Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 14

“Ili ndi Lamulo Lokhudza Kachisi”

“Ili ndi Lamulo Lokhudza Kachisi”

EZEKIELI 43:12

MFUNDO YAIKULU: Masomphenya a kachisi​—zimene anthu a m’nthawi ya Ezekieli anaphunzira kuchokera ku masomphenyawa komanso zimene ifeyo tikuphunzirapo masiku ano

1, 2. (a) Kodi m’mutu wapitawu tinaphunzira chiyani chokhudza masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona? (b) Kodi tikambirana mafunso awiri ati m’mutu uno?

 EZEKIELI sanaone masomphenya a kachisi wamkulu wauzimu amene Paulo anamufotokoza patapita zaka zambiri. Tinaphunzira zimenezi m’mutu wapitawu. Tinaphunziranso kuti cholinga cha masomphenyawa n’kuphunzitsa anthu a Mulungu kufunika kotsatira mfundo za Mulungu pa kulambira koyera. Anthuwo akanakhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova pokhapokha ngati akanatsatira mfundo zimenezi. N’chifukwa chake tikuona kuti Yehova anatsindika kawiri mfundo yofunika muvesi limodzi. Mfundo yake ndi yakuti: “Ili ndi lamulo lokhudza kachisi.”​—Werengani Ezekieli 43:12.

2 Tsopano tiyeni tikambirane mafunso ena awiri. Loyamba: Kodi anthu a m’nthawi ya Ezekieli anaphunzira zinthu zapadera ziti m’masomphenyawa zokhudza mfundo za Yehova pa nkhani yakulambira koyera? Yankho la funso limeneli litithandiza kuyankha funso lachiwiri lakuti: Kodi masomphenyawa akutanthauza chiyani kwa ife m’masiku otsiriza ovuta ano?

Kodi Anthu a M’nthawi ya Ezekieli Anaphunzira Chiyani M’masomphenyawa?

3. Kodi mfundo yakuti zimene Ezekieli anaona m’masomphenya zinkachitikira paphiri lalitali, zinapangitsa bwanji anthu kuti achite manyazi?

3 Kuti tiyankhe funso loyambali, tiyeni tikambirane zinthu zingapo zochititsa chidwi m’masomphenya a kachisiwa. Phiri lalitali. Anthu ayenera kuti ankayerekezera malo amene Ezekieli anaona m’masomphenyawa ndi ulosi wobwezeretsa wokhudza mtima umene Yesaya ananena. (Yes. 2:2) Koma kodi anaphunzira chiyani ataona nyumba ya Yehova ili pamwamba pa mapiri ataliatali choncho? Anaphunzira kuti kulambira koyera kuyenera kukhala pamwamba, kokwezeka komanso kwapamwamba kuposa china chilichonse. Ndipotu kulambira koyera kuyenera kukhala kokwezeka chifukwa amene anakuyambitsa ndi “wokwezeka kwambiri kuposa milungu ina yonse.” (Sal. 97:9) Koma anthu sankachita mbali yawo polimbikitsa kulambira koyera. Kwa zaka zambiri, iwo mobwerezabwereza anakhala akudetsa, kusiya komanso kuipitsa kulambira koyera. Kuona nyumba ya Yehova itakwezedwa n’kuikidwa pamwamba, pa malo aulemerero komanso apamwamba amene imayenera kukhala, kunachititsa kuti anthu a mtima wabwino achite manyazi.

4, 5. Kodi anthu amene ankamvetsera masomphenya a Ezekieli anaphunzira chiyani pa mageti ataliatali a kachisi?

4 Mageti ataliatali. Kumayambiriro kwa masomphenyawa, Ezekieli anaona mngelo amene amamuonetsa kachisi uja, akuyeza mageti. Mageti amenewa anali aatali pafupifupi mamita 30. (Ezek. 40:14) M’magetiwa munali zipinda za alonda. Kodi onse amene anaona zimenezi pa pulani ya kachisiyo anaphunzirapo chiyani? Yehova anauza Ezekieli kuti: “Uonetsetse khomo lolowera mʼkachisi.” Chifukwa chiyani anamuuza zimenezi? Chifukwa chakuti anthu ankabweretsa anthu “osachita mdulidwe wamumtima ndi mdulidwe wa khungu lawo,” n’kuwalowetsa m’nyumba yopatulika yolambirira Mulungu. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yehova ananena kuti, “iwo amadetsa kachisi wanga.”​—Ezek. 44:5, 7.

5 Anthu amene ‘sanachite mdulidwe wa khungu lawo,’ analephera kumvera lamulo lomveka bwino lochokera kwa Mulungu limene anthu anakhala akulitsatira kuyambira nthawi ya Abulahamu. (Gen. 17:9, 10; Lev. 12:1-3) Koma anthu amene anali “asanachite mdulidwe wamumtima” anali ndi vuto lalikulu kwambiri. Anali ouma mtima komanso opanduka ndipo sankamvera malangizo ndi malamulo ochokera kwa Yehova. Anthu amenewo sankayenera kuloledwa kuti alowe m’nyumba yopatulika yolambirira Yehova. Yehova amadana ndi chinyengo koma anthu ake analola kuti chinyengocho chimere mizu m’nyumba yake. Mageti komanso zipinda za alonda za m’masomphenya a kachisiyo, zinapereka phunziro lomveka bwino lakuti: Zimenezi ziyenera kutheratu. Aliyense ankayenera kutsatira mfundo zapamwamba kuti alowe m’nyumba ya Mulungu. Zimenezi zikanathandiza kuti Yehova adalitse kulambira kwa anthuwo.

6, 7. (a) Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji mpanda umene unazungulira malo akachisi popereka uthenga kwa anthu ake? (b) Kodi anthu a Yehova ankachita chiyani ndi nyumba yake m’mbuyomo? (Onani mawu am’munsi.)

6 Mpanda umene unazungulira malo a kachisiyo. Chinthu china chochititsa chidwi chokhudza masomphenya a kachisiwa chinali mpanda umene unazungulira malo onse pamene panali kachisiyu. Ezekieli ananena kuti mpandawo unali wautali mabango 500 mbali zonse kapena kuti mamita 1,555 omwe ndi makilomita pafupifupi 1.6. (Ezek. 42:15-20) Komatu nyumba ya kachisiyo ndi mabwalo ake zinali pa malo amene anali okwana mikono 500 yokha mbali zonse kapena mamita 259 mbali iliyonse. Choncho kuzungulira kachisiyo panali malo aakulu ndipo malowo anali ku mpandawo. a Kodi malowo anali antchito yanji?

7 Yehova ananena kuti: “Tsopano asiye kuchita zauhule ndi milungu ina ndipo achotse mitembo ya mafumu awo nʼkukaiika kutali ndi ine. Akatero ine ndidzakhala pakati pawo mpaka kalekale.” (Ezek. 43:9) Zikuoneka kuti “mitembo ya mafumu awo,” inkaimira kulambira mafano. Choncho tinganene kuti Yehova anagwiritsa ntchito malo aakulu a m’masomphenya a Ezekieli a kachisi ponena kuti: “Zonyansa zonsezi muziike kutali. Zisayandikire kuno.” Choncho ngati anthuwo akanayesetsa kuti kulambira kwawo kukhale koyera, Yehova akanawadalitsa pokhala pakati pawo.

8, 9. Kodi anthu ayenera kuti anaphunzira chiyani pa malangizo amphamvu amene Yehova anapereka kwa amuna audindo?

8 Malangizo amphamvu kwa amuna audindo. Yehova anaperekanso malangizo amphamvu koma achikondi kwa amuna omwe anali ndi udindo pakati pa anthuwo. Anadzudzula mwamphamvu Alevi amene anatalikirana kwambiri ndi Mulungu pamene anthu anayamba kulambira mafano. Koma anayamikira ana a Zadoki ‘amene ankagwira ntchito zapamalo ake opatulika pa nthawi imene Aisiraeli anachoka kwa iye.’ Gulu lililonse analichitira zinthu mwachilungamo komanso mwachifundo mogwirizana ndi zochita zawo. (Ezek. 44:10, 12-16) Mofanana ndi zimenezi nawonso atsogoleri a Isiraeli anadzudzulidwa mwamphamvu.​—Ezek. 45:9.

9 Pochita zimenezi Yehova anasonyeza kuti amuna amene anali ndi udindo komanso oyang’anira ankayenera kuyankha kwa iye mmene akuchitira ndi udindo wawo. Iwo ankafunika kulangizidwa, kudzudzulidwa komanso kupatsidwa chilango. Zimenezi zikusonyeza kuti ankayenera kutsogolera anthu powalimbikitsa kuti azitsatira mfundo za Yehova.

10, 11. Kodi pali umboni wotani umene ukusonyeza kuti ena mwa anthu amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo anaphunzirapo kanthu pa masomphenya amene Ezekieli anaona?

10 Kodi anthu amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo anagwiritsa ntchito zimene anaphunzira kuchokera m’masomphenya a Ezekieli? N’zoona kuti sitingadziwe zonse zokhudza zimene amuna ndi akazi okhulupirika a m’nthawi ya Ezekieli ankaganiza zokhudza masomphenya ochititsa chidwiwa. Komabe Mawu a Mulungu amatiuza zambiri zokhudza zimene anthu amene anabwerera kwawowo anachita komanso mmene ankaonera kulambira Yehova m’njira yovomerezeka. Kodi iwo ankatsatira mfundo zimene anaphunzira m’masomphenya a Ezekieli? Ankatsatira ndithu, makamaka tikayerekezera ndi makolo awo amene anapandukira Mulungu, Ayuda asanatengedwe kupita ku ukapolo ku Babulo.

11 Amuna okhulupirika ngati mneneri Hagai komanso Zekariya, Ezara amene anali wansembe ndiponso wokopera malemba komanso bwanamkubwa Nehemiya, onsewa anagwira ntchito mwakhama yophunzitsa anthu mfundo ngati zimene zinali m’masomphenya a Ezekieli a kachisi. (Ezara 5:1, 2) Iwo ankaphunzitsa anthu kuti kulambira koyera kuyenera kukwezedwa komanso kuti kuyenera kukhala pamalo oyamba kuposa chuma komanso zinthu zina zimene timafuna. (Hag. 1:3, 4) Iwo ankalimbikitsa anthu kuti azilemekeza mfundo zimene akuyenera kutsatira pa kulambira koyera. Mwachitsanzo, Ezara ndi Nehemiya analamula anthu mwamphamvu kuti achotse akazi awo achilendo amene ankafooketsa anthu mwauzimu. (Werengani Ezara 10:10, 11; Neh. 13:23-27, 30) Nanga bwanji pankhani ya kulambira mafano? Zikuoneka kuti Ayuda atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo, anayamba kudana ndi tchimo limeneli, limene m’mbuyomu linkawatchera msampha mobwerezabwereza. Nanga bwanji za ansembe, atsogoleri komanso akalonga? Monga mmene masomphenya a Ezekieli akusonyezera, iwo anali m’gulu la anthu amene analandira uphungu komanso malangizo ochokera kwa Yehova. (Neh. 13:22, 28) Anthu ambiri anamvera malangizo amenewo modzichepetsa.​—Ezara 10:7-9, 12-14; Neh. 9:1-3, 38.

Nehemiya anaphunzitsa anthu zokhudza kulambira koyera pamene ankagwira nawo ntchito limodzi (Onani ndime 11)

12. Kodi anthu amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo Yehova anawadalitsa m’njira ziti?

12 Chifukwa cha zimenezi Yehova anadalitsa anthu ake. Anthu ankasangalala chifukwa anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, anali ndi thanzi labwino komanso ankakhala mwabata zimene zinali zisanachitikepo kwa nthawi yaitali. (Ezara 6:19-22; Neh. 8:9-12; 12:27-30, 43) N’chifukwa chiyani zinali chonchi? Chifukwa chakuti anthuwo anayamba kutsatira mfundo za Yehova zolungama pa nkhani ya kulambira koyera. Mfundo zimene anaphunzira m’masomphenya a kachisi, zinathandiza anthu ambiri omwe anali ndi mtima wabwino. Choncho mwachidule tinganene kuti masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi anathandiza Ayuda amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo m’njira ziwiri zofunika. (1) Anaphunzira zimene angachite kuti azitsatira mfundo zokhudza kulambira koyera komanso mmene angalimbikitsire ena kuti azitsatira mfundo zimenezi. (2) Masomphenyawo anawapatsa ulosi wolimbikitsa. M’masomphenyawa munali ulosi wakuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa komanso analosera mmene Yehova adzadalitsire anthu ake ngati angapitirize kumachita zinthu zokhudzana ndi kulambira koyera. Komabe ifenso masiku ano tingafune kudziwa kuti: Kodi masomphenyawa akukwaniritsidwanso panopa?

Zimene Masomphenya a Ezekieli Amatiphunzitsa Masiku Ano

13, 14. (a) Tikudziwa bwanji kuti masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona akukwaniritsidwa masiku ano? (b) Kodi masomphenyawa akutithandiza m’njira ziwiri ziti masiku ano? (Onani bokosi 13A lakuti, “Akachisi Osiyana Omwe Akufotokoza Zinthu Zosiyana.”)

13 Kodi tingakhale otsimikiza kuti masomphenya a Ezekieli akutikhudza ifeyo masiku ano? Inde. Kumbukirani kufanana kumene kulipo pakati pa masomphenya a Ezekieli okhudza nyumba yopatulika ya Mulungu imene ili pamwamba ‘pa phiri lalitali kwambiri,’ ndi ulosi wa Yesaya umene umanena kuti “phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu.” Yesaya akutiuza mosapita m’mbali kuti ulosi wake udzakwaniritsidwa “m’masiku otsiriza.” (Ezek. 40:2; Yes. 2:2-4; onaninso Mika 4:1-4.) Apa tinganene kuti maulosiwa akunena zimene zikuchitika m’masiku otsiriza kungoyambira mu 1919, pamene kulambira koyera kunabwezeretsedwa ngati kuti kwaikidwa paphiri lalitali. b

14 Choncho kunena mosapita m’mbali, masomphenya a Ezekieli akukhudza kulambira koyera masiku ano. Monga mmene masomphenyawo anathandizira Ayuda amene anachokera ku ukapolo, akuthandizanso ifeyo masiku ano m’njira ziwiri. (1) Akutiuza zimene tingachite kuti tilimbikitse mfundo za Mulungu zokhudza kulambira koyera. (2) Akutipatsa ulosi umene ukutitsimikizira kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa ndipo Yehova adzatidalitsa.

Mfundo Zimene Tikuyenera Kutsatira Masiku ano pa Kulambira Koyera

15. Kodi tizikumbukira chiyani tikamaona zimene tikuphunzira m’masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona?

15 Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene Ezekieli anaona m’masomphenya. Yerekezerani kuti tikuyendera limodzi ndi Ezekieli pamene akukamuonetsa kachisi m’masomphenyawo. Kumbukirani kuti sitikuona kachisi wamkulu wauzimu, koma tikungofuna kuona zomwe tingaphunzire zimene tingazigwiritse ntchito pa kulambira koyera masiku ano. Kodi zina zimene tikuphunzirapo ndi ziti?

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa ntchito yoyeza imene inachitika m’masomphenya a Ezekieli? (Onani chithunzi choyambirira.)

16 N’chifukwa chiyani anayeza zinthu zosiyanasiyana? Ezekieli ankaonerera pamene mngelo yemwe ankaoneka ngati kopa ankayeza kachisi, mpanda wake, mageti, zipinda za alonda, mabwalo komanso guwa lansembe. Munthu amene akuwerenga angadabwe ndi kuchuluka kwa zinthu zimene anayeza. (Ezek. 40:1–42:20; 43:13, 14) Komabe taganizirani za mfundo zofunika zimene tikuphunzirapo pamenepa. Pochita zimenezi Yehova akutsindika mwamphamvu kufunika kwa mfundo zake. Iye ndi amene anakhazikitsa mfundozo osati anthu. Anthu amene amanena kuti tingathe kulambira Mulungu m’njira iliyonse akulakwitsa kwambiri. Kuwonjezera pamenepo poyeza kachisi mwatsatanetsatane, Yehova anatsimikizira kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa ndithu. Kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu n’kotsimikizirika ngati miyezo imeneyo. Pamenepa Ezekieli anatsimikizira kuti kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera m’masiku otsiriza ano ndi kotsimikizirika.

Kodi mukuphunzira chiyani mukaganizira miyezo imene anapeza atayeza kachisi? (Onani ndime 16)

17. Kodi mpanda umene unazungulira kachisi ukutikumbutsa chiyani masiku ano?

17 Mpanda. Takambirana kale kuti Ezekieli anaona mpanda umene unazungulira malo onse a kachisi amene anaona m’masomphenya. Mpanda umenewu unkakumbutsa anthu a Mulungu kuti akuyenera kuika kutali zinthu zonse zokhudzana ndi kulambira, zimene zingaipitse kulambira koyera kuti nyumba ya Mulungu isadetsedwe. (Werengani Ezekieli 43:7-9.) Malangizo amenewo ndi ofunikanso kwa ife masiku ano. Anthu a Mulungu atamasulidwa ku ukapolo wauzimu wa Babulo Wamkulu, kumene anakhalako kwa nthawi yaitali, Khristu anasankha kapolo wokhulupirika komanso wanzeru mu 1919. Kungoyambira nthawi imeneyo, anthu a Mulungu ayesetsa mwakhama kuchotsa ziphunzitso zabodza ndi miyambo yokhudzana ndi kulambira mafano komanso chipembedzo chachikunja. Tikuyesetsa mwakhama kuti tipewe chilichonse chimene chingadetse kulambira koyera. Kuwonjezera pamenepo sitichita malonda m’Nyumba za Ufumu. Timaonetsetsa kuti zimenezi sitikuziphatikiza ndi kulambira koyera.​—Maliko 11:15, 16.

18, 19. (a) Kodi mageti ataliatali amene Ezekieli anaona m’masomphenya akutiphunzitsa chiyani? (b) Kodi tinganene chiyani kwa anthu amene amaona kuti mfundo zapamwamba za Yehova n’zosathandiza? Perekani chitsanzo.

18 Mageti ataliatali. Kodi tikuphunzira chiyani tikamaganizira mageti ataliatali amene Ezekieli anaona? Mosakaikira mageti amene Ezekieli anaona m’masomphenya a kachisi anaphunzitsa Ayuda amene anachokera ku ukapolo kuti Yehova ali ndi mfundo za makhalidwe abwino zapamwamba kwambiri. Ngati zimenezi zinali choncho kalelo, kuli bwanji masiku ano? Tikulambira mu kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. Kodi sitinganene kuti makhalidwe olungama opanda chinyengo ndi ofunikanso kwambiri panopa? (Aroma 12:9; 1 Pet. 1:14, 15) M’masiku otsiriza ano, Yehova akutsogolera anthu ake kuti azitsatira kwambiri mfundo zake zamakhalidwe abwino. c Mwachitsanzo munthu woipa amene sakulapa amachotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:11-13) Kuwonjezera pamenepo, zipinda za alonda zimene zinali pageti zikutikumbutsa kuti masiku ano pa nkhani yolambira Yehova, munthu wosavomerezedwa ndi Mulungu saloledwa kulowa m’kachisi wake. Mwachitsanzo, munthu amene ali ndi moyo wachiphamaso, angalowe m’Nyumba ya Ufumu koma Yehova sangasangalale naye pokhapokha atayamba kuchita zimene Mulungu amafuna. (Yak. 4:8) Zimenezitu n’zofunika kwambiri kuti kulambira koyera kutetezeke pa nthawi ino, imene anthu ambiri akuchita makhalidwe oipa.

19 Baibulo linaneneratu kuti makhalidwe a anthu m’dzikoli adzaipa kwambiri mapeto asanafike. Mwachitsanzo timawerenga kuti, “anthu oipa ndi achinyengo adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.” (2 Tim. 3:13) Anthu ambiri masiku ano akusocheretsedwa ndipo akuganiza kuti mfundo zapamwamba za Yehova ndi zopanikiza kwambiri, ndi zachikale kapena kuti zolakwika. Kodi inunso musocheretsedwa? Mwachitsanzo, kodi mungavomereze munthu wina atakuuzani kuti mfundo za Mulungu zokhudza anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha ndi zolakwika? Kapena kodi mungakhale kumbali ya Yehova Mulungu amene Mawu ake amanena mosapita m’mbali kuti amene amachita zimenezi ‘akuchita zinthu zonyansa’? Mulungu amatichenjeza kuti tisamasangalale ndi makhalidwe onyansa. (Aroma 1:24-27, 32) Tikakumana ndi nkhani ngati zimenezi, tingachite bwino kuganizira masomphenya a Ezekieli a kachisi ndi mageti ake ataliataliwo n’kumakumbukira kuti: Yehova satsitsa mfundo zake zolungama ngakhale kuti dziko loipali likukakamiza anthu ake kuti azichita zoipa. Kodi ifenso timayendera mfundo za Atate wathu wakumwamba n’kumachita zinthu zomwe ndi zoyenera?

Timapereka nsembe zotamanda Mulungu tikamachita nawo zinthu zokhudza kulambira koyera

20. Kodi a “khamu lalikulu” amapeza mfundo zolimbikitsa ziti m’masomphenya a Ezekieli?

20 Mabwalo. Ezekieli ataona bwalo la kunja kwa kachisi lomwe linali lalikulu, ayenera kuti anadabwa kwambiri ndipo n’kutheka kuti ankaganiza za kuchuluka kwa anthu olambira Yehova amene angasonkhane m’bwalo limeneli. Masiku ano Akhristu amalambira Mulungu m’malo oyera kwambiri. A “khamu lalikulu” amene akulambira Mulungu m’bwalo lakunja la kachisi wauzimu wa Yehova, amapeza mfundo zolimbikitsa m’masomphenya a Ezekieli. (Chiv. 7:9, 10, 14, 15) Ezekieli anaona kuti m’mabwalowa munali zipinda zodyera zomwe anthu amene ankalambira Mulungu ankadyeramo nsembe zamgwirizano zimene ankabweretsa. (Ezek. 40:17) Tinganene kuti ankadyera limodzi ndi Yehova Mulungu chomwe ndi chizindikiro choti anali naye pa ubwenzi komanso pamtendere. Masiku ano sitipereka nsembe ngati mmene Ayuda amene ankatsatira Chilamulo cha Mose ankachitira. Koma timapereka nsembe ‘zotamanda Mulungu.’ Timachita zimenezi tikamachita zinthu zokhudzana ndi kulambira koyera monga kupereka ndemanga pofotokoza chikhulupiriro chathu pamisonkhano kapena tikamagwira ntchito yolalikira. (Aheb. 13:15) Timasangalalanso ndi chakudya chauzimu chomwe Yehova amatipatsa. Mpake kuti timamva ngati mmene anamvera ana a Kora amene anaimbira Yehova kuti: “Kukhala tsiku limodzi mʼmabwalo anu nʼkwabwino kuposa kukhala kwinakwake masiku 1,000.”​—Sal. 84:10.

21. Kodi Akhristu odzozedwa angaphunzire chiyani kwa ansembe a m’masomphenya a Ezekieli?

21 Ansembe. Ezekieli anaona kuti mageti amene ansembe komanso Alevi ankagwiritsa ntchito akamalowa m’bwalo lamkati, anali ofanana ndi mageti amene mafuko omwe sanali ansembe ankagwiritsa ntchito akamalowa m’bwalo lakunja. Imeneyi inali njira yabwino yokumbutsira ansembewo kuti nawonso ankayenera kukwaniritsa mfundo za Yehova zokhudza kulambira koyera. Nanga bwanji masiku ano? Pakati pa anthu a Yehova masiku ano palibe fuko la ansembe. Koma Akhristu odzozedwa amauzidwa kuti: “Inu ndi ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu.’” (1 Pet. 2:9) Mu Isiraeli wakale, ansembe ankalambira m’bwalo lapadera. Masiku ano Akhristu odzozedwa salekanitsidwa ndi olambira anzawo mwanjira iliyonse koma amasangalala ndi mgwirizano wapadera umene ali nawo ndi Yehova chifukwa anawatenga kukhala ana ake. (Agal. 4:4-6) Komanso Akhristu odzozedwa amapeza mfundo zothandiza m’masomphenya a Ezekieli. Mwachitsanzo, amaona kuti ansembe ankapatsidwa malangizo komanso chilango. Akhristu tonse tiyenera kukumbukira kuti tili ‘m’gulu limodzi’ la nkhosa ndipo tikutumikira moyang’aniridwa ndi ‘mʼbusa mmodzi.’—Werengani Yohane 10:16.

22, 23. (a) Kodi akulu Achikhristu masiku ano angaphunzire chiyani kuchokera kwa atsogoleri amene afotokozedwa m’masomphenya a Ezekieli? (b) Kodi n’chiyani chimene chingadzachitike m’tsogolo?

22 Mtsogoleri. Masomphenya a Ezekieli akusonyeza kuti mtsogoleri anali munthu wodalirika. Iye sanali wa fuko la ansembe ndipo akafika pakachisi ankayenera kutsatira malangizo ochokera kwa ansembe. Koma n’zoonekeratu kuti anali ngati mtsogoleri pakati pa anthu ndipo ankathandiza anthuwo popereka nsembe. (Ezek. 44:2, 3; 45:16, 17; 46:2) Choncho iye ndi chitsanzo chabwino kwa amuna Achikhristu masiku ano amene ali ndi udindo mumpingo. Ndipotu akulu mumpingo wa Chikhristu kuphatikizapo oyang’anira madera, akuyenera kugonjera kapolo wokhulupirika. (Aheb. 13:17) Akulu amayesetsa mwakhama kuthandiza anthu a Mulungu kuti azipereka nsembe zotamanda Mulungu pamisonkhano yampingo komanso muutumiki. (Aef. 4:11, 12) Komanso akulu ayenera kuphunzirapo kanthu akaona mmene Yehova anadzudzulira atsogoleri a Isiraeli chifukwa chogwiritsa ntchito udindo wawo molakwika. (Ezek. 45:9) Mofanana ndi zimenezi, akulu sayenera kuganiza kuti si oyenera kulandira uphungu komanso malangizo. Mosiyana ndi zimenezi, akulu amasangalala ndi mwayi wophunzitsidwa ndi Yehova n’cholinga choti akhale abusa komanso oyang’anira abwino kwambiri.​—Werengani 1 Petulo 5:1-3.

23 M’dziko lapansi la paradaiso, Yehova adzapitiriza kutipatsa oyang’anira oyenerera komanso achikondi. Tinganene kuti akulu ambiri masiku ano akuphunzitsidwa mmene angadzakhalire abusa othandiza komanso oyenerera m’Paradaiso. (Sal. 45:16) N’zosangalatsatu kwambiri tikamaganizira mmene amuna amenewa adzatithandizire m’dziko latsopano. Pa nthawi yoyenera ya Yehova tidzamvetsa bwino masomphenya a Ezekieli mofanana ndi maulosi ena okhudza kubwezeretsa. Mwina zinthu zina zimene panopa sitingazimvetse tidzaona zikukwaniritsidwa m’tsogolo. Nthawi idzafika.

Kodi mageti ataliatali komanso mabwalo akutiphunzitsa chiyani zokhudza kulambira? (Onani ndime 18-21)

Yehova Akudalitsa Kulambira Koyera

24, 25. Kodi masomphenya a Ezekieli anasonyeza bwanji kuti Yehova adzadalitsa anthu ake omwe akulimbikitsa kulambira koyera?

24 Pomaliza, tiyeni tikambirane chinthu china chachikulu chimene chikuchitika m’masomphenya a Ezekieli. Yehova akubwera m’kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya ndipo akulonjeza anthu ake kuti adzakhala nawobe, ngati anthuwo adzatsatira mokhulupirika mfundo zokhudza kulambira koyera. (Ezek. 43:4-9) Kodi kupezeka kwa Yehova m’kachisiyu kunakhudza bwanji anthuwo komanso dziko lawo?

25 Masomphenyawo akufotokoza mmene Mulungu anadalitsira anthu ake pogwiritsa ntchito mafanizo awiri a ulosi: (1) Mtsinje ukuyenda kuchokera m’kachisi ndipo ukubweretsa moyo ndi nthaka yachonde. (2) Dzikolo linagawidwa mwadongosolo ndipo kachisi ndi mabwalo ake anaikidwa pakati penipeni. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani masiku ano? Tikukhala m’nthawi imene Yehova walowa, kuyeretsa komanso kuvomereza kachisi wamkulu wauzimu, yomwe ndi njira yopatulika kwambiri ya kulambira. (Mal. 3:1-4) M’mutu 19 mpaka 21 wa buku lino tidzambirana mafanizo awiri aulosi amenewa.

a Choncho Yehova ankasiyanitsa mmene anthu ake anachitira ndi nyumba yake yopatulika m’mbuyomo ponena kuti: “Iwo anaipitsa dzina langa loyera chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anachita pamene anaika khomo lawo pafupi ndi khomo langa, nʼkuika felemu la khomo lawo pafupi ndi felemu la khomo langa moti pakati pa iwowo ndi ine nʼkungokhala khoma lokha lotisiyanitsa.” (Ezek. 43:8) Kale ku Yerusalemu, mpanda wokha ndi umene unkasiyanitsa kachisi wa Yehova ndi nyumba za anthu. Anthu atasiya kutsatira mfundo zolungama za Yehova, anabweretsa zinthu zonyansa zomwe ndi kulambira mafano pafupi ndi nyumba ya Yehova. Zimenezo zinali zosaloleka.

b Masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona, akugwirizananso ndi maulosi ena okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera amene akukwaniritsidwa m’masiku otsiriza ano. Mwachitsanzo, onani kufanana komwe kulipo pakati pa Ezekieli 43:1-9 ndi Malaki 3:1-5 komanso Ezekieli 47:1-12 ndi Yoweli 3:18.

c Kachisi wauzimu anayamba kugwira ntchito koyamba mu 29 C.E., pamene Yesu anabatizidwa n’kuyamba ntchito yake ngati Mkulu wa Ansembe. Koma kulambira koyera kunanyalanyazidwa kwa nthawi yaitali padziko lapansi atumwi onse a Yesu atamwalira. Kuyambira mu 1919 m’pamene kulambira koyera kunakwezedwa.