Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 21

“Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”

“Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”

EZEKIELI 48:35

MFUNDO YAIKULU: Tanthauzo la mzinda komanso chopereka

1, 2. (a) Kodi ndi gawo lapadera liti la dziko, limene ankafunika kulipatula? (Onani chithunzi chapachikuto.) (b) Kodi masomphenyawa anawatsimikizira chiyani anthu omwe anali ku ukapolo?

 M’MASOMPHENYA ake omaliza, Ezekieli anauzidwa za gawo lina la malo amene akuyenera kudzapatulidwa kuti adzagwire ntchito ina yapadera. Malo opatulidwawo sanali oti adzaperekedwe kwa fuko lina la Isiraeli ngati cholowa chawo, koma anali oti aperekedwe kwa Yehova ngati chopereka. Ezekieli anauzidwanso za mzinda wina umene unali ndi dzina lochititsa chidwi. Mbali imeneyi ya masomphenya inalimbikitsa kwambiri Ayuda amene anali ku ukapolo chifukwa inawatsimikizira kuti Yehova adzakhala nawo akadzabwerera kudziko lawo limene ankalikonda.

2 Ezekieli anafotokoza momveka bwino za chopereka chimenechi. Tiyeni tikambirane nkhani imeneyi chifukwa ili ndi mfundo zolimbikitsa kwambiri kwa ife amene timalambira Yehova m’njira yovomerezeka.

“Chopereka Chopatulika Ndiponso Malo a Mzinda”

3. Kodi malo amene Yehova anapatula anali ndi mbali 5 ziti, nanga ntchito ya mbali zimenezo inali yotani? (Onani bokosi lakuti “Gawo Loti Likhale Chopereka Chanu.”)

3 Malo apaderawa anali okwana mikono 25,000 (makilomita 13) kuchokera kumpoto kukafika kum’mwera komanso mikono 25,000 kuchoka kum’mawa kukafika kumadzulo. Malo amenewa anali ofanana mbali zonse ndipo ankatchedwa kuti “malo onse oti aperekedwe.” Malowa anagawidwa m’magawo atatu. Gawo lakumtunda linali la Alevi, gawo lapakati linapatulidwa kuti likhale la kachisi komanso ansembe. Magawo onse awiriwa ndi amene ankapanga “chopereka chopatulika.” Gawo laling’ono limene linali m’munsi kapena kuti “malo otsala,” anali “oti munthu aliyense angagwiritse ntchito.” Malo amenewa anali a mzinda.​—Ezek. 48:15, 20.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yokhudza chopereka kwa Yehova?

4 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi yokhudza chopereka kwa Yehova? Yehova anayamba ndi kupatula malo a chopereka chapadera kenako malo a mafuko. Pochita zimenezi iye anasonyeza kuti chofunika kwambiri chinali malo amene amakhudza kulambira koyera. (Ezek. 45:1) Mosakayikira, Ayuda amene anali ku ukapolowo anaphunzira zambiri pa dongosolo limeneli la mmene anagawira dzikoli. Ankayenera kuika patsogolo nkhani yokhudza kulambira Yehova pa moyo wawo. Masiku anonso timaona kuti zinthu zokhudza kulambira, monga kuphunzira Mawu a Mulungu, kupita ku misonkhano ya Chikhristu komanso kugwira nawo ntchito yolalikira ndi zofunika kwambiri. Tikamatsanzira chitsanzo cha Yehova choika zinthu zofunika pamalo oyamba, timasonyeza kuti timaona kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu ndi kulambira Yehova.

“Mzinda Ukhale Pakati pa Malowa”

5, 6. (a) Kodi mzinda unali wa ndani? (b) Kodi mzindawo sukuimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tikutero?

5 Werengani Ezekieli 48:15. Kodi “mzinda” ndi malo ozungulira ankaimira chiyani? (Ezek. 48:16-18) M’masomphenya, Yehova anali atauza Ezekieli kuti: “Malo a mzinda . . . adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli.” (Ezek. 45:6, 7) Zimenezi zikutanthauza kuti mzindawo komanso malo onse ozungulira sanali mbali ya “chopereka chopatulika” lomwe linali ‘gawo loti liperekedwe kwa Yehova.’ (Ezek. 48:9) Pamene tikukambirana za kusiyana kumeneku, tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira masiku ano pa dongosolo la mzindali.

6 Kuti tidziwe zimene tikuphunzira pa mzindawu, choyamba tikufunika tidziwe kuti mzinda umenewu sukuimira chiyani. Sukuimira mzinda wa Yerusalemu umene unamangidwanso komanso kachisi wake. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti m’kati mwa mzinda umene Ezekieli anaona m’masomphenya munalibe kachisi. Komanso mzindawu sukuimira mzinda wina uliwonse m’dziko lobwezeretsedwa la Isiraeli. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Ayuda amene anabwerera kwawo komanso mbadwa zawo sanamange mzinda wokhala ndi zinthu zimene zafotokozedwa m’masomphenyawo. Kuwonjezera pamenepo, mzindawu sukuimira mzinda wakumwamba. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mzindawo unamangidwa pamalo amene anasankhidwa kuti akhale “malo wamba” [kapena kuti malo omwe si opatulika]. Zimenezi ndi zosiyana ndi nyumba zimene zinamangidwa pamalo amene anasankhidwa kuti agwiritsidwe ntchito pa kulambira koyera.​—Ezek. 42:20.

7. Kodi mzinda umene Ezekieli anaona m’masomphenya ndi uti, nanga zikuoneka kuti ukuimira chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)

7 Ndiye kodi mzinda umene Ezekieli anaona unali uti? Kumbukirani kuti iye anaona mzindawu m’masomphenya omwewo amene anaonanso dzikolo. (Ezek. 40:2; 45:1, 6) Mawu a Mulungu akusonyeza kuti dzikolo ndi dziko lophiphiritsa, choncho mzindawo uyenera kuti ukuimiranso mzinda wophiphiritsa. Ndiye tinganene kuti mawu akuti “mzinda” akutanthauza chiyani? Mawuwa akupereka chithunzi cha anthu amene akukhala monga gulu limodzi ndipo gulu lawo ndi logwirizana. Choncho mzinda womangidwa mwadongosolo umene Ezekieli anaona, umene kukula kwake unali wofanana mbali zonse, zikuoneka kuti ukuimira mzinda umene umachita zinthu mwadongosolo.

8. Kodi oyang’anira a mzinda umene umachita zinthu mwadongosolo ntchito yawo amagwirira kuti, nanga n’chifukwa chiyani?

8 Kodi oyang’anira amene amachita zinthu mwadongosolowa ntchito yawo amagwirira kuti? Masomphenya a Ezekieliwa akusonyeza kuti mzindawu uli m’dziko lophiphiritsa. Choncho zimenezi zikusonyeza kuti oyang’anirawa amatsogolera zochita za anthu a Mulungu. Kodi mfundo yoti mzindawu uli pamalo wamba kapena kuti malo omwe si opatulika ikutanthauza chiyani? Ikutikumbutsa kuti ulamulirowo sukuimira mzinda wakumwamba koma wa padziko lapansi umene wakhala ukuthandiza anthu onse amene ali m’paradaiso wauzimu.

9. (a) Kodi oyang’anira amenewa padziko lapansi pano ndi ndani? (b) Kodi Yesu adzachita chiyani mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000?

9 Kodi oyang’anira amenewa ndi ndani? M’masomphenya a Ezekieli, amene akutsogolera mzindawo akutchedwa “mtsogoleri.” (Ezek. 45:7) Iye anali woyang’anira pakati pa anthuwo koma sanali wansembe kapena wa fuko la Levi. Mtsogoleri ameneyu akutipangitsa kuganizira kwambiri za oyang’anira mumpingo masiku ano amene si odzozedwa ndi mzimu. Abusa achikondi amenewa omwe ali m’gulu la “nkhosa zina,” ndi atumiki odzichepetsa a boma lakumwamba lomwe wolamulira wake ndi Khristu. (Yoh. 10:16) Mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000, Yesu adzasankha komanso kuika akulu oyenerera kapena kuti “akalonga padziko lonse lapansi.” (Sal. 45:16) Ufumu wakumwamba udzathandiza akulu amenewa kuti azipereka zinthu zofunika kwa anthu a Mulungu mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu.

“Yehova Ali Kumeneko”

10. Kodi dzina la mzindawo ndi chiyani, nanga zimenezi zikutitsimikizira chiyani?

10 Werengani Ezekieli 48:35. Dzina la mzindawo ndi lakuti “Yehova Ali Kumeneko.” Dzina limeneli linkatsimikizira anthu okhala mumzindawo kuti Yehova adzakhala nawo. Posonyeza Ezekieli mzinda umenewo, umene unali pakati pa dzikolo, zinali ngati Yehova akuuza Ayuda amene anali ku ukapolo kuti: ‘Ndidzakhalanso nanu.’ Zimenezitu zinali zolimbikitsa kwambiri.

11. Kodi tikuphunzira chiyani m’masomphenya a Ezekieli okhudza mzinda ndi dzina lake losangalatsa?

11 Kodi tikuphunzira chiyani pa mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli? Dzina la mzinda umenewu, womwe ukuimira ulamuliro, likutsimikizira atumiki a Mulungu masiku ano kuti panopa Yehova amakhala ndi atumiki ake okhulupirika padziko lapansi ndipo adzakhala nawo mpaka kalekale. Dzina lapaderali likutsindikanso mfundo yofunika ya choonadi yakuti: Sikuti mzindawu ulipo kuti upereke mphamvu kwa munthu aliyense koma kuti uthandize anthu kutsatira njira za Yehova zomwe ndi zachikondi komanso zosavuta kutsatira. Mwachitsanzo, Yehova sanapereke udindo kwa oyang’anirawo kuti agawe dzikolo mmene anthu akufunira, titero kunena kwake. M’malomwake, Yehova amayembekezera kuti oyang’anirawo azilemekeza gawo kapena utumiki uliwonse umene iyeyo wapereka kwa atumiki ake kuphatikizapo ‘onyozeka.’​—Miy. 19:17; Ezek. 46:18; 48:29.

12. (a) Kodi chochititsa chidwi ndi chiyani ndi mzinda umenewu, nanga kodi zimenezi zikuimira chiyani? (b) Kodi mbali imeneyi ya masomphenya ikukumbutsa oyang’anira a Chikhristu mfundo yofunika iti?

12 Kodi ndi chinthu china chiti chochititsa chidwi ndi mzinda wodziwika ndi dzina lakuti “Yehova ali Kumeneko”? Mizinda yakale inali ndi mipanda yachitetezo komanso mageti ochepa, koma mzinda uwu uli ndi mageti 12. (Ezek. 48:30-34) Kuchuluka kwa magetiwa (omwe analipo atatu mbali iliyonse ya mzindawo) kukusonyeza kuti oyang’anirawo anali osavuta kuwafikira ndipo mtumiki aliyense wa Mulungu akanatha kuwapeza mosavuta. Kuwonjezera pamenepo, mfundo yakuti mzindawo unali ndi mageti 12 ikusonyeza kuti “anthu a nyumba yonse ya Isiraeli” akanatha kulowa mumzindawo mosavuta. (Ezek. 45:6) Mfundo yoti zinali zosavuta kuti aliyense alowe mumzindawo ikukumbutsa oyang’anira a Chikhristu mfundo yofunika kwambiri. Yehova akufuna kuti anthu azikhala omasuka kufika kwa oyang’anira komanso kuti azipezeka mosavuta kwa onse amene akukhala m’paradaiso wauzimu.

Oyang’anira a Chikhristu amakhala osavuta kuwafikira ndipo amapezeka mosavuta (Onani ndime 12)

Anthu a Mulungu “Alowa Kudzalambira” Ndipo “Akugwira Ntchito Mumzinda”

13. Kodi Yehova anati chiyani za mautumiki osiyanasiyana amene anthu azidzachita?

13 Tiyeni tibwerere m’nthawi ya Ezekieli ndipo tione mfundo zina zimene akufotokoza m’masomphenya ochititsa chidwiwa zokhudza kugawa dziko. Yehova akutchula anthu amene akuchita mautumiki osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ansembe omwe ndi “atumiki apamalo opatulika,” ankayenera kupereka nsembe komanso kuyandikira kwa Yehova n’kumamutumikira. Alevi omwe anali “atumiki apakachisi,” ankayenera kuchita “utumiki wapakachisi ndi zinthu zonse zimene zikuyenera kuchitika mʼkachisimo.” (Ezek. 44:14-16; 45:4, 5) Kuwonjezera pamenepo, antchito ankagwira ntchito zosiyanasiyana pafupi ndi mzindawo. Kodi antchito amenewa ndi ndani?

14. Kodi anthu ogwira ntchito pafupi ndi mzinda akutikumbutsa chiyani?

14 Anthu ogwira ntchito pafupi ndi mzinda ankachokera “mʼmafuko onse a Isiraeli.” Iwo ankagwira ntchito zosiyanasiyana mumzindawo. Ntchito yawo inali yolima mbewu kuti “zizikhala chakudya cha amene akugwira ntchito mumzindawo.” (Ezek. 48:18, 19) Kodi zimenezi zikutikumbutsa mwayi umene tili nawo masiku ano? Inde. Masiku ano onse amene ali m’paradaiso wauzimu ali ndi mwayi wothandiza ntchito za abale ake a Khristu, omwe ndi odzozedwa, komanso ntchito za a “khamu lalikulu” amene Yehova wawapatsa udindo wotsogolera. (Chiv. 7:9, 10) Njira yaikulu imene timawathandizira ndi kumvera ndi mtima wonse malangizo ochokera kwa kapolo wokhulupirika.

15, 16. (a) Kodi m’masomphenya a Ezekieli tingapezemo mfundo zina ziti zofunika? (b) Kodi tili ndi mwayi uti wogwira nawo ntchito yofanana ndi imeneyi?

15 Masomphenya a Ezekieliwa ali ndi mfundo inanso imene ikutiphunzitsa chinthu chofunika kwambiri chokhudza utumiki wathu. Kodi mfundo yake ndi yotani? Yehova ananena kuti anthu ochokera m’mafuko 12 amene si Alevi adzakhala akugwira ntchito m’malo awiri: m’bwalo la kachisi komanso m’malo odyetsera ziweto amumzindawo. Kodi ntchito yawo ndi yotani m’malo onsewo? Mafuko onse ‘amalowa [m’bwalo la kachisi] kudzalambira’ popereka nsembe kwa Yehova. (Ezek. 46:9, 24) Anthu ochokera m’mafuko onse amabwera kudzathandiza pa ntchito zimene zikuchitika mumzindawo pogwira ntchito yolima m’malo amumzindawo. Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amene akugwira ntchito zimenezi?

16 Masiku ano a khamu lalikulu ali ndi mwayi wogwira ntchito zofanana ndi zimene zikuchitika m’masomphenya a Ezekieliwa. Iwo amalambira Yehova “mʼkachisi wake,” popereka nsembe zotamanda. (Chiv. 7:9-15) Iwo amachita zimenezi pogwira nawo ntchito yolalikira komanso posonyeza chikhulupiriro chawo mwa kupereka ndemanga pamisonkhano ya Chikhristu. Iwo amaona kuti chofunika kwambiri kwa iwo ndi kutumikira Yehova mwa njira imeneyi. (1 Mbiri 16:29) Kuwonjezera pamenepo, anthu ambiri a Mulungu amathandiza gulu la Mulungu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amathandiza pa ntchito zomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu komanso maofesi a nthambi ndiponso amathandiza nawo ntchito zina zambiri zimene gulu la Yehova likuchita. Ena amathandiza pa ntchito zimenezi popereka ndalama. Iwo amagwira ntchito imeneyi, yomwe tinganene kuti ili ngati ntchito yolima, kuti abweretse “ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) Iwo amagwira ntchito mwakhama komanso mosangalala chifukwa akudziwa kuti Yehova “amasangalala ndi nsembe zoterozo.” (Aheb. 13:16) Kodi mukugwira nawo mokwanira ntchito zimenezi?

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Ezekieli anafotokoza zokhudza ntchito zosiyanasiyana zimene zinkachitika mkati ndi kunja kwa mzinda? (Onani ndime 14-16)

“Pali Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano Zimene Ife Tikuyembekezera”

17. (a) Kodi m’tsogolo tidzaona kukwaniritsidwa kwakukulu kuti kwa masomphenya a Ezekieli? (b) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, kodi ndi ndani amene adzapindule ndi oyang’anira amene ali ngati mzinda?

17 Kodi m’tsogolo tidzaona kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenya a Ezekieli a chopereka? Inde. Ganizirani mfundo iyi: Ezekieli anaona kuti gawo la dzikolo limene linapatsidwa dzina lakuti “chopereka chopatulika,” linali pakati pa dzikolo. (Ezek. 48:10) Mofanana ndi zimenezi, pambuyo pa Aramagedo Yehova adzakhala nafe kulikonse kumene tingakhale. (Chiv. 21:3) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, oyang’anira amene ali ngati mzinda, amene apatsidwa udindo wosamalira anthu a Mulungu padziko lapansi, adzathandiza kuti madalitso a ufumuwa afike padziko lonse lapansi. Iwo adzachita zimenezi popereka malangizo achikondi kwa onse amene adzapange “dziko lapansi latsopano,” omwe ndi anthu okhala padziko lapansi amene Mulungu azidzasangalala nawo.​—2 Pet. 3:13.

18. (a) N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti oyang’anira amene ali ngati mzinda azidzachita zinthu mogwirizana ndi ulamuliro wa Mulungu? (b) Kodi dzina la mzindawo likutitsimikizira mfundo yofunika iti?

18 N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti oyang’anira amene ali ngati mzinda adzachita zinthu mogwirizana ndi ulamuliro wa Mulungu? Chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amanena momveka bwino kuti mzinda wapadziko lapansi, womwe uli ndi mageti 12, ukusonyeza mmene mzinda wakumwamba wokhala ndi mageti 12, womwe ndi Yerusalemu Watsopano ulili. Mzinda umenewu wapangidwa ndi anthu 144,000 amene adzalamulire limodzi ndi Khristu. (Chiv. 21:2, 12, 21-27) Zimenezi zikusonyeza kuti oyang’anira apadziko lapansi azidzatsatira ndi kuchita zimene Ufumu wa Mulungu kumwamba wasankha. Inde, dzina la mzinda lakuti “Yehova ali Kumeneko” likutsimikizira aliyense wa ife kuti kulambira koyera kudzapitiriza mpaka kalekale m’Paradaiso. M’tsogolomutu muli zabwino kwambiri.