BOKOSI 6A
“Umete Tsitsi Lako Ndi Ndevu Zako”
Zimene Ezekieli anachita zinasonyeza zinthu zomwe zinali zitatsala pang’ono kuchitika mu Yerusalemu
-
“Umete”
Ayuda adzaukiridwa ndipo adzawonongedwa
-
‘Uyeze Tsitsi, Ukatero Uligawe’
Chiweruzocho adzachita kuchikonzekera ndipo adzachipereka mwadongosolo
-
‘Uliwotche’
Anthu ena adzafera mumzindawo
-
“Nʼkumalimenya”
Anthu ena adzaphedwa kunja kwa mzindawo
-
‘Uliuluze’
Anthu ena adzathawa koma sadzapeza mtendere
-
“Nʼkulikulunga”
Anthu ena amene anali ku ukapolo adzabwerera ku Yerusalemu ndipo adzateteza kulambira koyera