Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 16

“Ulembe Chizindikiro Pazipumi”

“Ulembe Chizindikiro Pazipumi”

EZEKIELI 9:4

MFUNDO YAIKULU: Mmene anthu okhulupirika a m’nthawi ya Ezekieli anawalembera chizindikiro kuti adzapulumuke komanso zimene kuika chizindikiro kukutanthauza masiku ano

1-3. (a) N’chifukwa chiyani Ezekieli anali wodabwa ndipo anauzidwa chiyani zokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

 EZEKIELI anadabwa kwambiri. Anali atangoona masomphenya a zinthu zonyansa zimene Ayuda opanduka ankachita m’kachisi ku Yerusalemu. a Anthu opandukawa anaipitsa malo amene anali likulu la kulambira koyera mu Isiraeli. Koma anthuwo sanaipitse kachisi yekha. Dziko la Yuda linali litadzaza ndi zachiwawa ndipo linali loti silingabwererenso mwakale. Yehova atakwiya kwambiri ndi zinthu zimene anthu ake osankhidwawo ankachita, anauza Ezekieli kuti: “Ndidzawalanga nditakwiya kwambiri.”​—Ezek. 8:17, 18.

2 Ezekieli ayenera kuti zinam’pweteka kwambiri atadziwa kuti Yehova wakwiyira Yerusalemu ndi kachisi wake, amene poyamba anali wopatulika komanso atadziwa kuti mzindawu udzawonongedwa. N’kutheka kuti Ezekieli ankadzifunsa kuti: ‘Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire anthu okhulupirika omwe ali mumzindawu? Kodi adzapulumuka? Ngati ndi choncho, kodi adzapulumuka bwanji? Sipanapite nthawi yaitali kuti Ezekieli apeze mayankho a mafunso amenewa. Atangomva chiweruzo champhamvu chimene chidzaperekedwe kwa Yerusalemu, anamva mawu ofuula akuitana anthu opereka chilango cha Mulungu. (Ezek. 9:1) Pamene masomphenyawo ankapitirira, mneneriyu anamva mfundo ina imene inamulimbikitsa yakuti chiweruzocho sichidzaperekedwa kwa anthu onse. Iye anamva kuti mzindawo ukamadzawonongedwa anthu ena adzapulumuka.

3 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, ifenso tingamadzifunse kuti, kodi ndi ndani amene adzapulumuke chiwonongeko chachikulu chimene chikubwerachi? Tsopano tiyeni tikambirane mafunso awa: (1) Kodi kenako Ezekieli anaona chiyani m’masomphenyawo? (2) Kodi masomphenyawo anakwaniritsidwa bwanji m’nthawi ya Ezekieli? (3) Kodi masomphenyawo akutanthauza chiyani masiku ano?

“Itana Anthu Amene Akuyenera Kupereka Chilango”

4. Fotokozani zimene kenako Ezekieli anamva ndi kuona m’masomphenya.

4 Kodi kenako Ezekieli anaona ndi kumva chiyani m’masomphenyawo? (Werengani Ezekieli 9:1-11.) Panabwera amuna 7 “kuchokera kugeti lakumtunda loyangʼana kumpoto,” mwina pafupi ndi pamene panali chizindikiro cha nsanje kapena pafupi ndi pamene akazi ankalirira mulungu wotchedwa Tamuzi. (Ezek. 8:3, 14) Amuna 7 amenewo analowa m’bwalo lamkati la kachisi ndipo anaima pafupi ndi guwa lansembe lakopa. Koma amunawa sanapite kumeneko kukapereka nsembe. Pa nthawi imeneyo Yehova anali atasiya kulandira nsembe zimene zinkaperekedwa pakachisipo. Amuna 6 mwa amuna amenewo anaima pamenepo “aliyense atanyamula chida chake chowonongera.” Koma mwamuna wa 7 anali wosiyana kwambiri ndi amuna enawa. Mwamuna ameneyu anavala zovala zansalu ndipo sananyamule chida chilichonse koma ananyamula “kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki.”

5, 6. Kodi tinganene kuti chinachitika n’chiyani ndi anthu amene analembedwa chizindikiro? (Onani chithunzi choyambirira.)

5 Kodi munthu ameneyu amene anali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ankafunika kuchita chiyani? Yehova anamupatsa ntchito yaikulu pamene anamuuza kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse wa Yerusalemu ndipo ulembe chizindikiro pazipumi za anthu amene akuusa moyo komanso kubuula chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.” Mwina pa nthawiyo Ezekieli anakumbukira makolo okhulupirika a Chiisiraeli, amene anapaka magazi pafelemu lapamwamba pa chitseko komanso pamafelemu awiri am’mbali mwa khomo kuti chikhale chizindikiro chothandiza kuti ana awo oyamba kubadwa asaphedwe. (Eks. 12:7, 22, 23) M’masomphenya a Ezekieli, kodi chizindikiro chimene munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki anaika pazipumi za anthu chikugwira ntchito yofanana ndi imeneyi? Kodi zikusonyeza kuti munthu amene ali ndi chizindikirochi adzapulumuka Yerusalemu akamadzawonongedwa?

6 Tingamvetse bwino yankho la funsoli tikaganizira cholinga cha chizindikirochi. Munthuyo ankayenera kulemba chizindikirochi pazipumi za anthu amene “akuusa moyo komanso kubuula” chifukwa cha zonyansa zonse zimene zinkachitika “mumzindawu.” Ndiye kodi tinganene chiyani za anthu amene analembedwa chizindikiro? Choyamba, anthuwo anali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha kulambira mafano kumene kunkachitika pakachisi komanso chifukwa cha zinthu zachiwawa, zachiwerewere komanso zachinyengo zimene zinadzaza mu Yerusalemu. (Ezek. 22:9-12) Kuwonjezera pamenepo, zikuoneka kuti anthuwo sanabise mmene ankamvera. Mosakayikira, zimene anthu amitima yabwinowo ananena komanso kuchita zinasonyeza kuti ankaipidwa ndi zimene zinkachitika m’dziko lawo komanso zinasonyeza kuti anali odzipereka pa kulambira koyera. Chifukwa chakuti Yehova ndi wachifundo adzapulumutsa anthu amitima yabwino amenewa.

7, 8. Kodi amuna amene anali ndi zida zowonongera ankayenera kuchita chiyani pokwaniritsa ntchito imene anawapatsa, nanga zotsatirapo zake zinali zotani?

7 Koma kodi amuna 6 omwe anali ndi zida zowonongera akanagwira bwanji ntchito yawo? Ezekieli anamva malangizo amene Yehova ankawapatsa akuti: Tsatirani munthu amene ali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndipo mukaphe aliyense kupatulapo amene ali ndi chizindikiro pachipumi. Yehova anawauza kuti: “Muyambire pamalo anga opatulika.” (Ezek. 9:6) Opha anthuwo ankayenera kuyambira ku kachisi, amene anali malo ofunika kwambiri ku Yerusalemu, omwe pa nthawiyi sanalinso oyera pamaso pa Yehova. Anthu oyambirira kuphedwa anali “akuluakulu amene anali kutsogolo kwa nyumbayo,” akulu 70 a mu Isiraeli amene anali m’kachisi ndipo ankapereka nsembe zofukiza kwa milungu yabodza.​—Ezek. 8:11, 12; 9:6.

8 Kodi zotsatira zake zinali zotani? Ezekieli anapitiriza kuona komanso kumvetsera pamene munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi uja ankapereka lipoti kwa Yehova kuti: “Ndachita zonse zimene munandilamula.” (Ezek. 9:11) Ndiye tingafunse kuti: ‘Kodi anthu amene ankakhala mu Yerusalemu zinthu zinawathera bwanji? Kodi panali anthu aliwonse okhulupirika amene anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa?’

Kodi Masomphenyawa Anakwaniritsidwa Bwanji M’nthawi ya Ezekieli?

9, 10. Kodi ena mwa anthu amene anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa ndi ati, nanga tinganene chiyani za anthu amenewo?

9 Werengani 2 Mbiri 36:17-20. Ulosi wa Ezekieli unakwaniritsidwa mu 607 B.C.E., pamene asilikali a Babulo anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake. Mofanana ndi ‘kapu mʼdzanja la Yehova,’ a Babulo anali ngati chida cha Yehova chimene anachigwiritsa ntchito popereka chilango kwa anthu osakhulupirika mu Yerusalemu. (Yer. 51:7) Kodi popereka chiweruzocho anapha aliyense? Ayi. Masomphenya a Ezekieli ananeneratu kuti padzakhala ena amene sadzaphedwa ndi a Babulo.​—Gen. 18:22-33; 2 Pet. 2:9.

10 Anthu ena okhulupirika anapulumuka kuphatikizapo Arekabu, Ebedi-meleki wa ku Itiyopiya, mneneri Yeremiya ndi mlembi wake Baruki. (Yer. 35:1-19; 39:15-18; 45:1-5) Malinga ndi zimene tikuona m’masomphenya a Ezekieliwa, tinganene kuti anthu amenewa ‘ankausa moyo komanso kubuula’ chifukwa cha zonyansa zonse zimene zinkachitika mu Yerusalemu. (Ezek. 9:4) Mosakaikira mzindawo usanawonongedwe, anthuwa anasonyeza kuti ankadana ndi zinthu zoipa komanso anali odzipereka pa kulambira koyera ndipo zimenezi zinachititsa kuti apulumuke.

11. Kodi amuna 6 amene anali ndi zida zowonongera komanso munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki, akuimira ndani?

11 Kodi anthu okhulupirikawa ankafunika kulembedwa chizindikiro chenicheni kuti apulumuke? Palibe mneneri aliyense, ngakhale Ezekieli, amene anayendayenda mu Yerusalemu n’kumalemba chizindikiro pazipumi za anthu okhulupirika. Choncho masomphenya a Ezekieli akusonyeza zinthu zimene zinkachitika kumwamba zimene anthu sakanatha kuziona ndi maso awo. Munthu amene ananyamula kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki komanso amuna 6 omwe anali ndi zida zowonongera, akuimira angelo okhulupirika a Yehova amene nthawi zonse amakhala okonzeka kuchita zimene iye akufuna. (Sal. 103:20, 21) N’zoonekeratu kuti Yehova anagwiritsa ntchito angelo kuti atsogolere pa ntchito yopereka chiweruzo kwa anthu osakhulupirika mu Yerusalemu. Angelowo anaonetsetsa kuti chiweruzocho chaperekedwa kwa anthu oyenera osati kungopha anthu mwachisawawa. Zimenezi zinali ngati kuika chizindikiro pazipumi za anthu amene amayenera kupulumuka.

Kodi Masomphenya a Ezekieli Ali ndi Tanthauzo Lotani Masiku Ano?

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anatsanulira mkwiyo wake pa Yerusalemu, nanga n’chifukwa chiyani tikuyenera kuyembekezera zofanana ndi zimenezi masiku ano? (b) Kodi Yerusalemu amene anali wosakhulupirika akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu? Fotokozani. (Onani bokosi lakuti “Kodi Yerusalemu Ankaimira Matchalitchi Amene Amati ndi a Chikhristu?”)

12 Masiku anonso tikuyembekezera kuti Mulungu apereka chiweruzo chimene sanaperekepo chiyambire. “Pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko mpaka lero, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:21) Pamene tikuyembekezera chiweruzo chimenechi tingamadzifunse kuti: Kodi pa chiweruzochi anthu sadzaphedwa mwachisawawa? Kodi anthu amene akulambira Yehova m’njira yovomerezeka adzaikidwa chizindikiro mwa njira inayake kuti apulumuke? M’mawu ena, tinganene kuti kodi masomphenya a Ezekieli a munthu amene anali ndi kachikwama konyamulira inki akukwaniritsidwa masiku ano? Yankho la mafunso atatu onsewa ndi lakuti inde. N’chifukwa chiyani tikuyankha choncho? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyeni tionenso masomphenya a Ezekieli aja.

13 Kodi mukukumbukira chifukwa chake Yehova anakwiyira Yerusalemu wakale? Onaninso lemba la Ezekieli 9:8, 9. (Werengani.) Ezekieli atadandaula kuti chiweruzocho chidzawonongeratu “anthu onse amene anatsala mu Isiraeli,” Yehova anapereka zifukwa 4 zimene ankayenera kuperekera chiweruzocho. Choyamba, “zolakwa” za Aisiraeli zinali ‘zazikulu kwambiri.’ b Chachiwiri, dziko la Yuda linali ‘litadzaza ndi kukhetsa magazi.’ Chachitatu, Yerusalemu amene anali likulu la ufumu wa Yuda, anali ‘atadzaza ndi zinthu zopanda chilungamo.’ Cha 4, anthuwo akamachita zoipazo ankadzikhululukira n’kumanena kuti Yehova “sakuona” zoipa zimene ankachitazo. Mawu amenewa akusonyezanso mmene zinthu zaipira masiku ano. Anthu akuchita makhalidwe oipa, zachiwawa, zinthu zopanda chilungamo komanso ndi osakhulupirika. Popeza kuti Yehova “sasintha,” zimene zinapangitsa kuti akwiye mu nthawi ya Ezekieli, ndi zimenenso zikumukwiyitsa masiku ano. (Yak. 1:17; Mal. 3:6) Choncho tingayembekezere kuti amuna 6 amene anali ndi zida zowonongera aja komanso munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki alinso ndi ntchito yaikulu yoti agwire masiku ano.

Amuna 6 amene ali ndi zida zowonongera akhala ndi ntchito yoti achite posachedwapa (Onani ndime 12, 13)

14, 15. Ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova amachenjeza anthu nthawi yoti awawononge isanafike?

14 Ndiye kodi masomphenya a ulosi a Ezekieli akukwaniritsidwa bwanji masiku ano? Tikaona mmene masomphenyawa anakwaniritsidwira m’mbuyomu, tingathe kudziwa zimene zichitike panopa komanso m’tsogolo. Taganizirani zinthu zina zimene zachitika kapena zimene zidzachitike pokwaniritsa ulosi wa Ezekieli.

15 Yehova amachenjeza anthu asanapereke chiweruzo. Monga mmene tinaonera m’Mutu 11 wa bukuli, Yehova anatuma Ezekieli kuti akakhale “mlonda wa nyumba ya Isiraeli.” (Ezek. 3:17-19) Kuyambira mu 613 B.C.E., Ezekieli anachenjeza Aisiraeli mosapita m’mbali za chiwonongeko chimene chinkabwera. Aneneri enanso kuphatikizapo Yesaya ndi Yeremiya nawonso ankachenjeza anthu za tsoka limene lidzagwere Yerusalemu. (Yes. 39:6, 7; Yer. 25:8, 9, 11) Masiku ano Yehova kudzera mwa Khristu, wagwiritsa ntchito kagulu kakang’ono ka atumiki ake odzozedwa kuti azipereka chakudya pa nthawi yake kwa antchito ake apakhomo komanso kuti azichenjeza ena za chisautso chachikulu chimene chikuyandikira kwambiri.​—Mat. 24:45.

16. Kodi ifeyo monga anthu a Yehova timalemba anthu chizindikiro kuti adzapulumuke? Fotokozani.

16 Anthu a Yehova salemba zizindikiro pazipumi za anthu amene adzapulumuke. Kumbukirani kuti Ezekieli sanauzidwe kuti ayendeyende mu Yerusalemu n’kumalemba zizindikiro pazipumi za anthu kuti adzapulumuke. Mofanana ndi zimenezi, anthu a Yehova masiku ano sanapatsidwe ntchito yoti azilemba zizindikiro pazipumi za anthu amene akuyenera kudzapulumuka. M’malomwake, monga antchito apakhomo m’nyumba yauzimu ya Khristu, tapatsidwa ntchito yolalikira. Tikamagwira mwakhama ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu komanso kuchenjeza anthu kuti dziko loipali latsala pang’ono kuwonongedwa, timasonyeza kuti timaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri. (Mat. 24:14; 28:18-20) Choncho tili ndi udindo wothandiza anthu oona mtima kuti ayambe kulambira koyera.​—1 Tim. 4:16.

17. Kodi anthu akuyenera kuchita chiyani panopa kuti akhale m’gulu la anthu amene adzaikidwe chizindikiro m’tsogolo?

17 Kuti anthu adzapulumuke pa nthawi imene oipa azidzawonongedwa akuyenera kusonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro panopa. Monga mmene taonera kale, anthu amene anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa mu 607 B.C.E., anasonyeza nthawiyo isanafike kuti ankadana ndi zoipa komanso kuti anali odzipereka pa kulambira koyera. N’chimodzimodzinso masiku ano. Chiwonongeko chisanafike anthu akuyenera ‘kuusa moyo komanso kubuula’ kapena kuti kumva chisoni mumtima mwawo chifukwa cha zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli. M’malo mobisa mmene akumvera mumtima mwawo, akuyenera kusonyeza mwa zochita komanso zolankhula zawo kuti ndi odzipereka pa kulambira koyera. Kodi angachite bwanji zimenezi? Akuyenera kumvetsera uthenga wabwino umene ukulalikidwa masiku ano n’kuchitapo kathu, akuyenera kupitiriza kutsanzira makhalidwe a Khristu, akuyenera kubatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova komanso akuyenera kuthandiza abale ake a Khristu mokhulupirika. (Ezek. 9:4; Mat. 25:34-40; Aef. 4:22-24; 1 Pet. 3:21) Anthu okhawo amene akuchita zimenezi masiku ano, amene adzadutse pa chisautso chachikulu monga olambira oona, ndi amene adzaikidwe chizindikiro kuti apulumuke.

18. (a) Kodi Yesu Khristu adzaika bwanji chizindikiro pa anthu oyenerera, nanga adzawaika liti chizindikirocho? (b) Kodi Akhristu odzozedwa okhulupirika akufunikanso kulembedwa chizindikiro? Fotokozani.

18 Yesu ndi amene adzalembe chizindikiro anthu amene akuyenera kupulumuka. M’nthawi ya Ezekieli, angelo anagwira ntchito yolemba chizindikiro anthu okhulupirika kuti adzapulumuke. Pa kukwaniritsidwa kwa ulosiwu masiku ano, munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi koikamo inki akuimira Yesu Khristu “akadzabwera mu ulemerero wake,” monga woweruza wa mitundu yonse. (Mat. 25:31-33) Kubwera kwa Yesu kumeneku kudzachitika pa chisautso chachikulu pambuyo poti chipembedzo chabodza chawonongedwa. c Pa nthawi yovuta imeneyo Aramagedo itatsala pang’ono kuyamba, Yesu adzaweruza anthu kuti ndi nkhosa kapena mbuzi. A “khamu lalikulu” adzaweruzidwa kapena kuti kulembedwa chizindikiro kuti ndi nkhosa. Zimenezi zidzasonyeza kuti akuyenera ‘kupita kumoyo wosatha.’ (Chiv. 7:9-14; Mat. 25:34-40, 46) Nanga chidzachitike n’chiyani kwa odzozedwa okhulupirika? Iwo sakuyenera kulembedwa chizindikiro kuti adzapulumuke pa Aramagedo. M’malomwake, adzaikidwa chidindo chomaliza asanafe kapena chisautso chachikulu chisanayambe. Ndiyeno pa nthawi ina Aramagedo isanayambe, adzaukitsidwa n’kupita kumwamba.​—Chiv. 7:1-3.

19. Kodi ndi ndani amene adzabwere ndi Yesu kudzapereka chiweruzo padziko loipali? (Onani bokosi lakuti “Kuusa Moyo ndi Kubuula, Kulemba Zizindikiro Komanso Kuphwanya​—Kodi Zimenezi Zidzachitika Liti?”)

19 Yesu Khristu yemwe ndi mfumu yakumwamba ndi magulu ake ankhondo akumwamba adzapereka chiweruzo padziko loipali. M’masomphenya a Ezekieli, amuna 6 amene anali ndi zida zowonongera aja sanayambe ntchito yawo yowononga mpaka munthu wovala zovala za nsalu atamaliza ntchito yake yolemba zizindikiro. (Ezek. 9:4-7) Mofanana ndi zimenezi, chiwonongeko chimene chikubweracho chidzayambika Yesu akadzamaliza kuweruza anthu onse amitundu ina komanso kulemba chizindikiro pa nkhosa kuti zidzapulumuke. Ndiye mkati mwa nkhondo ya Aramagedo, Yesu adzatsogolera gulu lankhondo lakumwamba lopereka chiweruzo, limene ndi angelo oyera komanso a 144,000 onse amene adzalamulire naye limodzi. Amenewa adzapereka chiweruzo padziko loipali n’kuliwonongeratu ndipo adzapulumutsa anthu amene akulambira Mulungu m’njira yovomerezeka, n’kuwalowetsa m’dziko lapansi lolungama.​—Chiv. 16:14-16; 19:11-21.

20. Kodi taphunzira mfundo zolimbikitsa ziti m’masomphenya a Ezekieli a munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki?

20 Tikuyamikira kwambiri mfundo zolimbikitsa zimene tikuphunzira m’masomphenya a Ezekieli a munthu amene anali ndi kachikwama ka mlembi koikamo inki. Tingakhale otsimikiza kuti Yehova sadzawononga anthu olungama limodzi ndi anthu oipa. (Sal. 97:10) Tikudziwa zimene tikuyenera kuchita panopa kuti tilembedwe chizindikiro kuti m’tsogolo tidzapulumuke. Monga olambira a Yehova, tikufunitsitsa kugwira nawo ntchito yolengeza uthenga wabwino ndi kuchenjeza anthu amene akuusa moyo ndi kubuula chifukwa cha zoipa zimene zikuchitika m’dziko la Satanali. Tikamachita zimenezi tingathe kuthandiza anthu amene ali ‘ndi maganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha’ kuti agwirizane nafe pa kulambira koyera. Zimenezi zingathandize kuti adzaikidwe chizindikiro chowathandiza kuti apulumuke n’kulowa m’dziko lapansi lolungama la Mulungu.​—Mac. 13:48.

a Masomphenya amene Ezekieli anaona a zinthu zoipa zimene zinkachitika kukachisi, afotokozedwa m’Mutu 5 wa bukuli.

b Malinga ndi zimene buku lina limanena, mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “cholakwa” angatanthauze zinthu “zoipa kwambiri.” Buku lina limanena kuti mawu amenewa “akukhudzana kwambiri ndi zachipembedzo ndipo pafupifupi nthawi zonse amasonyeza kuti munthu ali ndi mlandu pamaso pa Mulungu chifukwa cha makhalidwe ake oipa.”

c Zikuoneka kuti Babulo Wamkulu akamadzawonongedwa sizikutanthauza kuti anthu onse omwe ali m’zipembedzo zabodza adzaphedwa. Pa nthawiyo, ngakhale atsogoleri ena azipembedzo angadzachoke m’zipembedzo zawo n’kumanena kuti sanali m’zipembedzo zimenezo.​—Zek. 13:3-6.