Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

‘Muyenela kukhala aphunzitsi.’ (Aheb. 5:12) Tangoganizani! Yehova—Mphunzitsi wopambana onse kumwamba na pa dziko lapansi, akutipatsa mwayi wophunzitsako ena za iye! Nchito iliyonse yophunzitsa coonadi ponena za Yehova—kaya ni m’banja, mu mpingo, kapena mu ulaliki—ni mwayi wosaneneka, komanso udindo waukulu. Koma kodi tingaukwanitse bwanji?

Yankho lake ili m’mawu amene mtumwi Paulo analembela Timoteyo kuti: “Pitiliza kukhala wodzipeleka poŵelenga pamaso pa anthu, powadandaulila, ndi powaphunzitsa.” Anatinso: “Cifukwa ukatelo udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvela.” (1 Tim. 4:13, 16) Muli na uthenga wopatsa moyo. Conco, tifunika kukulitsa luso lathu la kuŵelenga na kuphunzitsa. Colinga ca kabuku kano ni kukuthandizani kucita zimenezi. Onani zina zimene zilimo.

Pa peji iliyonse pali lemba logwilizana na mfundo yophunzila, kapena na citsanzo ca mfundo yophunzila.

Yehova ndiye “Mlangizi Wamkulu.” (Yes. 30:20) N’zoona kuti kabuku kano kadzakuthandizani kunola maluso anu a kuŵelenga na kuphunzitsa. Ngakhale n’conco, osaiŵala kuti Yehova ndiye Gwelo la uthenga wathu, ndipo ndiye amakoka anthu. (Yoh. 6:44) Conco, pemphelelani mzimu woyela kaŵili-kaŵili. Muzikonda kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu. Chukitsani Yehova kwa omvela anu, osati inu mwini. Athandizeni kum’konda kwambili.

Mwapatsidwa mwayi wolalikila za uthenga wofunika kwa anthu kuposa wina uliwonse. Ndipo tili na cidalilo kuti ngati “mudalila mphamvu imene Mulungu amapeleka,” mudzakwanitsa.—1 Pet. 4:11.

Ise aphunzitsi anzanu,

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova