Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 21A

“The Contribution That You Are to Set Apart”

“The Contribution That You Are to Set Apart”

EZEKIELI 48:8

Tiyeni tiyendere limodzi ndi Ezekieli pamene akuonetsetsa malo amene Yehova anawapatula. Malo amenewa ali ndi mbali 5. Kodi mbali zake ndi ziti? Nanga ali ndi ntchito yotani?

“Chopereka”

Malo amenewa anali oti azigwiritsidwa ntchito ndi oyang’anira ndipo akudziwikanso kuti “chopereka chopatulika.”

EZEK. 48:8

“Malo Onse Oti Aperekedwe”

Malo amenewa anaikidwa padera kuti akhale a ansembe, Alevi komanso a mzinda. Anthu onse ochokera m’mafuko onse 12 ankalowa m’malo amenewa kudzalambira Yehova komanso kudzathandiza pa ntchito zosiyanasiyana.

EZEK. 48:20

“Malo a Mtsogoleri”

“Malo amenewa adzakhale cholowa cha mtsogoleriyo mu Isiraeli.” “Akhale a mtsogoleri wa anthu.”

EZEK. 45:7, 8; 48:21, 22

“Chopereka Chopatulika”

Malo amenewa akutchulidwanso kuti “gawo loyera.” Mbali ya kumtunda inali ya “Alevi.” Anali “malo opatulika.” Mbali yapakati inali “chopereka chopatulika cha ansembe.” Anali “oti adzamangepo nyumba zawo komanso adzakhala malo opatulika omangapo kachisi.”

EZEK. 45:1-5; 48:9-14

“Malo Otsala”

“Malo amenewa adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli” ndipo adzakhala “malo a mzinda oti munthu aliyense angagwiritse ntchito. Malo amenewa akhale oti anthu azimangako nyumba komanso kudyetserako ziweto.”

EZEK. 45:6; 48:15-19