Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 1B

Mfundo Zachidule za M’buku la Ezekieli

Mfundo Zachidule za M’buku la Ezekieli

Mwachidule tingati buku la Ezekieli linagawidwa motere:

CHAPUTALA 1 MPAKA 3

Mu 613 B.C.E., pamene anali ku ukapolo ku Babulo limodzi ndi a Yuda ena, Ezekieli anaona masomphenya a Yehova ndipo anapatsidwa utumiki woti anenere kwa Ayuda amene ankakhala pafupi ndi mtsinje wa Kebara.

CHAPUTALA 4 MPAKA 24

Pakati pa 613 ndi 609 B.C.E., Ezekieli anapereka mauthenga a ulosi amene mbali yaikulu ankanena za chiweruzo cha Yerusalemu ndi anthu ake opanduka amenenso ankalambira mafano.

CHAPUTALA 25 MPAKA 32

Kuyambira mu 609 B.C.E., chaka chimene a Babulo anayamba kuzungulira mzinda wa Yerusalemu komaliza, Ezekieli anasiya kupereka uthenga wachiweruzo wokhudza mzinda wa Yerusalemu n’kuyamba kupereka uthenga wachiweruzo kwa adani awo amene anazungulira Yerusalemu. Adaniwo anali anthu a ku Amoni, Edomu, Iguputo, Mowabu, Filisitiya, Sidoni ndi Turo.

CHAPUTALA 33 MPAKA 48

Kuyambira mu 606 B.C.E., Yerusalemu komanso kachisi wake yemwe anali kutali, atawonongedwa, Ezekieli anayamba kupereka uthenga wosangalatsa wakuti kulambira Yehova Mulungu koyera kudzabwezeretsedwa.

Choncho tingati buku la Ezekieli linalembedwa potengera nthawi imene zinthu zinachitikira komanso mitu ya nkhani. Maulosi okhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu komanso kachisi wake ananenedwa koyambirira, maulosi ambiri okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera asananenedwe. Zimenezi n’zomveka chifukwa maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera akusonyeza kuti anthu anali atasiya kulambira pakachisi.

Komanso maulosi a Ezekieli okhudza kuwonongedwa kwa mitundu yozungulira imene inkadana ndi Ayuda (Chaputala 25 mpaka 32) anaikidwa pakati pa mauthenga ake achiweruzo okhudza Yerusalemu ndi maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. Poikira ndemanga pa mauthenga a chiweruzo a Ezekieli opita ku mitundu yosiyanasiyana, katswiri wina ananena kuti: “Mauthengawo amasonyeza mmene anasinthira kuchoka pa kulengeza zokhudza mkwiyo wa Mulungu, n’kuyamba kulengeza uthenga wokhudza mmene adzasonyezere chifundo kwa anthu ake, chifukwa chilango chimene Mulungu adzapereke kwa adani ake ndi mbali ya kupulumutsidwa kwa anthu ake.”

Bwererani ku mutu 1, ndime 18