Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 10B

“Mafupa Ouma” Komanso ‘Mboni Ziwiri’​—Kodi Zikugwirizana Bwanji?

“Mafupa Ouma” Komanso ‘Mboni Ziwiri’​—Kodi Zikugwirizana Bwanji?

MAULOSI awiri ofanana anakwaniritsidwa m’chaka cha 1919. Ulosi woyamba ndi wokhudza “mafupa ouma” ndipo ulosi wina ndi wokhudza ‘mboni ziwiri.’ Masomphenya a “mafupa ouma” akulosera za nthawi yaitali kwambiri imene inatenga zaka mahandiredi ambiri, ndipo inatha pamene gulu lalikulu la anthu a Mulungu linakhalanso lamoyo. (Ezek. 37:2-4; Chiv. 11:1-3, 7-13) Ulosi wokhudza ‘mboni ziwiri’ ukufotokoza za nthawi yochepa kwambiri (imene inayamba kuyambira kumayambiriro kwa 1914 kukafika kumayambiriro kwa 1919) ndipo inatha pamene kagulu kochepa kwambiri ka anthu a Mulungu kanakhalanso kamoyo. Maulosi onsewa akunena za kuukitsidwa kophiphiritsira ndipo m’masiku athu ano anakwaniritsidwa mu 1919 pamene Yehova anachititsa kuti atumiki ake odzozedwa ‘aimirire’ n’kuchoka mu ukapolo wa Babulo Wamkulu ndipo anawasonkhanitsanso pamodzi n’kupanga mpingo.​—Ezek. 37:10.

Koma onani kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kukusiyana m’njira yapadera kwambiri. Ulosi wa “mafupa ouma” ukunena za kukhalanso ndi moyo kwa odzozedwa onse amene adakali ndi moyo padziko lapansi. Ulosi wonena za ‘mboni ziwiri’ ukunena za kukhalanso ndi moyo kwa odzozedwa ena amene pa nthawiyo anali adakali ndi moyo padziko lapansi. Odzozedwa amenewa ankatsogolera gulu la Mulungu ndipo anaikidwa kukhala kapolo “wokhulupirika komanso wanzeru.”​—Mat. 24:45; Chiv. 11:6. a

“M’chigwamo Munali Mafupa Okhaokha”​—Ezek. 37:1

  1. 100 C.E. ITADUTSA

    Kuyambira mu 100 C.E. pamene mpingo wa Akhristu odzozedwa unaphedwa mophiphiritsira, ‘m’chigwa munali mafupa okhaokha’

  2. KUMAYAMBIRIRO KWA 1919

    1919: “Mafupa ouma” anakhalanso ndi moyo pamene Yehova anachititsa kuti Akhristu onse odzozedwa achoke m’Babulo Wamkulu n’kusonkhanitsidwira mumpingo wobwezeretsedwa

‘Mboni Ziwiri’​—Chiv. 11:3

  1. KUMAPETO KWA 1914

    kulalikira atavala “ziguduli”

    1914: ‘Mboni ziwiri’ zinkalalikira zitavala “ziguduli” kwa zaka zitatu ndi hafu. Chakumapeto kwa zaka zimenezi, mbonizi zinaphedwa mophiphiritsira

  2. imfa yophiphiritsira

  3. KUMAYAMBIRIRO KWA 1919

    1919: ‘Mboni ziwiri’ zinakhala ndi moyo pamene kagulu kochepa ka abale odzozedwa amene ankatsogolera m’gulu la Yehova, kanasankhidwa kuti kakhale “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru”

a Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya March 2016.