Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

“Ndinayamba Kuona Masomphenya a Mulungu”

“Ndinayamba Kuona Masomphenya a Mulungu”

EZEKIELI 1:1

MFUNDO YAIKULU: Mfundo zachidule za masomphenya a Ezekieli okhudza galeta lakumwamba

1-3. (a) Fotokozani zimene Ezekieli anaona komanso kumva. (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi ndi ndani amene ankachititsa zimene Ezekieli ankaona, nanga zinamukhudza bwanji?

 EZEKIELI akuyang’ana chapatali ndipo maso ake akuona chigwa chachikulu cha mchenga. Akufinya maso ake kenako akuwatsegula. Iye ali ndi mantha ndipo sakukhulupirira zimene akuona. Chapatali akuona kuti kukubwera mphepo yamkuntho. Koma imeneyi si mphepo wamba. Pamene mphepo yochititsa mantha yochokera kumpoto ikugwedeza tsitsi ndi zovala zake, iye akuona mtambo waukulu. Mtambowo ukuwala chifukwa cha malawi a moto ndipo kuwala kwake kukumukumbutsa chitsulo chamtengo wapatali chosungunula. a Pamene mtambowo ukuyandikira Ezekieli, pakumveka phokoso limene likuwonjezerekawonjezereka. Phokosoli likumveka ngati mkokomo wa gulu lalikulu la asilikali amene akuyenda.​—Ezek. 1:4, 24.

2 Izi zinali zinthu zoyamba pa zinthu zambiri zosaiwalika zimene zinachitikira Ezekieli ndipo apa n’kuti ali ndi zaka pafupifupi 30. Iye ankaona kuti “mphamvu za Yehova,” kapena kuti mphamvu zazikulu za mzimu woyera wa Yehova, zikugwira ntchito pa iye. Zimene Ezekieli anaona komanso kumva mothandizidwa ndi mzimuwo, zinali zochititsa chidwi ndiponso zodabwitsa kwambiri kuposa zinthu zimene munthu angaone m’mafilimu amene anthu akupanga masiku ano. Ezekieli ataona masomphenya amenewa anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo anachita mantha kwambiri.​—Ezek. 1:3, 28.

3 Koma Yehova anali ndi zinthu zambiri zoti amuonetse osati kungomuchititsa mantha. Masomphenya oyamba a Ezekieli, mofanana ndi masomphenya ena onse amene analembedwa m’buku la maulosi ochititsa chidwili, ali ndi tanthauzo lofunika kwambiri kwa iyeyo komanso kwa atumiki onse okhulupirika a Yehova masiku ano. Choncho tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane zimene Ezekieli anaona ndi kumva.

Mmene Zinthu Zinalili

4, 5. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi imene Ezekieli ankaona masomphenya?

4 Werengani Ezekieli 1:1-3. Choyamba tiyeni tione mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Chinali chaka cha 613 B.C.E. Monga tinaonera m’mutu wapita uja, Ezekieli anali ku Babulo ndipo ankakhala mphepete mwa mtsinje wa Kebara limodzi ndi anthu ena amenenso anatengedwa kupita ku ukapolo. Zikuoneka kuti mtsinje umenewu unali ngalande imene anthu anachita kukumba ndipo inatuluka mumtsinje wa Firate n’kukalumikizananso ndi mtsinje womwewo kutsogolo kwake.

Ezekieli ankakhala pafupi ndi mtsinje wa Kebara limodzi ndi anthu ena amene anatengedwa kupita ku ukapolo (Onani Ndime 4)

5 Anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolowa anachokera ku Yerusalemu, mtunda wa makilomita pafupifupi 800. b M’kachisi amene bambo ake a Ezekieli ankatumikira monga wansembe, munkachitika zakatangale komanso anthu ankalambiriramo mafano. Mpando wachifumu ku Yerusalemu, umene unali waulemerero pamene Davide ndi Solomo ankalamulira, pa nthawiyi chinali chinthu chochititsa manyazi. Mfumu Yehoyakini amene analibe chikhulupiriro, anatengedwa limodzi ndi Ayuda ena kupita ku Babulo. Zedekiya, amene analowa m’malo mwake, ankangouzidwa zochita ndi mfumu ina ndipo anali munthu woipa.​—2 Maf. 24:8-12, 17, 19.

6, 7. N’chifukwa chiyani Ezekieli ayenera kuti ankaona kuti imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri?

6 Kwa munthu wachikhulupiriro ngati Ezekieli, imeneyi iyenera kuti inali nthawi yovuta kwambiri. Mwina anthu ena amene anatengedwa naye limodzi kupita ku ukapolo ankadzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova watisiya mpaka kalekale? Kodi ulamuliro woipa wa Babulowu limodzi ndi milungu yake yabodza uthetsadi kulambira koyera komanso ulamuliro wa Yehova padziko lapansi?’

7 Pamene mukuganizira mfundo zimenezi, mungachite bwino kuyamba kuphunzira panokha nkhani imeneyi powerenga zimene Ezekieli anafotokoza momveka bwino m’masomphenya ake oyamba. (Ezek. 1:4-28) Mukamawerenga, muziyerekezera kuti ndinu Ezekieli ndipo mukuona zimene iye ankaona komanso kumva zimene ankamva.

Mtsinje wa Firate m’dera lapafupi ndi Karikemisi (Onani Ndime 5-7)

Galeta Lapadera Kwambiri

8. Kodi Ezekieli anaona chiyani m’masomphenya ndipo chinkaimira chiyani?

8 Kodi chinthu chimene Ezekieli anaona tingachifotokoze bwanji? Chinkaoneka ngati galeta lalikulu komanso lochititsa mantha. Galetalo linali ndi mawilo 4 akuluakulu ndipo panalinso angelo 4 ooneka modabwitsa, amene pambuyo pake anadziwika kuti anali akerubi. (Ezek. 10:1) Pamwamba pa akerubiwo panali thambo lalikulu looneka ngati madzi oundana. Pamwamba pa thamboli panali mpando wachifumu waulemerero wa Mulungu ndipo Yehova anali atakhalapo. Koma kodi galeta limeneli linkaimira chiyani? Masomphenya a Ezekieli amenewa akuimira chinthu chimodzi basi chomwe ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani mfundo zitatu izi zimene zikutipangitsa kunena zimenezi.

9. Kodi mmene Yehova amachitira zinthu ndi angelo zikugwirizana bwanji ndi mmene galeta lake lilili?

9 Ubwenzi umene Yehova ali nawo ndi angelo. Kumbukirani kuti m’masomphenyawa, mpando wachifumu wa Yehova waikidwa pamwamba pa akerubi. Mavesi ena m’Baibulo amafotokoza kuti Yehova wakhala pamwamba kapena pakati pa akerubi ake. (Werengani 2 Mafumu 19:15; Eks. 25:22; Sal. 80:1) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti wakhala pamwamba pa akerubi enieniwo ngati kuti amafunika kunyamulidwa ndi angelo amphamvuwo kapenanso ngati kuti amafunika kukwera galeta lenileni. Koma akerubiwo amatumikira Yehova yemwe ndi Wolamulira Wamkulu ndipo iye amatha kuwatuma kulikonse m’chilengedwechi kuti akachite zinthu zokhudzana ndi chifuniro chake. Mofanana ndi angelo onse a Mulungu, akerubi amachita zimene Yehova wasankha monga atumiki kapena kuti amithenga ake. (Sal. 104:4) Akamachita zimenezi, zimakhala ngati Yehova “wakhala” pamwamba pawo ndipo akuwatsogolera monga wolamulira wawo, ngati kuti ndi galeta limodzi lalikulu.

10. N’chiyani chikusonyeza kuti pagaleta lakumwambali pali angelo ambiri osati 4 okha?

10 Galeta likuimira zambiri osati akerubi okha. Akerubi amene Ezekieli anaona analipo 4. M’Baibulo nambala imeneyi nthawi zambiri imasonyeza kuti chinthu chimapezeka paliponse komanso kuti mbali zonse 4 za chinthu chinachake n’zofanana kapena kuti n’zokwanira. Choncho n’zomveka kunena kuti akerubi 4 amene analipowa, akuimira angelo onse okhulupirika a Yehova. Koma kumbukirani kuti mawilo komanso akerubiwo anali ndi maso paliponse. Zimenezi zikusonyeza kuti angelo onse, osati 4 okha, amakhala tcheru komanso maso nthawi zonse. Ndipotu mmene Ezekieli akulifotokozera galetalo zikusonyeza kuti ndi lalikulu kwambiri, zimene zikuchititsa kuti akerubiwo azioneka aang’ono. (Ezek. 1:18, 22; 10:12) Mofanana ndi zimenezi, mbali yakumwamba ya gulu la Yehova ndi yayikulu kwambiri kuposa akerubi 4.

Ezekieli anachita mantha ataona masomphenya a galeta lakumwamba la Yehova (Onani Ndime 8-10)

11. Kodi Danieli anaona masomphenya ati ofanana ndi a Ezekieli, nanga zimenezi zikutiuza chiyani?

11 Danieli nayenso anaona masomphenya akumwamba. Mneneri Danieli anakhala ku ukapolo ku Babulo kwa nthawi yayitali ndipo nayenso anaonetsedwa masomphenya akumwamba. N’zochititsa chidwi kuti m’masomphenya amenewonso mpando wachifumu wa Yehova unali ndi mawilo. Masomphenya amene Danieli anaona anafotokoza kwambiri za kukula kwa banja la Yehova lauzimu lakumwamba. Danieli anaona ana auzimu a Mulungu “okwana 1 miliyoni . . . ndi enanso 100 miliyoni,” ataima pa maso pa Yehova. Iwo amakhala ngati mmene anthu amakhalira m’bwalo la milandu ndipo aliyense amakhala pamalo amene anapatsidwa. (Dan. 7:9, 10, 13-18) Choncho n’zomveka kunena kuti masomphenya amene Ezekieli anaona akuimiranso gulu lauzimu komanso laulemerero lomweli.

12. Kodi kuphunzira nkhani zokhudza masomphenya a Ezekieli a galeta lakumwamba kungatiteteze bwanji?

12 Yehova amadziwa kuti anthufe timakhala otetezeka tikamaika maganizo athu pa zinthu zakumwamba zimene mtumwi Paulo anazifotokoza kuti ndi “zinthu zosaoneka.” Chifukwa chiyani amaona choncho? Chifukwa monga anthu, nthawi zambiri timakonda kuganizira kwambiri za zinthu “zooneka,” zimene ndi zinthu zimene timafuna pa moyo wathu zomwe n’zosakhalitsa. (Werengani 2 Akorinto 4:18.) Satana amapezerapo mwayi pamenepa ndipo amatipangitsa kuti tiziganizira kwambiri za zinthu zakuthupi. Kuti atithandize kupewa zimenezi, mwachikondi Yehova anatipatsa nkhani zimene timazipeza m’Baibulo ngati zimene zili muulosi wa Ezekieliwu. Nkhani zimenezi zimatikumbutsa za banja lakumwamba la Yehova lomwe ndi lalikulu kwambiri komanso lochititsa mantha.

“Mawilo Inu!”

13, 14. (a) Kodi mawilo amene Ezekieli anaona anawafotokoza bwanji? (b) N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti galeta la Yehova ili ndi mawilo?

13 Poyamba, Ezekieli anayamba kufotokoza za akerubi 4 ndipo m’Mutu 4 wa buku lino tidzaona zimene angelo amenewa komanso maonekedwe awo ochititsa chidwi akutiphunzitsa zokhudza Yehova. Komabe Ezekieli anaona mawiro 4 amene anali pambali pa akerubiwo. Zikuoneka kuti mawilowo anali kumbali zonse 4 ndipo anapanga chinthu chachikulu cha mbali 4 zofanana. (Werengani Ezekieli 1:16-18.) Zikuoneka kuti mawilowo anapangidwa ndi kulusolito umene ndi mwala wamtengo wapatali, woonekera mkati komanso wamtundu wachikasu kapena girini wopitira ku chikasu. Mwala wokongolawu unkachititsa kuti mawilowo aziwala kwambiri.

14 Masomphenya amene Ezekieli anaona amanena kwambiri za mawiro a galeta. N’zochititsa chidwi kuti akufotokoza za mpando wachifumu umene uli ndi mawiro, si choncho? Timaganiza kuti mpando wachifumu umayenera kukhala malo amodzi ndipo ndi mmene ziyenera kukhalira, chifukwa olamulira a dzikoli amakhala ndi mphamvu zolamulira m’dziko lawo lokha basi. Koma ulamuliro wa Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi ulamuliro uliwonse wa anthu. Mogwirizana ndi zimene Ezekieli anaona, ulamuliro wa Yehova ulibe malire. (Neh. 9:6) Kunena zoona Wolamulira Wamkulu ameneyu ali ndi mphamvu zolamulira kulikonse.

15. Kodi Ezekieli anazindikira chiyani chokhudza mmene mawilo anapangidwira komanso kukula kwake?

15 Ezekieli anachita mantha kwambiri ndi kukula kwa mawilo. Iye analemba kuti: “Malimu a mawilowo anali aatali kwambiri moti anali ochititsa mantha.” Mwina Ezekieli anachita kuyang’ana m’mwamba kuti athe kuona bwinobwino malimu akuluakuluwo. Ndiyeno iye anawonjezera mfundo ina yochititsa chidwi yakuti: “Malimu 4 onsewo anali ndi maso paliponse.” Mwina chimene chinali chochititsa chidwi kwambiri ndi mmene mawilowo ankaonekera. Iye anafotokoza kuti: “Anapangidwa mooneka ngati wilo lina lili pakati pa linzake.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

16, 17. (a) Kodi mungafotokoze bwanji mfundo yakuti mawilo a galetali anali ndi wilo lina mkati? (b) Kodi mawilowa akusonyeza kuti chimachitika n’chiyani galeta la Yehovali likafuna kusintha kolowera?

16 Zikuoneka kuti wilo lililonse limene Ezekieli anaona linapangidwa ndi mawilo awiri ophatikizana. Wilo limodzi linali mkati mwa wilo linzake mopingasa. N’chifukwa chake mawilo amenewa ankayenda ngati mmene Ezekieli anafotokozera kuti: “Mawilowo ankalowera kumbali iliyonse pambali zonse 4 ndipo sankafunika kuchita kukhota akamayenda.” Kodi mawilo amenewa akutiuza chiyani za galeta lakumwamba limene Ezekieli anaona?

17 Mawilo aakulu kwambiri ngati amenewa angathe kuyenda mtunda wautali akangozungulira kamodzi kokha. Ndipotu masomphenyawo akusonyeza kuti galetalo linkayenda mofulumira ngati mphezi. (Ezek. 1:14) Kuwonjezera pamenepo mawilowa ankayenda modabwitsa chifukwa ankatha kukhotera kulikonse. Mainjiniya amafuna kupanga mawilo ngati amenewa koma sangakwanitse. Galeta limeneli lingathe kusintha kolowera popanda kuchepetsa liwiro kapena kukhota. Koma sikuti limangoyenda mwachisawawa. Maso amene ali m’mawilo a galetali, akusonyezeratu kuti galetali limadziwa chilichonse chimene chikuchitika kulikonse kumene lingalowere.

Mawilo a galetali anali aakulu kwambiri ndipo ankathamanga pa liwiro lodabwitsa (Onani Ndime 17)

18. Kodi tikuphunzira chiyani tikaona kukula kwa mawilowo komanso kuchuluka kwa maso amene ali m’mawilowo?

18 Ndiye kodi Yehova ankamuphunzitsa chiyani Ezekieli komanso anthu okhulupirika zokhudza mbali yakumwamba ya gulu lake? Ganizirani zimene takambirana pofika pano. Kuwala kwa mawilo aja komanso kukula kwake, zikusonyeza kuti galetali ndi laulemerero komanso lochititsa mantha. Kuchuluka kwa maso amene ali m’mawilowo kukusonyeza kuti galetali limadziwa chilichonse. Maso a Yehova amaona zinthu zonse. (Miy. 15:3; Yer. 23:24) Komanso ali ndi angelo mamiliyoni ambiri amene amamutumikira ndipo angawatumize kulikonse kumene wafuna. Angelo amenewa amaonetsetsa chilichonse chimene chikuchitika ndipo amakafotokoza zimene aona kwa Wolamulira wawo wamkulu.​—Werengani Aheberi 1:13, 14.

Mawilo ake anawapanga m’njira yakuti galetalo lizitha kukhotera kulikonse mosavuta (Onani Ndime 17, 19)

19. Kodi liwiro komanso kukhota mosavuta kwa galeta la Yehova zikutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova ndi mbali yakumwamba ya gulu lake?

19 Komanso taona kuti galetali limathamanga mofulumira kwambiri komanso limatha kukhotera kulikonse. Taganizirani kusiyana kumene kulipo pakati pa mbali yakumwamba ya gulu la Yehova ndi maboma komanso mabungwe a anthu. Mosiyana ndi galetali, maboma ndi mabungwe amenewa sadziwa njira yothetsera mavuto amene anthu akukumana nawo m’dzikoli ndipo zinthu zikasintha iwo sadziwa zoyenera kuchita moti amakumana ndi mavuto ndipo adzawonongedwa. Koma galeta la Yehova limasonyeza kuti Mulungu amene akuliyendetsa ndi wololera komanso amatha kusintha. Mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, iye angathe kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse cholinga chake. (Eks. 3:13, 14) Mwachitsanzo angasinthe mofulumira n’kukhala Msilikali wamphamvu amene akumenya nkhondo poteteza anthu ake. Angasinthenso mwamsanga n’kukhala wachifundo komanso Wokhululukira machimo, amene akusamalira ndiponso kulimbikitsa anthu ochimwa omwe akudzimvera chisoni ndipo alapa.​—Sal. 30:5; Yes. 66:13.

20. N’chifukwa chiyani tikuyenera kulemekeza kwambiri galeta la Yehova?

20 Zimene taona pofika pano m’masomphenya a Ezekieli zingatipangitse kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimalemekeza galeta la Yehova?’ Tizikumbukira kuti galetali si loyerekezera koma ndi lenileni ndithu. Tisamaganize kuti Yehova, Mwana wake komanso angelo onse sakuona mavuto amene tikukumana nawo. Komanso tisamade nkhawa kuti Mulungu wathu achedwa kuchitapo kathu pa mavuto athu kapena kuti gulu lake lilephera kuthana ndi mavuto adzidzidzi amene tingakumane nawo m’dziko loipali. Tizikumbukira kuti gulu la Yehova silinaime, nthawi zonse limakhala likuyenda. Komanso Ezekieli anamva mawu kuchokera kumwamba akuti: “Mawilo inu!” Zikuoneka kuti amenewa anali mawu olamula kuti mawilowo ayambe kuyenda. (Ezek. 10:13) Timachita chidwi tikaganizira mmene Yehova amayendetsera gulu lake koma timamulemekeza kwambiri tikaganizira makhalidwe amene ali nawo.

Amene Akuyendetsa Galeta

21, 22. Kodi n’chiyani chimene chimapangitsa kuti mbali zosiyanasiyana za galetali zikhale zolumikizana?

21 Ezekieli akusiya kuganizira za mawilowo ndipo tsopano akuganizira zimene akuona pamwamba pake. Iye akuona “chinachake chooneka ngati thambo chimene . . . chinali chonyezimira ngati madzi oundana ochititsa chidwi.” (Ezek. 1:22) Pamwamba kwambiri pa mitu ya akerubi panayalidwa chinachake chooneka ngati thambo ndipo chinkanyezimira ngati galasi. Apatu munthu amene amadziwa mmene mashini amagwirira ntchito angakhale ndi mafunso ambiri okhudza galeta limeneli. Mwachitsanzo, ena angafunse kuti: ‘Kodi chooneka ngati thambocho chinalumikizidwa bwanji ndi mawilowo? Nanga mawilowo angagwire ntchito bwanji popanda zitsulo zowalumikizitsa? Kumbukirani kuti mmene galeta limeneli limagwirira ntchito ndi zosiyana ndi mmene magaleta apadziko lapansi pano amagwirira ntchito. Galetali ndi lophiphiritsira chifukwa likuimira zinthu zenizeni zimene zikuchitika kumwamba. Taonaninso mawu ochititsa chidwi awa: “Mzimu womwe unkatsogolera angelowo unkatsogoleranso mawilowo.” (Ezek. 1:20, 21) Kodi mzimu womwe unkatsogolera akerubi komanso mawilowo ndi uti?

22 N’zodziwikiratu kuti ndi mzimu woyera wa Yehova, umene ndi wamphamvu kwambiri kuposa china chilichonse m’chilengedwechi. Mzimu woyera ndi umene umachititsa kuti mbali zonse za galetali zikhale zolumikizana, umalipatsa mphamvu komanso umachititsa kuti liziyenda mwadongosolo kwambiri. Mogwirizana ndi zimene taonazi, tiyeni tikambirane za amene akuyendetsa galetalo amene Ezekieli akumuyang’anitsitsa.

Ezekieli ankafunika kupeza mawu abwino ofotokozera zinthu zimene anaona zomwe zinali zovuta kuzifotokoza

23. Kodi Ezekieli anagwiritsa ntchito mawu ati pofotokoza za Yehova, nanga n’chifukwa chiyani anagwiritsa ntchito mawu amenewo?

23 Werengani Ezekieli 1:26-28. Pofotokoza masomphenyawa, Ezekieli ankakonda kugwiritsa ntchito mawu angati awa, “chooneka ngati,” “wooneka ngati” komanso akuti “chinkaoneka ngati.” Koma m’mavesi amene tawerengawa wagwiritsa ntchito kwambiri mawu amenewa. Zikuoneka kuti ankafufuza mawu ofotokozera zinthu zovuta kufotokoza zimene anaona. Iye anaona “chinachake chooneka ngati mwala wa safiro ndipo chinkaonekanso ngati mpando wachifumu.” Kodi mukuganiza kuti mpando wachifumu wosemedwa pamwala umodzi waukulu wa buluu wa safiro unkaoneka bwanji? Pampando umenewo “panakhala winawake wooneka ngati munthu.”

24, 25. (a) Kodi utawaleza umene wazungulira mpando wachifumu wa Yehova umatikumbutsa za chiyani? (b) Kodi nthawi zina masomphenya ngati amenewa amakhudza bwanji amuna okhulupirika?

24 Zinali zovuta kuona bwinobwino munthu amene anakhala pampandopo, chifukwa ulemerero wa Yehova unkaoneka ngati malawi a moto kuchokera m’chiuno kupita pansi komanso kuchokera m’chiuno kupita m’mwamba. Mneneriyu ankafunika kutsinzina pang’ono komanso kuphimba maso ake ndi dzanja pamene amayang’anitsitsa munthu waulemereroyo. Pamapeto pake Ezekieli anaona zinthu zinanso zochititsa chidwi. Iye anati: “Pamalo onse omuzungulira panali powala ngati utawaleza umene ukuoneka mumtambo pa tsiku la mvula.” Kodi munayamba mwasangalalapo mutaona utawaleza? Utawalezawu umatikumbutsa kuti Mlengi wathu ndi waulemerero. Tikaona mitundu yosiyanasiyana ya utawaleza m’mwamba timakumbukiranso pangano la mtendere limene Yehova anapanga pambuyo pa Chigumula. (Gen. 9:11-16) Ngakhale kuti Mulungu ndi Wamphamvuyonse, iye ndi wamtendere. (Aheb. 13:20) Zonse zimene amaganiza zimakhala za mtendere ndipo mtendere umenewo umafalikira kwa onse amene amamulambira mokhulupirika.

Utawaleza wochititsa chidwi umene wazungulira mpando wachifumu wa Yehova umatikumbutsa kuti tikutumikira Mulungu wamtendere (Onani Ndime 24)

25 Kodi Ezekieli zinamukhudza bwanji ataona chithunzi cha ulemerero wa Yehova Mulungu? Ezekieli analemba zimene zinachitika. Iye anati: “Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi.” Ezekieli atagwidwa ndi mantha anagwada n’kuweramira pansi. Aneneri enanso anachita zomwezi ataona masomphenya ochokera kwa Yehova. Masomphenya oterewa ayenera kuti amakhala ochititsa mantha kwambiri. (Yes. 6:1-5; Dan. 10:8, 9; Chiv. 1:12-17) Koma pambuyo pake, amuna amenewa analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene Yehova anawaululira. Nayenso Ezekieli analimbikitsidwa. Ndiye kodi tizimva bwanji tikamawerenga nkhani za m’Malemba ngati zimenezi?

26. Kodi masomphenya amene Ezekieli anaona ayenera kuti anamulimbikitsa bwanji?

26 Ngati Ezekieli ankavutika mumtima chifukwa chosadziwa zimene zichitikire anthu a Mulungu ku Babuloko, masomphenya amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri. N’zoonekeratu kuti Mulungu akanathandiza anthu ake okhulupirika kaya ali ku Yerusalemu, ku Babulo kapena kwina kulikonse. Galeta lalikulu la Yehova lingafike kulikonse kumene iwo ali. Kodi Satana ali ndi mphamvu zolimbana ndi Mulungu amene akutsogolera gulu lakumwamba, laulemerero limeneli? (Werengani Salimo 118:6.) Ezekieli anaonanso kuti galeta lakumwambali silinali kutali ndi anthu. Tikutero chifukwa mawilo ake anafika padziko lapansi. (Ezek. 1:19) Choncho Yehova ankaganizira kwambiri anthu ake omwe anali ku ukapolo. Atate wawo wachikondi akanatha kuwathandiza kulikonse kumene akanakhala.

Kodi Galetali Likukukhudzani Bwanji?

27. Kodi masomphenya a Ezekieli akutanthauza chiyani kwa ife?

27 Kodi masomphenya a Ezekieliwa ali ndi tanthauzo lililonse kwa ife masiku ano? N’zosachita kufunsa. Musaiwale kuti Satana akupitiriza kuukira kulambira koyera. Iye akufuna kuti tizikhulupirira kuti tili tokha, kumalo amene Atate wathu wakumwamba komanso gulu lake sangafikeko. Musalole kuti mabodza amenewa akusokonezeni. (Sal. 139:7-12) Mofanana ndi Ezekieli, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kukhala ndi mantha. Sitingagwade n’kuwerama mpaka nkhope pansi ngati mmene iye anachitira. Koma ifenso tingadabwe ndiponso kuchita mantha tikaona mmene mbali yakumwamba ya gulu la Yehova limachitira zinthu. Mbali imeneyi ya gulu la Yehova ndi yamphamvu, yaliwiro, imakhotera kulikonse, imasintha mosavuta komanso ndi yaulemerero.

28, 29. N’chiyani chikusonyeza kuti galeta la Yehova lakhala likuyenda zaka 100 zapitazi?

28 Musaiwalenso kuti gulu la Yehova lili ndi mbali yapadziko lapansi. N’zoona kuti mbali yapadziko lapansili yapangidwa ndi anthu omwe si angwiro. Koma ganizirani zimene Yehova wachita padziko lapansi pano. Padziko lonse lapansi Yehova wathandiza anthu wamba kuti achite zinthu zimene sakanakwanitsa kuchita paokha. (Yoh. 14:12) Tikamawerenga buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira timatha kuona mmene ntchito yolalikira yakhala ikuyendera zaka 100 zapitazo. Tikudziwanso zimene gulu la Yehova lachita pophunzitsa Akhristu oona, kuwina milandu kukhoti komanso ngakhale kugwiritsa ntchito njira zamakono pochita zimene Mulungu amafuna.

29 Tikaganizira zonse zimene zachitika pobwezeretsa kulambira koyera m’masiku otsiriza a dziko loipali, n’zoonekeratu kuti galeta la Yehova likuyenda. Ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu limeneli komanso kutumikira Wolamulira Wamkulu ameneyu.​—Sal. 84:10.

Mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikupita patsogolo (Onani Ndime 28, 29)

30. Kodi tiphunzira chiyani m’mutu wotsatira?

30 Koma pali zambiri zimene tingaphunzire m’masomphenya a Ezekieli. M’mutu wotsatira, tikambirana mwatsatanetsatane za “angelo” 4 kapena kuti akerubi ochititsa chidwi amenewa. Kodi tingaphunzire chiyani kwa akerubi amenewa zokhudza Yehova Mulungu, yemwe ndi Mfumu waulemerero?

a Ezekieli ananena kuti anali siliva wosakanikirana ndi golide.

b Umenewu unali mtunda wochokera ku Yerusalemu kukafika ku Babulo. Koma zikuoneka kuti njira imene anthu ogwidwa ukapolowo anadutsa inali yaitali kuwirikiza maulendo awiri.