Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 2A

Kumvetsa Maulosi a Ezekieli

Kumvetsa Maulosi a Ezekieli

TANTHAUZO​—KODI ULOSI N’CHIYANI?

M’Baibulo mawu a Chiheberi akuti na·vaʼʹ, amene anawamasulira kuti “ulosi,” kwenikweni amatanthauza kuphunzitsa makhalidwe abwino, kupereka uthenga wouziridwa, chiweruzo kapena malamulo ochokera kwa Mulungu. Angatanthauzenso kupereka uthenga wochokera kwa Mulungu, wa zinthu zimene zichitike m’tsogolo. M’maulosi a Ezekieli muli mauthenga a mitundu yonseyi.​—Ezek. 3:10, 11; 11:4-8; 14:6, 7; 37:9, 10; 38:1-4.

MMENE ANKAPEREKERA UTHENGAWO

  • MASOMPHENYA

  • MAFANIZO

  • KUYEREKEZERA

M’buku la Ezekieli muli masomphenya, mafanizo, miyambi komanso zinthu zongoyerekezera zomwe zili ndi uthenga waulosi.

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

Nthawi zina maulosi amene Ezekieli ananena amakwaniritsidwa m’njira zingapo. Mwachitsanzo, mbali yaing’ono ya maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera, inakwaniritsidwa pamene anthu a Mulungu anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa. Koma mogwirizana ndi zimene zafotokozedwa m’mutu 9 wa buku lino, maulosi ambiri okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera akukwaniritsidwa masiku ano ndipo adzakwaniritsidwanso m’tsogolo.

M’mbuyomu, tinkaona kuti zinthu zina zimene zinatchulidwa m’maulosi a Ezekieli zinkaimira zinthu zinazake. Koma bukuli silinafotokoze kuti munthu, chinthu, malo kapena chochitika chinachake ndi chaulosi ndipo chikuimira chinachake masiku ano pokhapokha ngati pali zifukwa za m’Malemba zonenera zimenezo. a M’malomwake, likufotokoza mmene maulosi ambiri a Ezekieli adzakwaniritsidwire m’njira yaikulu. Likufotokozanso zimene tikuphunzira kuchokera m’mauthenga a Ezekieli komanso kwa anthu, malo ndi zochitika zina zimene iye anatchula.

a Kuti muone nkhani yofotokoza kuti zinthu zina zinkaimira zinazake, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015, tsa. 9-11, ndime 7-12; komanso “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” tsa. 17-18 m’magazini yomweyi.