Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 6

“Mapeto Akufikira”

“Mapeto Akufikira”

EZEKIELI 7:3

MFUNDO YAIKULU: Mmene uthenga wa Yehova wa ziweruzo​—za Yerusalemu unakwaniritsidwira

1, 2. (a) Kodi Ezekieli anachita zinthu zodabwitsa ziti? (Onani chithunzi choyambirira) (b) Kodi zimene anachitazo zinkalosera chiyani?

 NKHANI yokhudza zinthu zodabwitsa zimene mneneri Ezekieli ankachita inafalikira mofulumira pakati pa Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo. Kwa mlungu umodzi Ezekieli anakhala pakati pawo atasokonezeka maganizo ndipo sankalankhula, koma kenako ananyamuka mwadzidzidzi n’kukadzitsekera m’nyumba. Anthu oyandikana nawo akuyang’anitsitsa modabwa, iye anatuluka m’nyumba mwake n’kunyamula njerwa ndi kuiika patsogolo pake kenako n’kujambulapo chithunzi mochita kugoba. Ndiyeno popanda kulankhula mawu aliwonse, Ezekieli anayamba kumanga mpanda waung’ono.​—Ezek. 3:10, 11, 15, 24-26; 4:1, 2.

2 Chiwerengero cha anthu amene ankaonerera zimenezi chiyenera kuti chinayamba kuwonjezereka ndipo mwina ankadzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Koma pambuyo pake, Ayuda amene anali ku ukapolowo anamvetsa kuti zinthu zodabwitsa zimene mneneri Ezekieli ankachita zimalosera zinthu zochititsa mantha zimene Yehova Mulungu adzachite posonyeza mkwiyo wake wolungama. Kodi zinthu zake zinali ziti? Nanga zinakhudza bwanji mtundu wakale wa Aisiraeli? Kodi zikukhudza bwanji anthu amene akulambira Mulungu woona masiku ano?

“Tenga Njerwa . . . Utenge Tirigu . . . Tenga Lupanga Lakuthwa”

3, 4. (a) Kodi Ezekieli anasonyeza ziweruzo zitatu ziti za Mulungu? (b) Kodi Ezekieli anachita chiyani pofuna kusonyeza kuti adani adzazungulira mzinda wa Yerusalemu?

3 Cha m’ma 613 B.C.E., Yehova anauza Ezekieli kuti achite zizindikiro zosonyeza njira zitatu zimene Mulungu adzaperekere ziweruzo pa Yerusalemu. Njira zake zinali: kuzunguliridwa kwa mzindawo, kuvutika kwa anthu okhala mumzindawo ndiponso kuwonongedwa kwa mzindawo komanso anthu ake. a Tiyeni tikambirane njira zimenezi mwatsatanetsatane.

4 Kuzunguliridwa kwa mzinda wa Yerusalemu. Yehova anauza Ezekieli kuti: “Tenga njerwa ndipo uiike patsogolo pako. . . . Umenye nkhondo ndi mzindawo.” (Werengani Ezekieli 4:1-3.) Njerwa inkaimira mzinda wa Yerusalemu pamene Ezekieliyo ankaimira gulu la nkhondo la a Babulo limene Yehova analigwiritsa ntchito. Ezekieli anauzidwanso kuti amange kampanda kakang’ono, malo okwera omenyerapo nkhondo komanso kuti apange zida zowonongera mzindawo. Kenako ankayenera kuika zinthu zimenezi kuzungulira njerwayo. Zinthu zimenezi zinkaimira zida za nkhondo zimene adani a Yerusalemu anagwiritsa ntchito pozungulira mzindawo ndi kuukira. Posonyeza kuti asilikali a adaniwo adzakhala amphamvu ngati chitsulo, Ezekieli ankayenera kuika “chiwaya” pakati pa iyeyo ndi mzindawo. Kenako ankayenera ‘kumayang’ana mzindawo monyansidwa.’ Zinthu zimene anachitazi zinali ngati “chizindikiro ku mtundu wa Isiraeli” chakuti pachitika zinthu zimene sankaziyembekezera. Yehova ankafuna kugwiritsa ntchito adani kuti awononge Yerusalemu, womwe unali mzinda wofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu chifukwa n’kumene kunali kachisi wa Mulungu.

5. Fotokozani zimene Ezekieli anachita posonyeza zimene zidzachitikire anthu okhala ku Yerusalemu.

5 Kuvutika kwa anthu okhala mu Yerusalemu. Yehova analamula Ezekieli kuti: “Utenge tirigu, balere, nyemba zikuluzikulu, mphodza, mapira ndi sipeloti [mtundu wina wa tirigu] . . . kuti zikhale chakudya chako,” ndipo “tsiku lililonse uzidzadya chakudya chochita kuyeza. Uzidzadya chakudya chokwana masekeli 20.” Kenako Yehova ananena kuti: “Ine ndidzachititsa kuti chakudya chisowe.” (Ezek. 4:9-16) Pa nthawiyi Ezekieli sakuimiranso gulu la asilikali ankhondo a Babulo, m’malomwake akuimira anthu amene akukhala ku Yerusalemu. Zimene Ezekieli anachitazi zinasonyeza kuti adani akadzaukira mzindawo kudzakhala njala ya dzaoneni. Pa nthawi imeneyo anthu adzaphika chakudya pogwiritsa ntchito zinthu zakalekale zimene zikusonyeza kuti anthu azidzadya chakudya chilichonse chimene chapezeka. Kodi njala imeneyi idzakhala yaikulu bwanji? Ezekieli akuyankha ngati kuti akuwauza anthu amene akukhala mu Yerusalemu kuti: “Azibambo amene ali mumzindawo adzadya ana awo ndipo ana adzadya abambo awo.” Pamapeto pake anthu ambiri adzavutika chifukwa cha ‘njala yomwe idzawaphe ngati mivi,’ ndipo anthu “adzaonda.”​—Ezek. 4:17; 5:10, 16.

6. (a) Kodi Ezekieli anachita zinthu ziwiri ziti pa nthawi imodzi? (b) Kodi lamulo la Mulungu lakuti ‘uyeze tsitsi, ukatero uligawe’ likusonyeza chiyani?

6 Kuwonongedwa kwa Yerusalemu komanso anthu ake. Zinthu za ulosi zimene Ezekieli akuchita pa nthawiyi zili ndi mbali ziwiri. Mbali yoyamba, Ezekieli akuchita zimene Yehova adzachite. Yehova anamuuza kuti: “Tenga lupanga lakuthwa kuti uligwiritse ntchito ngati lezala lometera.” (Werengani Ezekieli 5:1, 2.) Dzanja la Ezekieli limene linanyamula lupanga linkaimira dzanja la Yehova kapena kuti chiweruzo chake chimene anachipereka kudzera mwa asilikali a Babulo. Mbali yachiwiri, Ezekieli akusonyeza zimene Ayuda adzakumane nazo. Yehova anamuuza kuti: “Umete tsitsi lako ndi ndevu zako.” Kumeta tsitsi kumene Ezekieli anachita kunkaimira zimene zidzachitike Ayuda akadzaukiridwa n’kuphedwa. Komanso lamulo loti “utenge sikelo nʼkuyeza tsitsilo. Ukatero uligawe mʼmagawo atatu,” likutanthauza kuti Yehova sadzapereka chiweruzo pa Yerusalemu mwachisawawa koma adzachita kukonzekera ndipo adzachipereka mwadongosolo.

7. N’chifukwa chiyani Yehova anauza Ezekieli kuti agawe tsitsi m’magawo atatu komanso kuti gawo lililonse alichitire zosiyana ndi linzake?

 7 N’chifukwa chiyani Yehova anauza Ezekieli kuti agawe tsitsi limene anameta m’magawo atatu komanso kuti gawo lililonse alichitire zinthu zosiyana ndi linzake? (Werengani Ezekieli 5:7-12.) Ezekieli anawotcha gawo limodzi la tsitsilo “mumzindawo” pofuna kusonyeza anthu omwe ankaonerera kuti anthu ena okhala mu Yerusalemu adzafera mumzindamo. Kenako Ezekieli anatenga gawo lina la tsitsi lake n’kumalimenya ndi lupanga ‘akuzungulira mzindawo’ pofuna kusonyeza kuti anthu ena okhala mumzindawo adzaphedwa kunja kwa mzinda. Gawo lomaliza analiuluza ndi mphepo posonyeza kuti anthu ena okhala mumzindawo adzabalalika kupita kwa anthu amitundu ina koma ‘lupanga lidzawatsatira.’ Zimenezi zikusonyeza kuti kulikonse kumene anthu opulumukawo adzakhale sadzapeza mtendere.

8. (a) Kodi zinthu za ulosi zimene Ezekieli anachita zinapereka chiyembekezo chotani? (b) Kodi ulosi wokhudza “tsitsi lochepa” unakwaniritsidwa bwanji?

8 Komabe zinthu za ulosi zimene Ezekieli anachitazi zinaperekanso chiyembekezo. Ponena za tsitsi limene Ezekieli anameta lija, Yehova anauza mneneriyu kuti: “utengepo tsitsi lochepa nʼkulikulunga mʼzovala zako.” (Ezek. 5:3) Lamulo limeneli linasonyeza kuti Ayuda ochepa amene adzabalalikire m’mitundu ina, adzatetezeka. Lina mwa “tsitsi lochepa” limenelo, adzakhala Ayuda amene adzabwerere ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo ku Babulo pambuyo pa zaka 70. (Ezek. 6:8, 9; 11:17) Kodi ulosi umenewu unakwaniritsidwa? Inde. Patapita zaka zingapo Ayuda atachoka ku ukapolo ku Babulo, mneneri Hagai ananena kuti ena mwa Ayuda amene anabalalikira m’mitundu ina anabwereradi ku Yerusalemu. Ayuda amenewa anali “amuna achikulire amene anaona nyumba yoyambirira,” imene inali kachisi wa Solomo. (Ezara 3:12; Hag. 2:1-3) Yehova anaonetsetsa kuti kulambira koona kutetezeke mogwirizana ndi zimene analonjeza. M’Mutu 9 wa buku lino tidzakambirana zambiri zokhudza kubwezeretsa kumeneku.​—Ezek. 11:17-20.

Kodi Ulosi Umenewu Ukusonyeza Kuti M’tsogolo Mudzachitika Zotani?

9, 10. Kodi zinthu za ulosi zimene Ezekieli anachita zikutikumbutsa zinthu zapadera ziti zimene zichitike m’tsogolo?

9 Zinthu za ulosi zimene Ezekieli anachita zikutikumbutsa zinthu zofunika zimene Mawu a Mulungu ananeneratu kuti zidzachitika m’tsogolo. Kodi zina mwa zinthu zimenezi ndi ziti? Mofanana ndi zimene zinachitika ndi mzinda wakale wa Yerusalemu, Yehova adzagwiritsa ntchito magulu ankhondo am’dzikoli kuchita zinthu zimene anthu sanaziganizirepo. Magulu ankhondowo adzawononga mabungwe onse a zipembedzo zabodza amene ali padzikoli. (Chiv. 17:16-18) Kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu kunali “tsoka loti silinaonekepo.” Chimodzimodzi ndi “chisautso chachikulu” komanso nkhondo yake ya Aramagedo, chidzakhala chinthu choti “sichinachitikepo.”​—Ezek. 5:9; 7:5; Mat. 24:21.

10 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti anthu amene ali m’chipembedzo chabodza adzapulumuka mabungwe azipembedzo zabodzazo akamadzawonongedwa. Mwamantha, anthu amene adzapulumukewa adzagwirizana ndi anthu ena amene azidzafunafuna malo oti abisale. (Zek. 13:4-6; Chiv. 6:15-17) Zimene zidzawachitikirezi zikutikumbutsa zimene zinachitikira anthu omwe ankakhala mumzinda wakale wa Yerusalemu, amene anapulumuka pamene mzindawo unawonongedwa ndipo anauluzika “ndi mphepo.” Monga tinaonera  pandime 7, ngakhale kuti pa nthawi imeneyo anapulumuka, Yehova anasolola ‘lupanga n’kuwatsatira.’ (Ezek. 5:2) Mofanana ndi zimenezi, malo aliwonse omwe anthu amene adzapulumuke zipembedzo zikamadzawonongedwa adzathawireko, sadzawateteza ku lupanga la Yehova. Iwo adzaphedwa pa Aramagedo limodzi ndi anthu onse amene adzawaweruze kuti ndi mbuzi.​—Ezek. 7:4; Mat. 25:33, 41, 46; Chiv. 19:15, 18.

Nthawi ina tidzasiya kulengeza uthenga wabwino

11, 12. (a) Kodi kumvetsa ulosi wa Ezekieli wokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu kukutithandiza kuti tiziona bwanji utumiki wathu? (b) Kodi ntchito yathu yolalikira komanso uthenga wathu zidzasintha bwanji?

11 Kodi kumvetsa ulosi umenewu kukukhudza bwanji mmene timaonera utumiki wathu komanso changu chimene tiyenera kukhala nacho tikamachita utumikiwu? Ulosiwu ukutithandiza kuona kuti tikufunika kuyesetsa panopa kuti tithandize anthu kuti akhale atumiki a Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa nthawi imene yatsala kuti ‘tiphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira a Yesu’ ndi yochepa. (Mat. 28:19, 20; Ezek. 33:14-16) “Ndodo” (kapena kuti magulu ankhondo am’dzikoli) akadzayamba kuukira chipembedzo, sitizidzalalikiranso uthenga wachipulumutso. (Ezek. 7:10) Pa nkhani yolalikira uthenga wabwino tidzakhala chete ngati mmene Ezekieli anakhalira. Pa nthawi ina pamene ankachita utumiki wake iye anasiya kulengeza uthenga. (Ezek. 3:26, 27; 33:21, 22) N’zoona kuti pambuyo poti zipembedzo zabodza zawonongedwa, anthu adzasowa mtengo wogwira ndipo “azidzafuna kumva masomphenya kuchokera kwa mneneri,” koma sadzalandira malangizo aliwonse amene angadzawathandize kuti apulumuke. (Ezek. 7:26) Nthawi yoti alandire malangizo amenewo n’kukhala wophunzira wa Khristu idzakhala itadutsa.

12 Komabe ntchito yathu yolalikira siidzaima. Chifukwa chiyani tikutero? Pa nthawi ya chisautso chachikulu tikhoza kudzayamba kulengeza uthenga wachiweruzo umene udzakhale ngati mliri wa matalala. Uthenga umenewo udzakhala chizindikiro choonekeratu chakuti mapeto a dziko loipali afika.​—Chiv. 16:21.

“Akubwera Ndithu”

13. N’chifukwa chiyani Yehova anauza Ezekieli kuti agonere mbali yakumanzere kenako mbali yakumanja?

13 Atafotokoza ulosi wa mmene Yerusalemu adzawonongedwere, Ezekieli anachitanso zinthu zosonyeza nthawi imene zimenezi zidzachitike. Yehova anauza Ezekieli kuti agonere mbali ya kumanzere kwa masiku 390 komanso mbali ya kumanja kwa masiku 40. Tsiku limodzi linkaimira chaka. (Werengani Ezekieli 4:4-6; Num. 14:34) Zinthu zokhudza ulosi zimenezi, zimene Ezekieli ayenera kuti anazichita kwa nthawi yochepa tsiku lililonse, zikutifikitsa m’chaka chenicheni chimene Yerusalemu anawonongedwa. Zikuoneka kuti zaka 390 zimene Aisiraeli ankachita zolakwa zinayamba mu 997 B.C.E., chaka chimene ufumu wa mafuko 12 a Isiraeli unagawanika n’kukhala maufumu awiri. (1 Maf. 12:12-20) Zaka 40 zimene Ayuda ankachita zolakwa ziyenera kuti zinayamba mu 647 B.C.E. Chimenechi ndi chaka chomwe Yeremiya anasankhidwa kukhala mneneri kuti achenjeze ufumu wa Yuda mosapita m’mbali kuti udzawonongedwa. (Yer. 1:1, 2, 17-19; 19:3, 4) Choncho nthawi ziwiri zonsezi zinatha mu 607 B.C.E., chaka chenicheni chimene Yerusalemu anagwa n’kuwonongedwa, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena. b

Kodi Ezekieli anasonyeza bwanji chaka chenicheni chimene Yerusalemu adzawonongedwe? (Onani ndime 13)

14. (a) Kodi Ezekieli anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kuti Yehova amasunga nthawi? (b) Kodi n’chiyani chinachitika Yerusalemu asanawonongedwe?

14 N’kutheka kuti pa nthawi imene Ezekieli ankauzidwa ulosi wokhudza masiku 390 komanso masiku 40, sankadziwa chaka chenicheni chimene Yerusalemu adzawonongedwe. Komabe zaka zoti Yerusalemu awonongedwe zitayandikira, iye ankachenjeza Ayuda mobwerezabwereza kuti chiweruzo cha Yehova chikubwera. Iye ankalengeza kuti, ‘Mapeto akufikirani.’ (Werengani Ezekieli 7:3, 5-10.) Ezekieli sankakayikira kuti Yehova adzachita zinthu pa nthawi yake. (Yes. 46:10) Mneneriyu analoseranso zimene zidzachitike Yerusalemu asanawonongedwe. Iye anati: “Mʼdzikolo mudzakhala mavuto otsatizanatsatizana.” Mavuto amenewa adzapangitsa kuti makhalidwe a anthu, nkhani ya chipembedzo komanso ulamuliro zisokonekere.​—Ezek. 7:11-13, 25-27.

Yerusalemu atazunguliridwa anakhala ngati “mphika” umene waikidwa “pamoto” (Onani ndime 15)

15. Kodi ndi mbali ziti za ulosi wa Ezekieli zimene zinayamba kukwaniritsidwa mu 609 B.C.E. kupita m’tsogolo?

15 Patangodutsa zaka zochepa Ezekieli atalengeza kuti Yerusalemu adzawonongedwa, ulosiwo unayamba kukwaniritsidwa. Mu 609 B.C.E., Ezekieli anamva zoti adani ayamba kuukira mzinda wa Yerusalemu. Pa nthawiyi panamveka kulira kwa lipenga loitana anthu okhala mumzindawo kuti akauteteze, koma mogwirizana ndi zimene Ezekieli analosera, ‘palibe amene anapita kunkhondo.’ (Ezek. 7:14) Anthu okhala mu Yerusalemu sanasonkhane pamodzi kuti akamenyane ndi Ababulo n’kuteteza mzindawo. Ayuda ena ayenera kuti ankaganiza kuti Yehova awapulumutsa. Iye anachitapo zimenezo m’mbuyomo pamene Asuri ankafuna kuukira mzinda wa Yerusalemu, moti mngelo wa Yehova anapha asilikali awo ambiri. (2 Maf. 19:32) Koma pa nthawiyi Yehova sanatumize mngelo aliyense kuti awathandize. Pasanapite nthawi, mzinda womwe unazunguliridwa ndi adaniwo, unakhala ngati “mphika” umene waikidwa “pamoto” ndipo anthu okhala mumzindawo anali ngati “nyama” imene ili mumphikawo. (Ezek. 24:1-10) Mzinda wa Yerusalemu unazunguliridwa ndi adani kwa miyezi 18, kenako unawonongedwa.

“Unjikani Chuma Chanu Kumwamba”

16. Kodi masiku ano tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira kuti Yehova amasunga nthawi?

16 Kodi mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli ikutiphunzitsa chiyani? Kodi zikugwirizana ndi uthenga umene timalalikira komanso zimene anthu amachita akamva uthenga wathu? Yehova anasankhiratu nthawi imene zipembedzo zabodza zidzawonongedwe ndipo pa nkhani imeneyi Yehova adzasonyezanso kuti amachita zinthu pa nthawi yake. (2 Pet. 3:9, 10; Chiv. 7:1-3) Sitikudziwa tsiku lenileni limene zimenezi zidzachitike. Koma mofanana ndi Ezekieli tikupitiriza kuchita zimene Yehova watiuza, zoti tichenjeze anthu mobwerezabwereza kuti: ‘Mapeto akufikirani.’ N’chifukwa chiyani tikuyenera kulengeza uthenga umenewu mobwerezabwereza? Chifukwa chake ndi chofanana ndi chimene Ezekieli ankachitira zimenezi. c Anthu ambiri amene anawauza ulosi wochokera kwa Mulungu wakuti Yerusalemu adzawonongedwa, sanakhulupirire ulosiwo. (Ezek. 12:27, 28) Koma patapita nthawi, Ayuda ena omwe anali ku ukapolo ku Babulo anasonyeza mtima wabwino ndipo anabwerera kudziko lakwawo. (Yes. 49:8) Mofanana ndi zimenezi anthu ambiri masiku ano safuna kukhulupirira kuti dzikoli lidzatha. (2 Pet. 3:3, 4) Ngakhale zili choncho, tipitiriza kuthandiza anthu oona mtima kuti apeze njira ya kumoyo, nthawi yoti anthu amve uthenga wa Mulungu isanathe.​—Mat. 7:13, 14; 2 Akor. 6:2.

Ngakhale kuti anthu ambiri samvetsera uthenga wathu tikupitirizabe kufunafuna anthu oona mtima (Onani ndime 16)

N’chifukwa chiyani anthu okhala mu Yerusalemu wakale ‘anataya siliva wawo m’misewu’? (Onani ndime 17)

17. Kodi pa chisautso chachikulu tidzaona anthu akuchita zinthu ziti?

17 Ulosi wa Ezekieli ukutikumbutsanso kuti mabungwe a zipembedzo akadzawonongedwa, anthu amene ali m’zipembedzozo ‘sadzapita kunkhondo’ kuti ateteze zipembedzo zawo. M’malomwake akadzaona kuti palibe amene akuyankha kufuula kwawo koti “Ambuye, Ambuye,” “manja awo onse adzafooka” ndipo ‘azidzangonjenjemera.’ (Ezek. 7:3, 14, 17, 18; Mat. 7:21-23) Kodi adzachitanso chiyani? (Werengani Ezekieli 7:19-21.) Yehova akuti: “Siliva wawo adzamutaya mʼmisewu.” Mawu amenewa omwe akusonyeza zimene zinachitikira anthu amene ankakhala mu Yerusalemu wakale, akusonyezanso zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu. Pa nthawi imeneyo anthu adzazindikira kuti ndalama sizingawapulumutse ku tsoka limene likubwera.

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa ulosi wa Ezekieli pa nkhani yoika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba?

18 Kodi mukuona zimene tikuphunzirapo pa mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli? Phunziro lake ndi lakuti tiziika patsogolo zinthu zofunika kwambiri. Taganizirani izi: Anthu okhala mu Yerusalemu sankaika zinthu zofunika kwambiri patsogolo koma anasintha kwambiri atazindikira kuti mzinda wawo komanso moyo wawo watsala pang’ono kuwonongedwa ndipo chuma chawo sichingathe kuwapulumutsa. Iwo anataya chuma chawo n’kuyamba ‘kufunafuna kumva masomphenya kuchokera kwa mneneri.’ Koma anthuwo anasintha mochedwa kwambiri. (Ezek. 7:26) Mosiyana ndi Ayuda amenewa, ife tikudziwa kale kuti mapeto a dziko loipali ali pafupi. Choncho chifukwa choti timakhulupirira malonjezo a Mulungu, timaika zinthu zofunika kwambiri pa malo oyamba. Zimenezi zachititsa kuti tikhale akhama pofufuza chuma chauzimu chimene ndi chosatha ndipo sichidzataidwa “m’misewu.”​—Werengani Mateyu 6:19-21, 24.

19. Kodi uthenga wa ulosi umene Ezekieli ankalengeza ukutikhudza bwanji masiku ano?

19 Mwachidule, kodi tingati ulosi wa Ezekieli wokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu ukutikhudza bwanji masiku ano? Ukutikumbutsa kuti nthawi imene yatsala kuti tithandize anthu kuti akhale atumiki a Mulungu ndi yochepa. Choncho timaona kuti ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu tikuyenera kuigwira mwachangu. Timasangalala kwambiri anthu amitima yabwino akayamba kulambira Atate wathu Yehova. Komabe anthu amene sanayambe kulambira Atate wathu tikupitiriza kuwachenjeza, ngati mmene Ezekieli anachenjezera anthu a m’nthawi yake kuti: ‘Mapeto akufikirani.’ (Ezek 3:19, 21; 7:3) Pamene tikuchita zimenezi tikuyesetsa kuti tizikhulupirirabe Yehova komanso kuti tizilambira iye yekha pa moyo wathu.​—Sal. 52:7, 8; Miy. 11:28; Mat. 6:33.

a N’zomveka kunena kuti Ezekieli anachita zizindikiro zonsezi anthu akuonerera. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti pamene anamuuza kuti achite zinthu zina ngati kuphika chakudya komanso kunyamula katundu, Yehova analamula Ezekieli kuti achite zinthu zimenezi “iwo akuona.”​—Ezek. 4:12; 12:7.

b Polola kuti Yerusalemu awonongedwe, Yehova anapereka chiweruzo ku ufumu wa mafuko awiri wa Yuda komanso ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli. (Yer. 11:17; Ezek. 9:9, 10) Onani Insight on the Scriptures, Vol. 1, tsa. 462, “Chronology​—From 997 B.C.E. to Desolation of Jerusalem.”

c Onani kuti m’mavesi ochepa okha opezeka pa Ezekieli 7:5-7, Yehova anatchula mawu akuti “likubwera,” “kukubwera,” “akubwera” ndi “ikubwera” maulendo 5.