa Kulambira Koyera

22-24. Kodi Chilamulo chinatsindika bwanji kufunika kwa amene ankayenera kulandira nsembe za Aisiraeli, mtundu wa nsembe zimene ankayenera kupereka komanso njira imene ankayenera kuziperekera?

22 Yehova anapereka Chilamulo kwa mbadwa za Yakobo chimene chinawathandiza kuti azidziwa zimene Yehova ankafuna pa nkhani ya kulambira. Akanamvera Yehova akanakhala “chuma [chake] chapadera” komanso ‘mtundu woyera.’ (Eks. 19:5, 6) Tiyeni tione mmene Chilamulocho chinasonyezera kufunika kwa zinthu 4 zomwe ndi zofunika pa kulambira koyera.

23 Yehova anauza Aisiraeli momveka bwino za Mulungu amene akuyenera kumulambira. Yehova anawauza kuti: “Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.” (Eks. 20:3-5) Nsembe zimene ankapereka zinkayenera kukhala zabwino kwambiri. Mwachitsanzo nyama zimene ankapereka nsembe zinkayenera kukhala zopanda chilema. (Lev. 1:3; Deut. 15:21; Yerekezerani ndi Malaki 1:6-8.) Alevi ankapindula ndi mphatso zimene anthu ankapereka kwa Yehova koma nawonso ankapereka mphatso. Zimene ankapereka zinkayenera kuchokera “pa mphatso zonse zabwino koposa” zimene ankapatsidwa. (Num. 18:29) Ponena za njira imene Aisiraeli ankayenera kutsatira polambira, iwo anapatsidwa malangizo osapita m’mbali a nsembe zimene akuyenera kupereka, kumene akuyenera kuziperekera komanso mmene angaperekere nsembezo kwa Yehova. Malamulo onse amene anapatsidwa kuti aziwatsatira anali oposa 600 ndipo anauzidwa kuti: “Muonetsetse kuti mukuchita zimene Yehova Mulungu wanu wakulamulani. Musatembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.”—Deut. 5:32.

24 Kodi pakanakhala vuto ngati Aisiraeli akanamaperekera nsembe zawo pamalo alionse? Inde. Yehova anauza anthu akewo kuti amange chihema ndipo n’kumene kunkachitikira kulambira koyera. (Eks. 40:1-3, 29, 34) Pa nthawiyo, Aisiraeli akafuna kuti nsembe zawo zikhale zovomerezeka kwa Mulungu ankayenera kupita nazo kuchihemako. dDeut. 12:17, 18.

25. Pa nkhani ya nsembe, kodi chofunika kwambiri chinali chiyani? Fotokozani.

25 Chimene chinali chofunika kwambiri chinali cholinga chimene munthu aliyense wa Chiisiraeli anali nacho popereka mphatsoyo. Ankayenera kupereka nsembeyo chifukwa chokonda kwambiri Yehova komanso mfundo zake. (Werengani Deuteronomo 6:4-6.) Aisiraeli akamalambira Mulungu mwa mwambo chabe, Yehova ankakana kulandira nsembe zawozo. (Yes. 1:10-13) Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anasonyeza kuti sangapusitsidwe ndi zochita za munthu zongodzionetsera kuti ndi wodzipereka. Iye ananena kuti: “Anthu awa . . . amandilemekeza ndi milomo yawo yokha, koma mitima yawo aiika kutali ndi ine.”—Yes. 29:13.

Kulambira kwa Pakachisi

26. Poyamba kodi kachisi amene Solomo anamanga anathandiza bwanji pa kulambira koyera?

26 Patapita zaka zambiri Aisiraeli atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa, Mfumu Solomo anamanga likulu la kulambira koyera limene linali ndi ulemerero waukulu kuposa chihema. (1 Maf. 7:51; 2 Mbiri 3:1, 6, 7) Poyamba Yehova yekha ndi amene ankalandira nsembe zimene zinkaperekedwa pakachisi. Solomo ndi anthu ake anapereka nsembe zochuluka zabwino kwambiri ndipo anazipereka potsatira zimene Chilamulo cha Mulungu chinanena. (1 Maf. 8:63) Koma ndalama zimene anagwiritsa ntchito pomanga kachisiyo komanso kuchuluka kwa nsembe zimene ankapereka, si zimene zinkachititsa kuti Yehova azivomereza kulambira kwa pakachisi. Chofunika chinali zolinga za anthu amene akupereka nsembezo. Solomo anatsindika mfundo imeneyi pamene ankatsegulira kachisi. Iye ananena kuti: “Muzitumikira Yehova Mulungu wathu ndi mtima wathunthu potsatira malangizo ake ndi kusunga malamulo ake ngati mmene mukuchitira lero.”—1 Maf. 8:57-61.

27. Kodi mafumu a Isiraeli ndi anthu amene ankawalamulira anatani, nanga Yehova anachita chiyani?

27 N’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli sanapitirize kutsatira malangizo anzeru amene mfumuyi inapereka. Iwo analephera kukwaniritsa mfundo zofunika zokhudza kulambira koyera. Mafumu a Isiraeli komanso anthu awo analola kuti mitima yawo iipe, anasiya kukhulupirira Yehova komanso anasiya kutsatira mfundo zake zolungama. Nthawi ndi nthawi, mwachikondi Yehova ankatumiza aneneri kuti awathandize kusintha komanso kuwachenjeza kuti akapitiriza kuchita zoipa adzakumana ndi mavuto. (Yer. 7:13-15, 23-26) Mmodzi mwa aneneri amenewo anali Ezekieli yemwe anali munthu wokhulupirika. Iye anakhala ndi moyo pa nthawi yovuta kwambiri mumbiri ya kulambira koyera.

Ezekieli Anaona Anthu Akudetsa Kulambira Koyera

28, 29. Kodi tikudziwa chiyani zokhudza Ezekieli? (Onani bokosi lakuti “Moyo wa Ezekieli Komanso Mmene Zinthu Zinalili M’nthawi Yake.”)

28 Ezekieli ankadziwa bwino kwambiri kulambira kumene kunkachitika pakachisi amene Solomo anamanga. Bambo ake anali wansembe ndipo ayenera kuti ankatumikira kukachisi ameneyo. (Ezek. 1:3) Ezekieli ayenera kuti ankasangalala ali wamng’ono. N’zodziwikiratu kuti bambo ake anamuphunzitsa zokhudza Yehova ndi Chilamulo. Komanso pa nthawi imene Ezekieli anabadwa “buku la Chilamulo” linapezeka m’kachisi. e Yosiya yemwe anali mfumu yabwino yomwe inkalamulira pa nthawiyo anakhudzidwa kwambiri ndi zimene anamva moti anawonjezera ntchito imene ankachita yolimbikitsa kulambira koyera.—2 Maf. 22:8-13.

Mosakayikira bambo ake a Ezekieli anamuphunzitsa zokhudza Yehova ndi Chilamulo (Onani Ndime 28

29 Mofanana ndi amuna okhulupirika omwe analipo iye asanabadwe, Ezekieli anakwaniritsa zinthu 4 zomwe zimafunika pa kulambira koyera. Tikamawerenga buku la Ezekieli timaona kuti iye ankatumikira Yehova yekha ndipo nthawi zonse ankachita zimenezi modzipereka. Ankachita zimene Yehova wamuuza ndipo ankazichita mmene Mulunguyo akufunira. Ezekieli ankachita zonsezi chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro cholimba. Anthu ambiri m’nthawi yake sankachita zimenezi. Ali mwana Ezekieli ankamvetsera maulosi a Yeremiya amene anayamba utumiki wake mu 647 B.C.E. ndipo ankachenjeza anthu za kubwera kwa chiweruzo cha Yehova.

30. (a) Kodi maulosi amene Ezekieli analemba amasonyeza chiyani? (b) Kodi ulosi n’chiyani, nanga ulosi umene Ezekieli analemba tiziuona bwanji? (Onani bokosi lakuti, “Kumvetsa Maulosi a Ezekieli.”)

30 Mawu ouziridwa amene Ezekieli analemba amasonyeza kuti anthu a Mulungu anali atasiyiratu kumutumikira. (Werengani Ezekieli 8:6.) Pa nthawi imene Yehova anayamba kupereka chilango ku Yuda, Ezekieli anali m’gulu la anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. (2 Maf. 24:11-17) Ngakhale kuti anatengedwa kupita ku ukapolo, sikuti Ezekieli ankapatsidwa chilango. Yehova anali ndi ntchito yoti Ezekieli agwire pakati pa anthu ake, amene anali ku ukapolo. Masomphenya ochititsa chidwi komanso maulosi amene Ezekieli analemba anafotokoza zimene zidzachitike pobwezeretsa kulambira koyera ku Yerusalemu. Koma sizokhazo. Amasonyezanso mmene pamapeto pake kulambira koyera kudzabwezeretsedwere kwa onse amene amakonda Yehova.

31. Kodi bukuli litithandiza kuchita chiyani?

31 M’magawo otsatira a bukuli tikambirana za kumwamba kumene Yehova amakhala, tiona mmene anthu anadetsera kulambira koyera, tiphunzira mmene Yehova anabwezeretsera komanso kuteteza anthu ake ndipo tiona zakutsogolo pamene anthu onse azidzalambira Yehova. M’mutu wotsatira tikambirana masomphenya oyamba amene Ezekieli analemba. Masomphenyawo atithandiza kuona m’maganizo mwathu chithunzi cha Yehova komanso mbali yakumwamba ya gulu lake. Zimenezi zitithandiza kuona chifukwa chake iye yekha ali woyenera kulambiridwa.

a Zikuoneka kuti Abele anabadwa patangopita nthawi yochepa Adamu ndi Hava atathamangitsidwa m’munda wa Edeni. (Gen. 4:1, 2) Lemba la Genesis 4:25 limanena kuti Mulungu anapereka Seti “mʼmalo mwa Abele.” Adamu anali ndi zaka 130 pamene anabereka Seti, pambuyo poti Abele waphedwa mwankhanza. (Gen. 5:3) Choncho Abele ayenera kuti anali ndi zaka 100 pamene Kaini anamupha.

b Lemba la Genesis 4:26 limanena kuti m’masiku a Enosi, amene anali mdzukulu wake wa Adamu, “anthu anayamba kuitanira pa dzina la Yehova.” Koma zikuoneka kuti ankachita zimenezi mopanda ulemu. N’kutheka kuti ankagwiritsa ntchito dzina la Yehova polambira mafano.

c Mulungu wamwamuna dzina lake Nana ankadziwikanso ndi dzina lakuti Sini. Ngakhale kuti anthu a ku Uri ankalambira milungu yambiri, akachisi komanso maguwa ansembe amumzindawo ankawagwiritsa ntchito polambira mulungu ameneyu.

d Likasa lopatulika litachotsedwa m’chihema, zikuoneka kuti Yehova ankavomereza nsembe zimene zinkaperekedwa m’malo ena osati kuchihema kokha.—1 Sam. 4:3, 11; 7:7-9; 10:8; 11:14, 15; 16:4, 5; 1 Mbiri 21:26-30.

e Zikuoneka kuti Ezekieli anali ndi zaka 30 pamene anayamba kunenera mu 613 B.C.E. Choncho ayenera kuti anabadwa m’chaka cha 643 B.C.E. (Ezek. 1:1) Yosiya anayamba kulamulira mu 659 B.C.E., ndipo buku la Chilamulo, mwina loyambirira lenileni, linapezeka atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 18 akulamulira kapena cha m’ma 642-641 B.C.E.