Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 7A

Mitundu Imene Inazungulira Yerusalemu

cha m’ma 650-300 B.C.E.

Mitundu Imene Inazungulira Yerusalemu

TCHATI CHOSONYEZA NTHAWI (ZAKA ZONSE NDI ZA MU B.C.E.)

  1. 620: Ababulo anayamba kulamulira Yerusalemu

    Nebukadinezara anachititsa kuti mfumu ya ku Yerusalemu ikhale pansi pa ulamuliro wake

  2. 617: Ababulo anatenga gulu loyamba la akapolo kuchokera ku Yerusalemu

    Anatenga olamulira, asilikali amphamvu ndi amisiri n’kupita nawo ku Babulo

  3. 607: Ababulo anawononga Yerusalemu

    Mzindawo ndi kachisi wake zinawotchedwa

  4. Pambuyo pa 607: Mzinda wa Turo wakumtunda

    Nebukadinezara anaukira mzinda wa Turo kwa zaka 13. Iye anagonjetsa mzinda wa Turo wakumtunda koma mzinda wa Turo wapachilumba anausiya

  5. 602: Aamoni ndi Amowabu

    Nebukadinezara anaukira Aamoni ndi Amowabu

  6. 588: Ababulo anagonjetsa Aiguputo

    M’chaka cha 37 cha ulamuliro wake, Nebukadinezara anaukira Aiguputo

  7. 332: Mzinda wa Turo wapachilumba

    Gulu lankhondo la Agiriki limene ankalitsogolera ndi Alekizanda Wamkulu, linawononga mzinda wa Turo wapachilumba

  8. 332 kapena chakachi chisanafike: Filisitiya

    Alekizanda anagonjetsa mzinda wa Gaza umene unali likulu la Afilisiti

Malo amene ali pa Mapu

  • GIRISI

  • NYANJA YAIKULU

  • (NYANJA YA MEDITERRANEAN)

  • TURO

  • Sidoni

  • Turo

  • Samariya

  • Yerusalemu

  • Gaza

  • FILISITIYA

  • IGUPUTO

  • BABULO

  • AMONI

  • MOWABU

  • EDOMU