Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 19A

Mitsinje ya Madalitso Ochokera kwa Yehova

Mitsinje ya Madalitso Ochokera kwa Yehova

Ganizirani mavesi ena a m’Baibulo amene amanena za “mtsinje” komanso “madzi” poimira madalitso ochokera kwa Yehova. Tikawerenga mavesi onsewa timapeza mfundo yolimbikitsa ya mmene Yehova akutidalitsira. Ndiye kodi mavesi amenewa amatithandiza bwanji?

YOWELI 3:18 Ulosi umenewu ukusonyeza kasupe akutuluka m’malo opatulika a kachisi. Kasupeyo akuthirira “chigwa cha Mitengo ya Mthethe” chomwe ndi chouma. Choncho onse, Yoweli ndi Ezekieli, anaona mtsinje ukubweretsa moyo pamalo ouma. M’zitsanzo zonsezi, mtsinje ukutuluka m’nyumba ya Yehova kapena kuti m’kachisi.

ZEKARIYA 14:8 Mneneri Zekariya anaona “madzi a moyo” akutuluka kuchokera mumzinda wa Yerusalemu. Hafu ya madziwo ankapita ku nyanja yakum’mawa kapena kuti Nyanja Yakufa, ndipo hafu inayo ankapita ku nyanja yakumadzulo kapena kuti nyanja ya Mediterranean. Yerusalemu unali “mzinda wa Mfumu yamphamvu,” Yehova Mulungu. (Mat. 5:35) Choncho pamene Zekariya anatchula mzinda umenewu, akutikumbutsa kuti m’tsogolomu Yehova adzalamulira dziko lonse lapansi. Kwa nthawi yaitali takhala tikukhulupirira kuti madzi a mu ulosi umenewu akutanthauza kuti Yehova adzadalitsa magulu awiri a anthu okhulupirika m’Paradaiso. Gulu loyamba ndi la anthu amene adzadutse pa chisautso chachikulu ali ndi moyo ndipo gulu lachiwiri ndi la anthu amene adzaukitsidwe.

CHIVUMBULUTSO 22:1, 2 Mtumwi Yohane anaona mtsinje wophiphiritsira wofanana ndi umene Ezekieli anaona. Koma mtsinje umenewu sunkachokera m’kachisi koma unkachokera kumpando wachifumu wa Yehova. Choncho mofanana ndi ulosi wa Zekariya, zikuoneka kuti ulosiwu ukutsindika za madalitso amene tidzalandire mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu.

N’zoona kuti pali kusiyana pang’ono pakati pa madalitso amene adzabwere kuchokera mu Ulamuliro wa Yehova ndi amene akuimiridwa ndi mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya. Koma madalitso amenewa akuchokera kwa Yehova ndipo akupita kwa anthu ake okhulupirika.

SALIMO 46:4 Onani mmene vesi limodzi lokhali likufotokozera nkhani ya kulambira komanso ulamuliro. Apa tikuona mtsinje umene ukubweretsa chimwemwe ‘mumzinda wa Mulungu,’ zomwe zikuimira Ufumu komanso ulamuliro. Mtsinjewu ukubweretsanso chimwemwe ku “chihema chachikulu chopatulika cha Wamʼmwambamwamba,” chomwe chikuimira kulambira koyera.

Mavesi onsewa akutitsimikizira kuti Yehova adzadalitsa anthu okhulupirika m’njira ziwiri. Tidzapindula kwamuyaya. Choyamba, tidzapindula ndi ulamuliro wake ndipo chachiwiri, tidzapindula ndi njira imene wakonza yokhudza kulambira koyera. Choncho tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuti tipitirize kufunafuna “madzi opatsa moyo,” kuchokera kwa Yehova Mulungu komanso kwa Mwana wake. Madzi amenewa akuimira zinthu zimene Mulungu akupereka mwachikondi, zotithandiza kudzapeza moyo wosatha.​—Yer. 2:13; Yoh. 4:10.