Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Msonkhano wosaiwalika umene unachitika m’chaka cha 1919, unapereka umboni woonekeratu wakuti anthu a Yehova anali atamasulidwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu.

BOKOSI 9B

N’chifukwa Chiyani Tikuti Chinali Chaka Cha 1919?

N’chifukwa Chiyani Tikuti Chinali Chaka Cha 1919?

N’chifukwa chiyani timanena kuti anthu a Yehova anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu mu 1919? Tikutero chifukwa cha zimene ulosi wa m’Baibulo umanena komanso zimene zachitika m’mbiri ya anthu.

Ulosi wa m’Baibulo komanso zimene mbiri imanena zimasonyeza kuti Yesu anayamba kulamulira monga mfumu kumwamba mu 1914. Chimenechi chinali chizindikiro cha kuyambika kwa masiku otsiriza a dziko la Satanali. Kodi Yesu anachita chiyani atakhala Mfumu? Kodi nthawi yomweyo anamasula atumiki ake apadziko lapansi ku ukapolo wa Babulo Wamkulu? Kodi anasankha “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” n’kuyamba ntchito yokolola?​—Mat. 24:45.

N’zodziwikiratu kuti sanachite zimenezo. Kumbukirani kuti mtumwi Petulo anauziridwa kuti alembe kuti ‘chiweruzo chidzayambira panyumba ya Mulungu.’ (1 Pet. 4:17) Mofanana ndi zimenezi, mneneri Malaki analosera kuti nthawi ina Yehova adzabwera kunyumba yake yolambirira limodzi ndi “mthenga wa pangano” amene ndi mwana wa Mulungu. (Mal. 3:1-5) Imeneyo idzakhala nthawi yoyenga komanso yamayesero. Kodi zimene zinachitika zikugwirizana ndi zimene ulosiwu unanena?

Inde zikugwirizana. Chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa 1919 inali nthawi yovuta yamayesero komanso yoyengedwa kwa Ophunzira Baibulo, lomwe ndi dzina limene a Mboni za Yehova ankadziwika nalo pa nthawiyo. Mu 1914 anthu ambiri a Mulungu anakhumudwa chifukwa chakuti mapeto sanafike ngati mmene ankaganizira. Anthu anakhumudwanso kwambiri mu 1916 pambuyo pa imfa ya Charles T. Russell amene ankatsogolera anthu a Mulungu. Anthu amene ankakonda kwambiri M’bale Russell, ankatsutsa kwambiri zochita za M’bale Joseph F. Rutherford amene analowa m’malo mwa Russell potsogolera anthu a Mulungu. Anthu anagawanika ndipo zimenezi zinangotsala pang’ono kugawanitsa gulu la Yehova mu 1917. Kenako mu 1918, M’bale Rutherford limodzi ndi anzake ena 7 anaimbidwa milandu yabodza n’kutsekeredwa m’ndende ndipo zikuoneka kuti amene anachititsa zimenezi ndi atsogoleri achipembedzo. Likulu lathu ku Brooklyn linatsekedwa. N’zoonekeratu kuti anthu a Mulungu anali asanamasulidwe ku ukapolo wa Babulo Wamkulu.

Koma kodi chinachitika n’chiyani mu 1919? Zinthu zinasintha mofulumira kwambiri. Kumayambiriro kwa chakacho M’bale Rutherford ndi anzake aja anatulutsidwa m’ndende. Ndipo nthawi yomweyo anayambiranso kugwira ntchito yawo. Mofulumira kwambiri anayamba kukonzekera msonkhano wachigawo komanso anayamba kusindikiza magazini yatsopano yomwe inkadziwika kuti The Golden Age, (koma panopa imadziwika kuti Galamukani!) Magazini yatsopanoyi inakonzedwa n’cholinga choti izigwiritsidwa ntchito mu utumiki. Kuwonjezera pamenepo mumpingo uliwonse munasankhidwa otsogolera kuti azilimbikitsa anthu komanso kutsogolera ntchito yolalikira. M’chaka chomwecho kabuku kamene kankatchedwa kuti Bulletin (komwe panopa kamadziwika kuti kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu) kanatulutsidwa n’cholinga choti kazithandiza pa ntchito yolalikira.

Kodi chinachitika n’chiyani? N’zoonekeratu kuti Khristu anali atamasula anthu ake mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. Iye anali atasankha kapolo wokhulupirika komanso wanzeru. Pa nthawiyi ntchito yokolola inali itayamba. Kungoyambira m’chaka chimenecho cha 1919, ntchitoyi yapita patsogolo kwambiri.